Saturday, December 9, 2023

LAMULUNGU LA 02 MU NYENGO YA ADVENTI – CHAKA B

LAMULUNGU LA 02 MU NYENGO YA ADVENTI – CHAKA B

“Tikonze mseu wodzeramo Ambuye.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 40: 01 – 05, 09 – 11. (Konzani njira ya Chauta).

 

“Atonthozeni mtima, atonthozeni mtima anthu anga,” akutero Mulungu wanu. “Muwalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muwauze kuti nthawi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndawalanga mowirikiza chifukwa cha machimo ao.” Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m’thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m’chipululu. Chigwa chilichonse achidzaze, phiri lililonse ndi gomo lililonse alitsitse. Dziko lokumbikakumbika alisalaze, malo azitundazitunda awasandutse zidikha. Motero ulemerero wa Chauta udzaoneka, anthu onse adzauwona. Chauta mwini wake ndiye wanena zimenezi.” Kwera pa phiri lalitali, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Yerusalemu. Ufuule kwamphamvu, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Ziyoni. Kweza mau, usaope. Uuze mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera.” Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.

Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuwakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 85: 09 – 14.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

 

Ndimve zimene Chauta adzalankhula,

Chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake,

Kwa anthu ake oyera mtima,

Ngati sabwereranso ku zopusa zao.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

 

Zoonadi, Mulungu ali wokonzekera kuti apulumutse amene amamuwopa,

Kuti ulemerero wake ukhale m’dziko lathu.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

 

Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana,

Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana,

Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano,

Ndipo Mulungu wakumwamba adzawalungamitsa.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

Inde, Chauta adzapereka zabwino,

Ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri,

Mulungu ndi wolungama chikhalire,

Chilungamo chake chimaongolera zochita zake zonse.


Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU AM’KALATA YACHIWIRI YA PETRO WOYERA; 02 PETRO 03: 08 – 14. (Tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano).

Inu okondedwa, chinthu chimodzi musaiwale, kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka chikwi chimodzi, ndipo zaka chikwi chimodzi zili ngati tsiku limodzi. Sikuti akuzengereza

kuchita zimene adalonjeza, monga m’mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima. Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m’menemo zidzapseratu. Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu? Muziyembekeza tsiku la Ambuye ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo zakumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m’motomo. Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m’mene

chilungamo chizidzakhalamo. Choncho inu okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 03: 04, 06.

Alleluia, Alleluia – “Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu.” Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA; MARKO 01: 01 – 08. (Ongolani njira).

 

Uwu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Udayamba monga mneneri Yesaya adalembera m’buku mwake kuti: “Mulungu akuti, Ndidzatuma wamthenga wanga m’tsogolo mwako kuti akakonzeretu njira yoti iwe udzapitemo. Liwu la munthu wofuula m’chipululu: akunena kuti, Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.” Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.” Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumawabatiza mu Mtsinje wa Yordani. Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wa ngamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m’chiwuno. Chakudya chake chidaali dzombe ndi uchi wam’thengo. Kulalika kwake ankati, “Pambuyo panga pakubwera wina wamphamvu kuposa ine, mwakuti ineyo ndine wosayenera ngakhale kuwerama nkumasula zingwe za nsapato zake. Ine ndakubatizani ndi madzi, koma Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pamodzi ndi anthu onse amene akuyembekeza kudza kwa Ambuye, tiyeni tikweze mitima yathu ndi mapemphero athu kumwamba:

 

1.     Ansembe ndi atsogoleri onse alalike Mthenga Wabwino molimbika, ndipo autse chikhulupiriro chachikulu m’mitima mwa anthu.
Ambuye, tiwonetseni chikondi chanu ndipo mutipulumutse.

2.     Ayuda, maso ao atsekule ndipo mitima yao igonjere Yesu Khristu Mpulumutsi, pokhulupirira zomwe zidalembedwa m’Malembo Oyera.
Ambuye, tiwonetseni chikondi chanu ndipo mutipulumutse.

3.     Akatekumeni alimbike pa maphunziro ao ndipo asiye makhalidwe oipa, mpaka nawonso adzabatizidwe m'dzina la Yesu Khristu.
Ambuye, tiwonetseni chikondi chanu ndipo mutipulumutse.

4.     Ife tonse tili muno tipemphererane kuti mayendedwe athu ndi ntchito zathu zifulumize kudza kwa Ambuye pakati pa anzathu.
Ambuye, tiwonetseni chikondi chanu ndipo mutipulumutse.

 

Atate, tikutula m’manja mwanu mapemphero athuwa pamodzi ndi mafuno a anthu onse, tikuyamika chifundo chanu potipatsa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...