LAMULUNGU LA 04 MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA B
“Mulungu akwaniritsa lonjezo lake.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LACHIWIRI LA SAMUELE; 02 SAMUELE 07: 01 – 05, 08 – 12, 14, 16. (Banja lako pamodzi ndi ufumu wako ndidzazikhazikitsa mpaka muyaya pamaso panga).
Nthawi imene mfumu Davide anali atakhazikika m’nyumba mwake, Chauta adampumuza kwa adani ake onse omzungulira. Tsono adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m’nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m’hema.” Natani adauza mfumu kuti, “Ai, chitani chilichonse chimene mukuganiza mumtima mwanu, poti Chauta ali nanu.” Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti, “Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Kani wayesa udzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo? Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ndidakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa kuja kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele. Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzakumveketsa dzina lako kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi. Ndipo ndidzawasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuwakhazika kumeneko kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzawazunzanso monga momwe adaachitira kale lija, kuyambira nthawi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidakupumitsa kwa adani ako onse.
Kuwonjezera pamenepo, Chauta akukuuza kuti, Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako. Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako ku manda, ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba. Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m’mene bambo amalangira ana ake. Tsono banja lako pamodzi ndi ufumu wako ndidzazikhazikitsa mpaka muyaya pamaso panga. Ndithudi, ufumu wako udzakhazikika osatha konse.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 89: 02 – 05, 27, 29.
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika.
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika,
Ndidzalalika ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse,
Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya,
Kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika.
“Ndachita chipangano ndi wosankhidwa wanga,
Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya,
Ndidzasungira mibadwo yonse mpando wako waufumu.’
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika.
Iye adzandiwuza kuti, ‘Inu ndinu Atate anga,
Mulungu wanga, Thanthwe londipulumutsa,’
Ndidzamkonda nthawi zonse ndi chikondi changa chosasinthika,
Chipangano changa ndi iye sichidzaphwanyika.”
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 16: 25 – 27. (Zimene zinali zachinsinsi, ndipo zidaabisika pa zaka zonse kuyambira kalekale. Koma tsopano zatulukira poyera).
Abale, tiyeni tilemekeze Mulungu! Iye ali ndi mphamvu za kukulimbitsani potsata Uthenga Wabwino umene ndimaulalika, umene ndi mau olengeza za Yesu Khristu. Zimenezi zinali zachinsinsi, ndipo zidaabisika pa zaka zonse kuyambira kalekale. Koma tsopano zatulukira poyera kudzera m’zimene aneneri adalemba, ndiponso kudzera m’lamulo la Mulungu wachikhalire zadziwika kwa anthu a mitundu yonse, kuti azizikhulupirira ndi kuzimvera.
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 01: 38.
Alleluia, Alleluia – Ndine mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 01: 26 – 38 (Tamvera! Udzabala mwana).
Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete. Adamtuma kwa namwali wina wosadziwa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria.
Mngelo uja adadza kwa iye nati, “Moni, inu amene Mulungu wakukomerani mtima kotheratu. Ambuye ali nanu.” Maria adadzidzimuka nawo kwambiri mau amenewa, nayamba kusinkhasinkha kuti kodi moni umenewu ndi wa mtundu wanji? Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima. Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu. Adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse. Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide, ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya. Ufumu wake sudzatha konse.” Koma Maria adafunsa mngeloyo kuti, “Zimenezi zidzachitika bwanji, popeza kuti sindidziwa mwamuna.” Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu. Onani, m’bale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.” Apo Maria adati, “Ndine mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo.” Ndipo mngeloyo adamsiya.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, monga Paulo Woyera, ifenso tiyamike Atate athu a Kumwamba amene adatidalitsa kopambana potipatsa Mwana wao, Yesu Khristu ndipo tipempherere anthu onse:
1. Akhristu onse akonzekere kulandira Mpulumutsi wao ndi chikondi chachikulu, potsata chitsanzo cha Virgo Maria.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.
2. Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, podziwa kuti Yesu Khristu adadzera anthu onse, nafuna kuwasonkhanitsa onse mu ufumu wake.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.
3. Azimai amene ali ndi pakati akhale nawo maganizo omwe anali mwa Mai Maria, poyembekezera kubadwa kwa mwana ndi mtima wothokoza.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.
4. Ife tonse muno, tiwonetse nkhope yowala ndiponso mtima wachifundo pa ntchito zathu zotumikira anzathu, podziwa kuti Ambuye akudzatiyendera.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.
Atate, mutikomere mtima polandira mapemphero athuwa, ndipo kwa Inu kukhale ulemerero ndi chiyamiko mpaka muyaya. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:
Post a Comment