KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA B
[MISA YA USIKU]
“Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 09: 01 – 07. (Mwana watibadwira).
Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina. Aneneratu za mfumu yam’tsogolo. Anthu amene ankayenda mumdima aona kuwala kwakukulu. Amene ankakhala m’dziko la mdima wandiweyani, kuwala kwawaonekera. Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m’mene anthu amakondwera nthawi ya masika, monganso m’mene anthu amakondwera pogawana zofunkha. Pakuti inu mwathyola goli limene linkawalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani. Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni. Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m’manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.” Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 01 – 03, 11 – 13.
Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!
Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!
Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!
Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku,
Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse,
Simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m’maiko onse.
Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere,
Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam’menemo,
Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam’menemo,
Mitengo yam’nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta,
Pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.
Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo,
Adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.
Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA TITO; TITO 02: 11 – 14. (Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse).
Abale, Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu. Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake. Paja lye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 02:10 – 11.
Alleluia, Alleluia – Ndadzakuuzani za uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 02: 01 – 14. (Lero Mpulumutsi watibadwira).
Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m’maiko ake onse. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao. Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m’banja ndi fuko la Davideyo. Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi. Pamene anali kumeneko, nthawi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m’nsalu namgoneka m’chodyera cha zoweta, chifukwa adaasowa malo m’nyumba ya alendo. Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoweta zao ku dambo usiku. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udawala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo adawauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m’mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye. Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m’chodyera cha zoweta.” Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pamodzi ndi Yesu Khristu amene adadzakhala munthu m’nzathu kuti atitsogolere kwa Atate ake, tiyeni tipemphe madalitso a Mulungu pa ife ndi pa anthu onse.
1. Tipempherere Eklezia wa Mulungu, kuti apitirize kuunikira anthu onse pakuwaonetsa kukoma mtima kwa Mulungu kofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu amene adakali m’mdima, osadziwa mthenga wabwino wa pa Khrisimasi, maso awo akopedwe, poona m’mene akhristu amakonderana.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Ana onse obadwira m’dziko lino lapansi alandire chikondi ndi chisamaliro chokwanira kuchokera kwa makolo ao, ndipo choncho akule ndi moyo wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse a m’parish yathu ino, moyo wathu ukhale wochitira Mulungu ulemu ndi wodzetsa mtendere ndi chimwemwe m’mitima ya anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, ife tonse ana anu tikuyamika chifundo chanu chosaneneka. chifukwa mudatidalitsa koposa, pakutipatsa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment