Saturday, November 18, 2023

LAMULUNGU LA 33 PA CHAKA – CHAKA A

“Tizigwiritsa Ntchito Mphatso za Mulungu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MIYAMBO; MIYAMBO 31: 10 – 13, 19 – 20, 30 – 31 (Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani?).

 

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasowa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa. Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu. Thonje amadzilukira yekha, ndipo nsalu amadziwombera yekha. Anthu osauka amawachitira chifundo, amphawi amawapatsa chithandizo. Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda. Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 127: 01 – 05.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta,

Amene amayenda m’njira zake,

Udzadya zimene manja ako adzagwirira ntchito,

Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta.

 

Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka,

M’kati mwa nyumba yako,

Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi,

Kuzungulira tebulo lako.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta.

 

Zoonadi, ndimo m’mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta,

Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse,

Uwone m’mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino,

Masiku onse a moyo wako.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 01 ATESALONIKA 05: 01 – 06 (Koma inu abale, simuli m’chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala).

 

Abale, za nthawi ndi nyengo yake yodzachitika zimenezi, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani. Inu nomwe mukudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye likazafika ngati mbala yausiku. Pamene anthu azikati, Pali mtendere, tili pabwino, pamenepo chiwonongeko chidzawagwera modzidzimutsa. Chidzawadzidzimutsa monga momwe zowawa zimamchitira mkazi pa nthawi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba. Koma inu abale, simuli m’chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala. Paja nonsenu zanu zonse ndi zam’kuwala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai. Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 15: 04a, 05b.

Alleluia, Alleluia – Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu, atero Ambuye. Munthu wokhala mwa Ine amabereka zipatso zambiri. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 25: 14 – 30 (Popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, bwera udzakondwere pamodzi ndi ine).

 

Yesu adawauza ophunzira ake fanizo ili: “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, nawasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziwiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziwiri uja, adapindula ndalama zinanso ziwiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. Patapita nthawi yaitali, mbuye wao uja adabwerako nawaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene

adaachita ndi ndalama zija. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziwiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziwiri. Onani, ndidapindula ziwiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti,

‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati,

‘Ambuye, ine ndinkadziwa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziwa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tsopano tikweze mitima yathu ndi mapemphero athu Kumwamba kuti mau a Ambuye agwire ntchito mwa ife ndi mwa anthu onse:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo alimbikire kutumikira anthu ao modziiwala ndi modzichepetsa, pogwiritsa ntchito mphatso zomwe Mulungu adawaninkha.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulamulira maiko asenze udindo wao mofatsa ndi molimba mtima, potsata ubwino wa anthu ao momwe Mulungu afunira.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Mabanja onse, eniake akhale a mtima umodzi pa ntchito zokometsera moyo wao, makamaka pa ntchito zolera bwino ana ao.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse tili muno tikhale anthu achangu pa ntchito zothandiza Mpingo wa Ambuye ndi pa ntchito zotukula moyo wa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, musaleke kutilimbitsa ndi Mzimu wanu Woyera, kuti ntchito zathu zonse zikhale zokutsirani ulemu ndi zokulitsa chikondi chanu m’mitima ya anthu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...