Saturday, February 10, 2024

LAMULUNGU LA 06 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 06 PA CHAKA – B.

“Yesu adadzatichotsa khate la mumtima.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LEVITIKO: LEVITITKO 13: 01 – 02, 44 – 46. (Munthu akakhala ndi nthenda ya khate, akhale payekha kunja kwa mahema).

 

Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “munthu akakhala ndi chithupsa pathupi pake, kapena m’buko, kapena chikanga, ndipo mwina nkusanduka ngati nthenda ya khate pakhungu pakepo, munthuyo abwere naye kwa wansembe Aroni kapena kwa aliyense mwa ana ake amene ali ansembe. Ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Wansembe ayenera kumtchula kuti ndi woipitsidwa, ali ndi khate lakumutu. Munthu wakhate avale sanza, ndipo tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wam’mwamba, ndipo azifuula kuti, “ndine woipitsidwa, ndine woipitsidwa. Wodwalayo adzakhalabe woipitsidwa nthawi zonse pamene ali ndi nthendayo, ndipo akhale kunja kwa mahema.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 32: 01 – 02, 05, 11.

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

 

Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa,

Amene machimo ake afafanizidwa.

Ngwodala amene Chauta samawerengera mlandu wake,

Amene mumtima mwake mulibe zonyenga

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

 

Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu,

Sindidabise kuipa kwanga,

Ndidati, ‘ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,’

Pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

 

Sangalalani ndi kukondwa,

Inu nonse okonda Mulungu,

Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 10: 31 – 11:01. (Muzinditsanzira ine, monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu).

 

Abale, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu. Moyo wanu ukhale wosaphunthwitsa Ayuda, kapena anthu a mitundu ina, kapenanso Mpingo wa Mulungu. Muzichita monga momwe ndimachitira ine. Ndimayesa kukondweretsa anthu onse pa zonse. Sindifunafuna zokomera ineyo, koma ndimafunafuna zokomera anthu onse, kuti apulumuke. Muzinditsanzira ine monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 07: 16.

Alleluia, Alleluia – Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu. Mulungu wadzathandiza anthu ake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01: 40 – 45. (Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi).

 

Munthu wina wakhate adadza kwa Yesu. Adamugwadira nayamba kumdandaulira. Adati, “mutafuna, mungathe kundichiritsa.” Yesu adamumvera chifundo. Adatambalitsa dzanja nkumukhudza nati, “chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi. Tsono Yesu adamlamula kuti apite, namuuza mau amphamvu. Adati, “chenjera, usakambire wina aliyense zimenezo. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.” Koma munthuyo atachoka pamenepo, adayamba kumaulula zonse, ndi kufalitsa nkhani imeneyi, kotero kuti Yesu sadathenso kuwonekera poyera m’mudzi uliwonse. Nchifukwa chake ankakhala kwina, kumalo kosapitapita anthu, koma anthu ankabwerabe kwa Iye kuchokera uku ndi uku.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, monga wakhate uja, nafenso titembenukire kwa Ambuye ndi kuwadandaulira kuti,

Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa:

 

1.     Ansembe ndi atsogoleri a Mpingo awamvere chifundo anthu ochimwa ndi kuwalandira, pokhala nawo mtima womwe unali mwa Yesu Khristu.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

2.     Anthu akhate ndi ena onse ovutika azindikire kukoma mtima kwa Mulungu polandira chisamaliro kuchokera kwa anthu anzao.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

3.     Anthu amene mitima yao ikukangamira ku zoipa atsekule maso ao ndi kutembenukira kwa Mulungu pozindikira umphawi wao.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

4.     Ife amene adatiyeretsa kawirikawiri, tilimbikire kumtsira Iye ulemu ndi kukondweretsa anzathu pa zochitika zathu zonse.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

Atate, tikuyamika chifundo chanu, chifukwa muli wokonzeka kuchiritsa anthu onse amene akudandaulirani ndi mtima wolapa. Mwa Yesu Khristu Ambuye anthu. Amen.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...