Saturday, January 27, 2024

LAMULUNGU LA 04 PA CHAKA – B

 

                                            LAMULUNGU LA 04 PA CHAKA – B
                                               “Yesu ankaphunzitsa ndi ulamuliro.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTORONOMO: DEUTORONOMO 18:15 – 20. (Ndidzawatumizira mneneri ndipo adzalankhula m’dzina langa).

 

Mose adawauza anthu kuti: “Chauta adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo. Pa tsiku lija mudaasonkhana pa phiri la Horebuli, mudaapempha kuti, ‘tisamvenso Chauta, Mulungu wathu, akulankhula, ngakhale kuwonanso moto waukulu choterewu, kuti tingafe.’ Apo Chauta adaandiwuza kuti, ‘zonse zimene apemphazi anena mwanzeru. Ndidzawatumizira mneneri wonga iwe, wochokera mwa iwo amene. Ndidzamuuza zoti anene, ndipo   iyeyo azidzauza anthu zonse zimene ndikumlamula. Mneneriyo akalankhula m’dzina langa, Ine ndidzalanga aliyense wosamvera mau angawo. Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m’dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m’dzina la milungu ina.’”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95: 01 – 02, 06 – 09.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

 

Bwerani, timuimbire Chauta,

Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa,

Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,

Timuimbire nyimbo zotamanda.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

 

Bwerani, timpembedze ndi kumlambira,

Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,

Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ndife anthu a pa busa lake,

Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

 

Lero mukadamverako mau ake!

Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,

Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,

Pamene makolo anu adandiputa mondiyesa

Ngakhale anali ataona ntchito zanga.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 07: 32 – 35. (Mkazi wosakwatiwa, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m’mene angakondweretsere Ambuye).

 

Abale, ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhawa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amateketseka ndi zapansi pano, kuganiza za m’mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangoteketseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m’thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansi pano, kuganiza za m’mene angakondweretsere mwamuna wake. Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 04:16,

Alleluia, Alleluia – Anthu okhala mu mdima aona kuwala kwakukulu. Anthu okhala m’dziko la mdima wabii wa imfa, kuwala kwawaonekera. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01: 21 – 28. (Ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro).

 

Pa nthawi yomweyo, onsewo ankapita ku Kapernao. Tsono litafika tsiku la sabata. Yesu adalowa m’nyumba yamapemphero, nayamba kuphunzitsa. Zophunzitsa zake anthu zidaawagwira mtima kwambiri, chifukwa ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro, kusiyana ndi m’mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo. M’nyumba yamapempheroyo mudaalowa munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuwa kuti, “kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazerete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziwani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.” Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “khala chete, tuluka mwa munthu yu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwedeza kwamphamvu munthuyo, ndipo udakuwa koposa, nkutuluka. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, “kodi zimenezi nzotani? Zophunzitsa zamtundutu zimenezi! Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu, ndipo ikumumveradi.” Mwansanga mbiri yake idawanda ponseponse ku dera lonse la ku Galileya.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, monga Mulungu walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake, ifenso tsopano timupemphe kudzera mwa Yesu Khristu yemweyo kuti alimbikitse chikhulupiriro chathu:

1.     Atsogoleri a Mpingo alalike mau a Mulungu mokhulupirika ndi mopanda mantha, pokumbukira kuti alikupitiriza ntchito ya Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamula maiko akhale otekeseka ndi ubwino wa anthu ao, asawapondereze kapena kuwalanda ufulu, koma awatsogolere m’njira ya mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anzathu odwala ndi ena onse ovutika m’mitima mwao apeze mwa Yesu Khristu mphamvu zopirira mavuto pokhulupirira ntchito zake zowapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse tili muno tidziwe kumanga moyo wathu pa chikondi cha Ambuye, pomatekeseka ndi ntchito zodzetsa ufumu wa Mulungu pakati pa anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, potula mapemphero athuwa m’manja mwanu, tikuyamikani chifundo chanu chofuna kupulumutsa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, January 20, 2024

LAMULUNGU LACHITATU PA CHAKA – B

LAMULUNGU LACHITATU PA CHAKA – B

Yesu akuti: “Siyani zonse, ndipo munditsate!”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MNENERI YONA: YONA 03: 01 – 05, 10 (Anthu aku Ninive adasiya makhalidwe ao oipa).

 

Chauta adalankhula ndi Yona kachiwiri, namuuza kuti, “Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukulu uja, ukaulalikire uthenga umene ndikukuuza.” Yona adanyamuka, napita ku Niniveko, potsata mau a Chauta. Mzindawo unali waukulu kwambiri, wofunika masiku atatu kuudutsa. Yona adalowa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!” Anthu a ku Ninive adakhulupirira Mulungu. Adalengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamng’ono yemwe, asale zakudya, ndipo avale chiguduli. Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m’mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osawapatsa chilango chimene adaati adzawapatsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 25: 04 – 09.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta,

Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu,

Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza,

Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

 

Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika,

Chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale,

Koma mundikomere mtima, Inu Chauta,

Chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

 

Chauta ndi wabwino ndi wolungama,

Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake,

Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,

Amawaphunzitsa njira zake.

 

Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 07: 29 – 31. (Dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita).

 

Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthawi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire. Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo. Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisawagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopano, likupita.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 01: 15.

Alleluia, Alleluia – Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupilira Uthenga Wabwino. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO  01: 14 – 20. (Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu).

 

Yohane uja ataponyedwa m’ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu. Ankati, “Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.” Pamene Yesu ankayenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu awiri, Simoni ndi m’bale wake Andrea, akuponya khoka m’nyanjamo, popeza kuti anali asodzi. Yesu adawauza kuti, “inu, munditsate, ndikakusandutsani asodzi a anthu.”  Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pang’ono, Yesu adaona Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwowo anali m’chombo, akukonza makoka ao, nthawi yomweyo Iye adawaitana. Pamenepo iwowo adasiya bambo wao Zebedeo m’chombomo pamodzi ndi antchito ake, namatsata Yesu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pozindikira kufooka kwathu ndiponso umphawi wa anthu, tiyeni tipemphe Atate a Kumwamba kuti atithandize kulapa ndi kukhulupirira Mthenga Wabwino:

 

1.     Ansembe onse atsogolere anthu ao pa njira ya ungwiro, powaphunzitsa za kulapa, azitsata Yesu Khristu ndi mtima wosagawika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu okhala mumdima, osadziwa Mthenga Wabwino, atsekulire Mulungu mitima yao pomufunafuna Iyeyo ndi kuchita zolungama.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao ndi kukhulupirira Mthenga Wabwino, ndipo asonyeze kulapa kwao pakutenga makhalidwe okomera Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe, tisaleke kuwongola maganizo athu ndi mayendedwe athu, pomagwiritsa ntchito mau a Mulungu, kuti ifenso tisanduke asodzi a anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate okoma mtima, landirani mapemphero athuwa, ndipo mukhazikitse ufumu wanu wachikondi m’mitima mwathu ndi mwa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, January 13, 2024

LAMULUNGU LACHIWIRI PA CHAKA - B

LAMULUNGU LACHIWIRI PA CHAKA - B

“Adakapeza m’bale wake, napita naye kwa Yesu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LOYAMBA LA SAMUELE: 01 SAMUELE 03: 03 – 10, 19. (Yankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva).

 

Samuele anali gone m’Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthawiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime. Tsono Chauta adaitana kuti, “Samuele!” Iye adayankha kuti, “wawa!” Adathamangira kwa Eli nati, “Ndabwera, ndamva kuitana.” Koma Eli adati, “sindidakuitane, kagone.” Motero Samuele adapita kukagona. Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva Ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “sindidakuitane mwana wanga, kagone.” Pamenepo nkuti Samuele asanadziwe Chauta, ndipo mau a Chauta nkuti asanaululidwe kwa iyeyo. Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nanena kuti, “Ndabwera mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo. Tsono adauza Samuele kuti, “pita, kagone. Akakuitananso, ukanene kuti, Lankhulani, Inu Chauta, poti mtumiki wanune ndili kumva.” Choncho Samuele adapita kukagona kumalo kwake. Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthawi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.” Monse Samuele ankakula, Chauta anali naye, motero zonse zimene Samueleyo ankanena zinkachitikadi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 40: 02, 04, 07 – 10.

 

Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.

 

Ine ndidayembekeza Chauta kuti adzandithandize,

Adaweramira pansi nkuyang’ana kwa ine, namva kulira kwanga,

Mulungu waika nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,

Nyimbo yake yotamanda Iye.

 

Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.

 

Simudafune nsembe ndi zopereka,

Koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera,

Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo,

Tsono ndidati, Ndilipo, ndikubwera.

 

Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.

 

Monga zidalembedwa za ine m’buku la malamulo,

Ndimakonda kuchita zimene mumafuna,

Inu Mulungu wanga,

Malamulo anu ali mumtima mwanga.

 

Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.

 

Ndalalika Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu,

Pa msonkhano waukulu,

Sindidatseke pakamwa,

Monga Mukudziwa, Inu Chauta.

 

Ndilipo Ine, Mulungu wanga! Ndabwera kudzachita kufuna kwanu.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 06: 13 – 15, 17 – 20. (Kodi inu simudziwa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu?)

 

Abale, thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo. Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso. Kodi inu simudziwa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Monga Tsono ine nkutenga ziwalo za Khristu nkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Chosatheka.  Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala Mzimu umodzi. Thawani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, Tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 01: 41, 17b.

Alleluia, Alleluia – Tampeza Mesiya – ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Kudzera mwa Iye, Mulungu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 01: 35 – 42. (Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye Tsiku limenelo).

 

M’mawa mwakenso Yohane anali pamalo pomwepo pamodzi ndi ophunzira ake ena awiri. Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.” Ophunzira awiri aja atamva mauwo, adatsatira Yesu. Yesu adacheuka naona kuti akumtsatira, Tsono adawafunsa kuti, “kodi ulendowu?” Iwo adati, “timati tidziwe, kodi mumakhala kuti, Rabi?” (Tanthauzo la Rabi ndiye kuti, Mphunzitsi.) Yesu adati, “tiyeni mukakuwone.” Iwo adapita naye. Pamenepo nthawi inali ngati 4 koloko madzulo. Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye tsiku limenelo. M’modzi mwa awiri aja amene adaamva mau a Yohane natsatira Yesu, anali Andrea, m’bale wake wa Simoni Petro. Iye adayamba kukapeza m’bale wakeyo Simoni, namuuza kuti, “Tampeza Mesiya.” (Ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.) Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.)

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, ifenso tapezana ndi Ambuye lero ndipo tamva mau ao. Tsono tipemphe chithandizo chao malinga ndi zosowa zathu ndi za Mpingo wonse:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo alalike mau a Mulungu ndi chikhulupiriro cholimba; atsimikizire anthu onse kuti Mpulumutsi amakhala pakati pao.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu owe adakali padera osadziwa Mthenga Wabwino alimbikire kufunafuna Mulungu, amutsekulire Iye mitima yao kuti amve mau ake.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anyamata ndi atsikana okhulupirira Yesu Khristu aonetsane makhalidwe odziletsa ndi odzilemekeza pokumbukira kuti thupi lao ndi nyumba ya Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe amene tapeza Mpulumutsi, tiyesetse kukokera abale athu kwa Iyeyo kuti iwonso adzamve mau ake ndi kulandira chipulumutso chake.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani chifukwa simuleka kuitana anthu mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, January 6, 2024

CHAKA CHA EPIFANIA – B

CHAKA CHA EPIFANIA – B

“Yesu Mpulumutsi adadzera anthu a mitundu yonse.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 60: 01 – 06. (Ulemelero wa Chauta udzawoneka).

 

Iwe Yerusalemu dzuka, wala, kuwala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuwalira. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuwalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Anthu a mitundu ina adzatsata kuwala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuwa limene likutuluka kumene. Yang’ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali. Ana ako aakazi adzatengedwa m’manja ngati ana. Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe. Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing’onozing’ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 72: 01 – 02, 07 – 08, 10 – 13.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,

Patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo,

Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama,

Ndiponso anthu anu osauka mosakondera.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo,

Mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso,

Mafumu onse adzaigwadira,

Ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Ndithu iyo idzalanditsa anthu osowa amene amaiitana,

Idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda wowathandiza,

Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osowa,

Ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphawi.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 03: 02 – 03, 05 – 06. (Chinsinsicho nchakuti anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda).


Abale, kumva mudamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake. Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa. Chinsinsi chimenecho anthu a mibadwo yakale sadachidziwe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake. Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 02: 02.

Alleluia, Alleluia – Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 02: 01 – 12. (Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye).

 

Yesu adabadwira m’mudzi wa Betelehemu, m’dziko la Yudeya, pa nthawi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Iwowo ankafunsa kuti, “ali kuti mwana amene adabadwa kuti akhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.” Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu onse a m’Yerusalemu nawonso adavutika nazo. Tsono Herodeyo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, nawafunsa kuti, “kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?” Iwo adati, “M’mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti, Iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe wamng’ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri amene adzalamulira anthu anga Aisraele.” Pamenepo Herode adawaitanitsa paseri akatswiri a nyenyezi aja, nawafunsitsa za nthawi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo. Kenaka adawatumiza ku Betelehemu nkuwauza kuti, “pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziwitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.” Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idawatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo. Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Adalowa m’nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure. Mulungu adawachenjeza m’maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tonse taitanidwa kudzalandira chipulumutso mwa Yesu Khristu. Tiyeni tsono, tipemphe Mulungu kuti anthu onse avomere kuitana kwakeko.

 

1.     Eklezia wa Mulungu, aonetse anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu, m’maphunziro ake, ndinso m’ntchito zake zosamalira anthu osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu onse amene sanamvebe Mthenga Wabwino, atsekulire Mulungu mitima yao, amfunefune mwakhama mpaka adzampezedi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akulu olamulira maiko atsate ubwino wa anthu ao mopanda tsankho, ndipo awapatse ufulu weniweni pa za chipembedzo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse talandira udindo wotsogolera anzathu m’njira ya chipulumutso; kuwala kwa Yesu Khristu kuwonekere m’mayendedwe athu ndi m’zochita zathu zonse.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, tikupereka kwa Inu mapemphero athuwa pamodzi ndi zosowa za anthu onse. Tikuyamika kukoma mtima kwanu kofuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...