Saturday, December 16, 2023

LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA B [Gaudete Sunday]

LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA B

[Gaudete Sunday]

“Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 61: 01 – 02, 10 – 11. (Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta).

 

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am’ndende kuti adzawamasula. Wandituma kukalengeza za nthawi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti ye wamveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluwa m’khosi. Ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adadzalamo, momwenso Chauta adzawonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: LUKA 01: 46 – 50, 53 – 54.

 

Mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga.

 

Mtima wanga ukutamanda Ambuye,

Ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,

Popeza kuti wayang’ana kutsika kwa mtumiki wake,

Ndithu kuyambira tsopano anthu a mibadwo yonse adzanditcha wodala.

 

Mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga.

 

Pakuti Iye amene ali wamphamvu wandichitira zazikulu,

Ndipo dzina lake nloyera,

Amawachitira chifundo anthu a mibadwo ndi mibadwo,

Amene amamlemekeza.

 

Mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga.

 

Anthu anjala wawakhutitsa ndi zabwino,

Anthu olemera nkuwabweza osawapatsa kanthu,

Wadzathandiza anthu ake Aisraele,

Pokumbukira chifundo chake.

 

Mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU AM’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 01 ATESALONIKA 05: 16 – 24. (Akusungeni athunthu m’nzeru, mumtima ndi m’thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu).

 

Abale, khalani okondwa nthawi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi. Musayese kuletsa ntchito ya Mzimu Woyera. Musanyoze mau olalikidwa m’dzina la Mulungu, koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene Zili zabwino, ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse. Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m’nzeru, mumtima ndi m’thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu. Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YESAYA 61: 01 (YONENEDWA MU LUKA 04: 18).

Alleluia, Alleluia – “Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa Ine. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka.” – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 01: 06 – 08, 19 – 28. (Pakati panupa pali wina amene inu simukumdziwa).

 

Mulungu adaatuma munthu wina, dzina lake Yohane. Iyeyu adaabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuwala kuja, kuti anthu onse akhulupirire chifukwa cha umboni wakewo. Sikuti iyeyo ndiye anali kuwalako ai, koma adangobwera kudzachitira umboni kuwalako. Nthawi ina akuluakulu a Ayuda a ku Yerusalemu adaatuma ansembe ndi Alevi ena kukafunsa Yohane kuti, “Kodi iwe ndiwe yani?” Iye adayankha mosabisa konse, adanenetsa ndithu kuti, “Inetu sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja ai.” Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.” Tsono adamuuza kuti, “Tanena zenizenitu, kuti tikawafotokozere bwino amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe yani?” Yohane adawayankha kuti, “Monga adaanenera mneneri Yesaya: Ine ndine liwu la munthu wofuula m'chipululu; akunena kuti, Ongolani mseu wodzadzeramo Ambuye.” Anthu aja adaawatuma ndi Afarisi. Tsono adafunsa Yohane kuti, “Ngati sindiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena Eliya, kapenanso Mneneri tikumuyembekeza uja, nanga bwanji umabatiza?” Yohane adawayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziwa. Iyeyu ngwobwera pambuyo panga, komabe sindili woyenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake?” Zimenezi zidachitikira ku Betaniya, kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatiza.

 

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Ambuye ali pafupi, tiyeni tipempherere anthu onse ndi kuyamika Atate athu a Kumwamba amene adatipatsa Mpulumutsi:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo alalikire Mthenga Wabwino molimbika ndi kusonyeza anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu.
Bwerani, Ambuye, mudzatipulumutse.

2.     Akhristu onse akhale okondana, ndipo ntchito zao zachifundo ziwonetse kuti Yesu Mpulumutsi adabweradi pansi pano kudzakhala pakati pa anthu.
Bwerani, Ambuye, mudzatipulumutse.

3.     Anthu odwala ndipo ena onse amene akuvutika m’mitima mwao alandire chisangalalo kuchokera kumwamba pa nthawi ino ya Khrismasi.
Bwerani, Ambuye, mudzatipulumutse.

4.     Ife tonse amene tasonkhana pano tilimbikire kuchita ntchito zabwino ndi kudzetsa chimwemwe cha chipulumutso m’mitima ya anthu.
Bwerani, Ambuye, mudzatipulumutse.

Atate, tikuyamika chifundo chanu potipatsa Mwana wanu, chifukwa timapeza mwa iyeyo kuwala kotitsogolera ku moyo wosatha. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...