LAMULUNGU LA 32 PA CHAKA – CHAKA A.
“Simudziwa tsiku lake kapena nthawi yake.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA LUNTHA; LUNTHA 06: 12 – 16 (Luntha ndi lowala, lilibe mdima. Kwa olikonda, nkwapafupi kuliwona).
Luntha ndi lowala, lilibe mdima. Kwa olikonda, nkwapafupi kuliwona, olifunafuna amalipeza. Limadziwonetsa mwamsanga kwa anthu olifuna. Munthu wodzuka m’mamawa kuti alifune, sadzavutika, adzalipeza litakhala kale pakhomo pake. Kuikapo mtima pa za luntha ndiye kumvetsa bwino zinthu. Munthu wochita changu pofunafuna adzaona msanga mtendere wamumtima. Pajatu limayesayensa kufunafuna oyenera kulilandire, limadziwonetsa kwa iwowo m'njira zao, limapezekanso ndi m’maganizo ao omwe.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 63: 02 – 08.
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, Mulungu wanga.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani,
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu,
Thupi langa likulakalaka Inu,
Ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, Mulungu wanga.
Ndikukhumbira kukuwonani m’malo anu oyera,
Ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu,
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo,
Ndipo pakamwa panga padzakutamandani Inu.
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, Mulungu wanga.
Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera,
Mudzandikhutitsa ndi zonona,
Ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala.
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, Mulungu wanga.
Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu,
Usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu,
Inu mwakhala chithandizo changa,
Motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, Mulungu wanga.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 01 ATESALONIKA 04: 13 – 18 (Amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzawaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo).
Abale, tifuna kuti mudziweko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo. Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzawaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzawasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai. Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka. Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m’mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. Nchifukwa chake tsono muzithuzitsana mtima pokambirana zimenezi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 24: 42a, 44.
Alleluia, Alleluia – Khalani maso, chifukwa simudziwa tsiku limene Mwana wa Munthu adzabwera. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 25: 01 – 13 (Mkwati akubwera! Tulukani, kamchingamireni!).
Yesu adawauza ophunzira ake fanizo ili: “Pa nthawi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m’nsupa zao. Popeza kuti mkwati adaachedwa, onse aja adayamba kuwodzera, nagona tulo. Tsono pakati pa usiku kudamveka kufuula kuti, ‘Mkwati akubwera! Tulukani, kamchingamireni!’ Anamwali khumi aja adadzuka, nkuyamba kukonza nyale zao zija. Opusa aja adapempha ochenjera aja kuti, ‘Tipatseniko mafuta, onani nyale zathu zikuzima.’ Koma ochenjera aja adati, ‘Hi, ai, tikatero satikwanira tonsefe. Bwanji osati mungopita ku sitoro mukagule anu.’ Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adalowa naye pamodzi m’nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko. Kenaka m’mbuyo mwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’ Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziwani!’” Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziwa tsiku lake kapena nthawi yake?”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, ife amene tilikuyembekeza kubwera kwa Ambuye, tiyeni tipemphe Atate a Kumwamba kuti aike m’mitima mwathu ndi mwa anthu onse chikhulupiriro ndi chikondi choona:
1. Apapa, Aepiskopi ndi ansembe onse, atsogolere akhristu ao m’njira yaungwiro ndi yachikondi, powakumbutsa za kukonzekera kubwera kwa Ambuye.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu amene angokhulupirira zapansi pano adzidzimuke pakumva za chikondwerero chimene Mulungu wakonzera anthu ake Ufumu wa Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akhristu ofooka ndi osokera, adzuke ndi kubwerera kwa Mulungu ndi mtima wolapa, podziwa kuti Ambuye adzabwera pa nthawi imene ife sitiyembekezako.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tilimbikire kuchita ntchito zachifundo ndi kumapemphera, kuwopa kuti mwina nyale zathu zingazime.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mwa chifundo chanu mverani mapemphero athuwa. Mutikhazikitse m’chikondi chanu, kufikira tsiku limene adzatitenge. Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment