Saturday, February 24, 2024

LAMULUNGU LA 02 MUNYENGO YA LENTI – B

                                     LAMULUNGU LA 02 MUNYENGO YA LENTI – B

                        “Uyu ndi Mwana wanga amene ndimamukonda, mumumvere Iye.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 22: 01 – 02, 09 – 13, 15 – 18. (Lonjezo la Abrahamu, Tate wachikhulupiriro).

 

Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee, Ambuye.” Mulungu adati, “tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.” Atafika ku malo amene adamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo. Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo. Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, “usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziwa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.” Abrahamu atayang’ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m’ziyangoyango. Adapita kukaigwira, anaphia ngati nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake uja. Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiwiri kuchokera Kumwamba, adati, “Chauta akunena kuti, ‘ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezo, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m’mbali mwa Nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 116: 10, 15 – 19.

 

Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.

 

Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati,

“Ndazunzika koopsa.”

Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta,

Ndi yamtengowapatali pamaso pake.

 

Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.

 

Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni,

Inu mwamasula maunyolo anga,

Ndidzapereka kwa inu nsembe yothokozera,

Ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.

 

Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.

 

Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta,

Pamaso pa anthu ake onse,

Ndidzadzipereka m’mabwalo a Nyumba ya Mulungu,

Mu mzinda wa Yerusalemu.

 

Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 08: 31b – 34. (Mulungu sadaumire ngakhale Mwana wakewake).

 

Abale, tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere? Ndani angawaimbe mlandu anthu amene Mulungu adawasankha? Mulungu mwini wake amawaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angawaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 17: 05.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 09: 02 – 10. (Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda).

 

Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro ndi Yakobe ndi Yohane, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasintha iwo akuwona. Zovala zake zidasanduka zowala ndi zoyera kuti mbee, kupambana m’mene mmisiri wina aliyense angayeretsere nsalu pansi pano. Nthawi yomweyo ophunzira aja adaona Eliya ndi Mose, akukambirana ndi Yesu. Petro adauza Yesu kuti, “aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Ankatero chifukwa chosowa chonena, pakuti iye ndi anzake aja anali atagwidwa ndi mantha aakulu. Tsono padafika mtambo, nuwaphimba, ndipo mumtambomo mudamveka mau akuti, “uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.” Mwadzidzidzi ophunzirawo poyang’anayang’ana, adangoona kuti palibenso wina amene anali nawo pamenepo, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phirilo, Yesu adawaletsa kuti zimene adaaonazo asauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. Iwo adasungadi chinsinsichi, koma ankafunsana okhaokha kuti, “kodi kuuka kwa akufa akunena Yesuku ndiye kuti chiyani?”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Yesu alikutipempherera pokhala ku dzanja lamanja la Mulungu, tikweze mitima yathu kumwamba ndi kupempha chithandizo cha Ambuye:

 

1.     Eklezia wa Mulungu akhale chizindikiro chosonyeza kuwala kwa Yesu Khristu kwa anthu a mafuko onse.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.

2.     Akhristu amene akuzunzika chifukwa cha Mthenga Wabwino alimbikire m’chikhulupiriro chao pophathana ndi Yesu Khristu.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.

3.     Apezeke anyamata ndi atsikana ambiri odzipereka ku ntchito ya Mulungu: asaope kupereka moyo wao ngati nsembe chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.

4.     Ife tomwe tidziwe kulingalira m’mitima mwathu za masautso a Yesu Khristu pa nthawi ino ya Lenti, kuti timange moyo wathu pa chikondi chake.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.

Atate, tikuyamika chifundo chanu, chifukwa simuleka kutipatsa zonse mwaulere, mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, February 17, 2024

LAMULUNGU LA 01 MUNYENGO YA LENTI – B

LAMULUNGU LA 01 MUNYENGO YA LENTI – B

“Tilape ndi kuyamba moyo watsopano.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 09: 08 – 15. (Tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu, ndi zamoyo zonse).

 

Mulungu adauza Nowa ndi ana ake kuti, “tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu, ndi zamoyo zonse, mbalame, zoweta, nyama zakuthengo, ndi zina zonse zimene zidatuluka nanu m’chombo. Chipanganocho ndi ichi: ‘ndikulonjeza kuti sindidzaononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Ndithu chigumula sichidzaononganso dziko lapansi.’ Ndipo Mulungu adati, nachi chizindikiro cha chipangano chamuyaya chimene ndikuchiika pakati pa Ine ndi inu ndi cholengedwa chilichonse chimene chili ndi inu. Ndikuika utawaleza m’mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi. Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga, ndipo pakuoneka utawaleza m’mitambomo, ndizidzakumbukira lonjezo langa limene ndidachita ndi inu ndi nyama zonse, kuti chigumula chisadzaonongenso zamoyo zonse.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 25: 04 – 09.

 

Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta,

Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu,

Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza,

Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga.

 

Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.

 

Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu,

Ndi chikondi chanu chosasinthika,

Mundikomere mtima, Inu Chauta,

Chifukwa cha chikondi chanu.

 

Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.

 

Chauta ndi wabwino ndi wolungama,

Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake,

Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,

Amawaphunzitsa njira zake.

 

Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 1 PETRO 03:18 – 22. (Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani).

 

Abale, Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m’malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo. Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m’ndende. Mizimuyi ndi ya anthu amene kale lija sadamvere pamene Mulungu adaadikira moleza mtima, pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. M’chombomo anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, adapulumuka ndi madzi. Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m’thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu amene adapita Kumwamba, ndipo ali ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 95: 08.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Munthu sungakhale moyo ndi chakudya chokha, Koma ndi mau onse olankhula Mulungu. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01:12 – 15. (Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana anamuyesa, ndipo Angelo ankamutumikira).

 

Nthawi yomweyo Mzimu Woyera adapititsa Yesu ku chipululu. Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira. Yohane uja ataponyedwa m’ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu. Ankati, “Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati pa anthu. Tiyeni tipempherere anthu onse kuti alandire Mthenga Wabwino n’kuyambadi moyo watsopano.

 

1.     Atsogoleri a Mpingo athandize anthu ao kuyenda m'njira ya ungwiro powaphunzitsa nzeru zolapira machimo.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.

2.     Akhristu ofooka adzidzimuke mumtima mwao pa nthawi ino ya Lenti, pokumbukira chifundo chozama cha Yesu Khristu Mpulumutsi.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.

3.     Akatekumeni nawonso ayesetse kusiya makhalidwe oipa n’kusanduka anthu atsopano poika chikhulupiriro chao chonse pa Yesu Khristu.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.

4.     Ife tomwe tilimbikire kuchita zolungama ndi kuwonetsa anthu onse mtima wachifundo, pokumbukira zomwe zija tidalonjeza pa ubatizo.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.

Atate, mverani mapemphero athuwa ndipo mutiwongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti ntchito zathu za nthawi ino ya Lenti zikhale zodzetsa ufumu wanu m'dziko lino lapansi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Tuesday, February 13, 2024

TSIKU LA PHULUSA

TSIKU LA PHULUSA

“Ino ndi nthawi yoti tiyanjanenso ndi Mulungu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YOWELE: YOWELE 02: 12 – 18. (Ng’ambani mitima yanu osati zovala zanu chabe).

 

Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwerani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng’ambani mitima yanu osati zovala zanu chabe. Bwerani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthawi zonse ndi wokonzeka kukhululuka. Mwina mwake adzasintha mtima

ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu. Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitane msonkhano waukulu. Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m’chipinda mwao, abwere. Ansembe azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena awanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asawaseke pomafunsana kuti, ‘ha, ali kuti Mulungu waoyo?”’ Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adawachitira chifundo anthu ake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51: 03 – 06, 12 – 13.

 

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

 

Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika,

Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu,

Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga,

Mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.

 

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

 

Zolakwa zanga ndikuzidziwa,

Kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthawi zonse,

Ndachimwira Inu, Inu nokha,

Ndachita choipa pamaso panu.

 

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,

Muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika,

Musandipirikitse pamaso panu,

Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.

 

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

 

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,

Mulimbitse mwa ine mtima womvera,

Ambuye, tsekulani milomo yanga,

Ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu.

 

Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO:  02 AKORINTO 05: 20 – 06: 02. (Muvomere kuyanjananso ndi Mulungu… Pa nthawi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima).

 

Abale, ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwina ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m’dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu. Paja Mulungu akuti, “pa nthawi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthawi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi Lerotu tsiku la chipulumutso.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 95: 08.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, Ndipo mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 06: 01 – 06, 16 – 18. (Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho).

 

Yesu adati, “chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba. Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m’nyumba zamapemphero ndiponso m’misewu yam’mizinda. Iwowa amachita zimenezo kuti anthu awatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziwa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m’nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu ya m’mizinda. Amachita zimenezo kuti anthu awaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukuti upemphere, lowa m’chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 










Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, ino ndi nthawi yabwino imene Mulungu alikukomera anthu mtima. Tiyeni tidandaule kwa Atate athu a Kumwamba, pozindikira zosowa zathu ndi za anthu onse:

 

1.     Ansembe akhale akazembe enieni a Yesu Khristu polalika Mthenga Wabwino ndi kutsogolera akhristu ao m’njira ya kulapa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu amilandu ndi onse amene adaleka kupemphera, adzuke ndi kubwera kwa Mulungu Atate ao pa nthawi ino ya Lenti.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni alimbike m'chikhulupiriro ndipo aonetse kulapa kwenikweni pakuwongola makhalidwe ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife amene talandira phulusa tsopano apa, tikhale nawo mtima watsopano, pogonjetsa zilakolako zoipa pochita ntchito zachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mutibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, ndipo pakamwa pathu padzayamika ulemu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, February 10, 2024

LAMULUNGU LA 06 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 06 PA CHAKA – B.

“Yesu adadzatichotsa khate la mumtima.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LEVITIKO: LEVITITKO 13: 01 – 02, 44 – 46. (Munthu akakhala ndi nthenda ya khate, akhale payekha kunja kwa mahema).

 

Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “munthu akakhala ndi chithupsa pathupi pake, kapena m’buko, kapena chikanga, ndipo mwina nkusanduka ngati nthenda ya khate pakhungu pakepo, munthuyo abwere naye kwa wansembe Aroni kapena kwa aliyense mwa ana ake amene ali ansembe. Ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Wansembe ayenera kumtchula kuti ndi woipitsidwa, ali ndi khate lakumutu. Munthu wakhate avale sanza, ndipo tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wam’mwamba, ndipo azifuula kuti, “ndine woipitsidwa, ndine woipitsidwa. Wodwalayo adzakhalabe woipitsidwa nthawi zonse pamene ali ndi nthendayo, ndipo akhale kunja kwa mahema.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 32: 01 – 02, 05, 11.

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

 

Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa,

Amene machimo ake afafanizidwa.

Ngwodala amene Chauta samawerengera mlandu wake,

Amene mumtima mwake mulibe zonyenga

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

 

Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu,

Sindidabise kuipa kwanga,

Ndidati, ‘ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,’

Pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

 

Sangalalani ndi kukondwa,

Inu nonse okonda Mulungu,

Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.

 

Ambuye, Inu ndiye kothawira kwanga; mwa Inu ndimapezamo chimwemwe ndi chipulumutso.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 10: 31 – 11:01. (Muzinditsanzira ine, monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu).

 

Abale, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu. Moyo wanu ukhale wosaphunthwitsa Ayuda, kapena anthu a mitundu ina, kapenanso Mpingo wa Mulungu. Muzichita monga momwe ndimachitira ine. Ndimayesa kukondweretsa anthu onse pa zonse. Sindifunafuna zokomera ineyo, koma ndimafunafuna zokomera anthu onse, kuti apulumuke. Muzinditsanzira ine monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 07: 16.

Alleluia, Alleluia – Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu. Mulungu wadzathandiza anthu ake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01: 40 – 45. (Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi).

 

Munthu wina wakhate adadza kwa Yesu. Adamugwadira nayamba kumdandaulira. Adati, “mutafuna, mungathe kundichiritsa.” Yesu adamumvera chifundo. Adatambalitsa dzanja nkumukhudza nati, “chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi. Tsono Yesu adamlamula kuti apite, namuuza mau amphamvu. Adati, “chenjera, usakambire wina aliyense zimenezo. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.” Koma munthuyo atachoka pamenepo, adayamba kumaulula zonse, ndi kufalitsa nkhani imeneyi, kotero kuti Yesu sadathenso kuwonekera poyera m’mudzi uliwonse. Nchifukwa chake ankakhala kwina, kumalo kosapitapita anthu, koma anthu ankabwerabe kwa Iye kuchokera uku ndi uku.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, monga wakhate uja, nafenso titembenukire kwa Ambuye ndi kuwadandaulira kuti,

Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa:

 

1.     Ansembe ndi atsogoleri a Mpingo awamvere chifundo anthu ochimwa ndi kuwalandira, pokhala nawo mtima womwe unali mwa Yesu Khristu.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

2.     Anthu akhate ndi ena onse ovutika azindikire kukoma mtima kwa Mulungu polandira chisamaliro kuchokera kwa anthu anzao.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

3.     Anthu amene mitima yao ikukangamira ku zoipa atsekule maso ao ndi kutembenukira kwa Mulungu pozindikira umphawi wao.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

4.     Ife amene adatiyeretsa kawirikawiri, tilimbikire kumtsira Iye ulemu ndi kukondweretsa anzathu pa zochitika zathu zonse.
Ambuye, ngati mufuna, mutha kutichiritsa.

Atate, tikuyamika chifundo chanu, chifukwa muli wokonzeka kuchiritsa anthu onse amene akudandaulirani ndi mtima wolapa. Mwa Yesu Khristu Ambuye anthu. Amen.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...