Saturday, December 2, 2023

LAMULUNGU LA 01 MU NYENGO YA ADVENTI – CHAKA B

 

LAMULUNGU LA 01 MU NYENGO YA ADVENTI – CHAKA B

“Tikhale maso ndi kumakonzekeratu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 63: 16 – 17; 64: 01, 03 – 08. (Inu Chauta, bwanji osang’amba mlengalenga kuti mutsike pansi?).

Inu, Chauta, ndinu Atate athu, ndinu Momboli wathu kuyambira kalekale. Chifukwa chiyani mukutisokeretsa pa njira zanu? Bwanji mukutilola kuti tizikhala ouma mtima kotero kuti sitikukuwopaninso? Bwererani chifukwa cha atumiki anu, mafuko a anthu amene ali cholowa chanu. Inu Chauta, bwanji osang’amba mlengalenga kuti mutsike pansi? Nthawi ina yake mudatsika pansi pano kudzachita zinthu zoopsa zimene sitidaziyembekeze. Mapiri atakuwonani, adanjenjemera ndi mantha. Chikhalire palibe ndi m’modzi yemwe amene adaona kapena kumva za Mulungu wina wonga Inu, wochitira zotere anthu omkhulupirira. Inu mumawalandira onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amayesetsa kuyenda monga Inu mufunira. Inde mudatikwiyira, komabe ife tidapitiriza kuchimwa. Takhala ochimwadi nthawi yaitali, kodi tidzapulumuka kumene? Tonsefe tasanduka ngati anthu oipitsidwa, ndipo ntchito zathu zonse zabwino zakhala ngati nsanza zauve. Tonsefe tikufota ngati masamba, tikuuluzika ndi machimo athu, ngati tikuuluzika ndi mphepo. Palibe amene amatamira dzina lanu popemphera, kapena amene amatekeseka nzopempha chithandizo kwa Inu. Mwatifulatira ndipo mwatisandutsa akapolo a machimo athu. Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu. Ife tili ngati mtapo, Inu muli ngati woumba. Mudatipanga tonse ndi manja anu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 80: 02 – 03, 15 – 16, 18 – 19.

 

Inu Mulungu, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

 

Imvani, Inu Mbusa wa Israele,

Inu amene mumakhala pa akerubi ngati pa mpando wanu wachifumu,

Onetsani mphamvu zanu,

Ndipo mubwere kudzatipulumutsa.

 

Inu Mulungu, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

 

Mutembenukirenso kwa ife, Inu Mulungu Wamphamvuzonse,

Muyang’ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone,

Samalani mpesawo, mtengo woyambirira,

Umene Inu mudaubzala ndi dzanja lanu lamanja.

 

Inu Mulungu, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

 

Koma ndi dzanja lanu muteteze anthu amene mudawasankha,

Anthu amene Inu nomwe mwawalimbikitsa kuti akutumikireni,

Tsono sitidzakusiyaninso, tipatseni moyo,

Ndipo tidzatama dzina lanu mopemba.

 

Inu Mulungu, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 01 AKORINTO 01: 03 – 09. (Tili kudikira kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu).

Abale, Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Za madalitso ao mwa Khristu. Nthawi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu. Zoonadi mwa Khristu mwakhala anthu olemera pa zonse, makamaka pa kulankhula ndi pa kudziwa zinthu, popeza kuti mau ochitira Khristu umboni akhazikika mwa inu. Nchifukwa chake palibe mphatso yauzimu imene yakuperewerani, pamene mukudikira kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iye adzakulimbitsani mpaka chimalizo, kuti mudzakhale opanda cholakwa pa tsiku la Ambuye athu Yesu Khristu. Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 85: 08.

Alleluia, AlleluiaTiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA; MARKO 13: 33 – 37. (Khalani maso, chifukwa simudziwa mwini nyumba adzabwerera nthawi yanji).

 

Yesu adati kwa ophunzira ake: “Tsono chenjerani, khalani maso, chifukwa simudziwa kuti nthawiyo idzakwana liti. Ndi monga ngati bwana amene akunyamuka ulendo kuchoka kunyumba

kwake. Amasiya zinthu m’manja mwa antchito ake, aliyense ntchito yake, ndipo amauza wapakhomo kuti azikhala maso. Nanunso tsono khalani maso, chifukwa simudziwa mwini nyumba adzabwerera nthawi yanji: kaya ndi madzulo, kaya ndi pakati pa usiku, kaya ndi tambala woyamba, kapena m’bandakucha. Atha kudzabwera mwadzidzidzi, tsono asadzakupezeni muli m’tulo. Zimene ndikunenazi, sindikuuza inu nokha ai, koma ndikuuza anthu onse kuti, Khalani maso.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Mulungu ndiye watiitana kuti tikhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu, tiyeni tipempherere anthu onse:

 

1.     Akhristu ofooka ndi osokera adzuke ndi kubwerera kwa Mulungu pa nyengo ino yokonzekera Khrismasi, pozindikira kuti chipulumutso chayandikira.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.

2.     Ayuda ndi anthu ena onse amene akadali mu mdima atsekule mitima yao polandira kuwala kwa Mthenga Wabwino.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.

3.     Akatekumeni alimbikire m’maphunziro ao ndi kukula m’chikhulupiriro, podziwa kuti mwa Yesu Khristu iwonso adzasanduka anthu olemera pa zonse.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.

4.     Ife amene tili muno tikhale maso ndi kuwonetsa changu pa moyo wathu wachikhristu pokonzekera chaka cha kubadwa kwa Ambuye.
Ambuye, bwerani, mudzatipulumutse.

 

Atate, mverani mapemphero athuwa pamodzi ndi mafuno a anthu onse: ndipo mutipatse ife tonse mtima wolakalaka kudza kwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...