Saturday, January 20, 2024

LAMULUNGU LACHITATU PA CHAKA – B

LAMULUNGU LACHITATU PA CHAKA – B

Yesu akuti: “Siyani zonse, ndipo munditsate!”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MNENERI YONA: YONA 03: 01 – 05, 10 (Anthu aku Ninive adasiya makhalidwe ao oipa).

 

Chauta adalankhula ndi Yona kachiwiri, namuuza kuti, “Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukulu uja, ukaulalikire uthenga umene ndikukuuza.” Yona adanyamuka, napita ku Niniveko, potsata mau a Chauta. Mzindawo unali waukulu kwambiri, wofunika masiku atatu kuudutsa. Yona adalowa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!” Anthu a ku Ninive adakhulupirira Mulungu. Adalengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamng’ono yemwe, asale zakudya, ndipo avale chiguduli. Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m’mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osawapatsa chilango chimene adaati adzawapatsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 25: 04 – 09.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta,

Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu,

Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza,

Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

 

Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika,

Chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale,

Koma mundikomere mtima, Inu Chauta,

Chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

 

Chauta ndi wabwino ndi wolungama,

Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake,

Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,

Amawaphunzitsa njira zake.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 07: 29 – 31. (Dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita).

 

Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthawi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire. Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo. Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisawagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopano, likupita.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 01: 15.

Alleluia, Alleluia – Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupilira Uthenga Wabwino. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO  01: 14 – 20. (Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu).

 

Yohane uja ataponyedwa m’ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu. Ankati, “Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.” Pamene Yesu ankayenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu awiri, Simoni ndi m’bale wake Andrea, akuponya khoka m’nyanjamo, popeza kuti anali asodzi. Yesu adawauza kuti, “inu, munditsate, ndikakusandutsani asodzi a anthu.”  Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pang’ono, Yesu adaona Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwowo anali m’chombo, akukonza makoka ao, nthawi yomweyo Iye adawaitana. Pamenepo iwowo adasiya bambo wao Zebedeo m’chombomo pamodzi ndi antchito ake, namatsata Yesu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pozindikira kufooka kwathu ndiponso umphawi wa anthu, tiyeni tipemphe Atate a Kumwamba kuti atithandize kulapa ndi kukhulupirira Mthenga Wabwino:

 

1.     Ansembe onse atsogolere anthu ao pa njira ya ungwiro, powaphunzitsa za kulapa, azitsata Yesu Khristu ndi mtima wosagawika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu okhala mumdima, osadziwa Mthenga Wabwino, atsekulire Mulungu mitima yao pomufunafuna Iyeyo ndi kuchita zolungama.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao ndi kukhulupirira Mthenga Wabwino, ndipo asonyeze kulapa kwao pakutenga makhalidwe okomera Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe, tisaleke kuwongola maganizo athu ndi mayendedwe athu, pomagwiritsa ntchito mau a Mulungu, kuti ifenso tisanduke asodzi a anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate okoma mtima, landirani mapemphero athuwa, ndipo mukhazikitse ufumu wanu wachikondi m’mitima mwathu ndi mwa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...