LAMULUNGU LACHIWIRI PA CHAKA - B
“Adakapeza m’bale wake, napita naye kwa Yesu.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LOYAMBA LA SAMUELE: 01 SAMUELE 03: 03 – 10, 19. (Yankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva).
Samuele anali gone m’Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthawiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime. Tsono Chauta adaitana kuti, “Samuele!” Iye adayankha kuti, “wawa!” Adathamangira kwa Eli nati, “Ndabwera, ndamva kuitana.” Koma Eli adati, “sindidakuitane, kagone.” Motero Samuele adapita kukagona. Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva Ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “sindidakuitane mwana wanga, kagone.” Pamenepo nkuti Samuele asanadziwe Chauta, ndipo mau a Chauta nkuti asanaululidwe kwa iyeyo. Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nanena kuti, “Ndabwera mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo. Tsono adauza Samuele kuti, “pita, kagone. Akakuitananso, ukanene kuti, Lankhulani, Inu Chauta, poti mtumiki wanune ndili kumva.” Choncho Samuele adapita kukagona kumalo kwake. Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthawi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.” Monse Samuele ankakula, Chauta anali naye, motero zonse zimene Samueleyo ankanena zinkachitikadi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 40: 02, 04, 07 – 10.
Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.
Ine ndidayembekeza Chauta kuti adzandithandize,
Adaweramira pansi nkuyang’ana kwa ine, namva kulira kwanga,
Mulungu waika nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,
Nyimbo yake yotamanda Iye.
Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.
Simudafune nsembe ndi zopereka,
Koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera,
Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo,
Tsono ndidati, Ndilipo, ndikubwera.
Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.
Monga zidalembedwa za ine m’buku la malamulo,
Ndimakonda kuchita zimene mumafuna,
Inu Mulungu wanga,
Malamulo anu ali mumtima mwanga.
Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.
Ndalalika Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu,
Pa msonkhano waukulu,
Sindidatseke pakamwa,
Monga Mukudziwa, Inu Chauta.
Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 06: 13 – 15, 17 – 20. (Kodi inu simudziwa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu?)
Abale, thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo. Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso. Kodi inu simudziwa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Monga Tsono ine nkutenga ziwalo za Khristu nkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Chosatheka. Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala Mzimu umodzi. Thawani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, Tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 01: 41, 17b.
Alleluia, Alleluia – Tampeza Mesiya – ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Kudzera mwa Iye, Mulungu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 01: 35 – 42. (Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye Tsiku limenelo).
M’mawa mwakenso Yohane anali pamalo pomwepo pamodzi ndi ophunzira ake ena awiri. Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.” Ophunzira awiri aja atamva mauwo, adatsatira Yesu. Yesu adacheuka naona kuti akumtsatira, Tsono adawafunsa kuti, “kodi ulendowu?” Iwo adati, “timati tidziwe, kodi mumakhala kuti, Rabi?” (Tanthauzo la Rabi ndiye kuti, Mphunzitsi.) Yesu adati, “tiyeni mukakuwone.” Iwo adapita naye. Pamenepo nthawi inali ngati 4 koloko madzulo. Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye tsiku limenelo. M’modzi mwa awiri aja amene adaamva mau a Yohane natsatira Yesu, anali Andrea, m’bale wake wa Simoni Petro. Iye adayamba kukapeza m’bale wakeyo Simoni, namuuza kuti, “Tampeza Mesiya.” (Ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.) Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.)
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, ifenso tapezana ndi Ambuye lero ndipo tamva mau ao. Tsono tipemphe chithandizo chao malinga ndi zosowa zathu ndi za Mpingo wonse:
1. Atsogoleri a Mpingo alalike mau a Mulungu ndi chikhulupiriro cholimba; atsimikizire anthu onse kuti Mpulumutsi amakhala pakati pao.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu owe adakali padera osadziwa Mthenga Wabwino alimbikire kufunafuna Mulungu, amutsekulire Iye mitima yao kuti amve mau ake.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anyamata ndi atsikana okhulupirira Yesu Khristu aonetsane makhalidwe odziletsa ndi odzilemekeza pokumbukira kuti thupi lao ndi nyumba ya Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe amene tapeza Mpulumutsi, tiyesetse kukokera abale athu kwa Iyeyo kuti iwonso adzamve mau ake ndi kulandira chipulumutso chake.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukuyamikani chifukwa simuleka kuitana anthu mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment