Saturday, November 4, 2023

LAMULUNGU LA 31 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 31 PA CHAKA – CHAKA A.

“Muli ndi Atate amodzi okha, ndiwo Atate anu a Kumwamba.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MALAKI; MALAKI 01: 14 – 02: 02. 08 – 10 (Koma inu ansembe mudasiya njira yanga. Mudaphunthwitsa anthu ambiri ndi zophunzitsa zanu).

 

Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine ndine Mfumu yaikulu, ndipo dzina langa nlochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu yonse. Tsono ansembe inu, lamulo ili nlokhalira inu. Mukapanda kundimvera, mukapanda kulemekeza dzina langa, ndidzakutembererani. Zabwino zimene mumazilandira nazonso ndidzazitemberera. Ndithu, ndazitemberera kale chifukwa simudamvere ndi mtima wonse. Koma inu ansembe mudasiya njira yanga. Mudaphunthwitsa anthu ambiri ndi zophunzitsa zanu. Mudaipitsa chipangano changa ndi Alevi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Nchifukwa chake Inenso ndakusandutsani onyozeka ndi achabechabe pamaso pa anthu, popeza kuti simudatsate njira zanga, ndipo mwakhala mukukondera poweruza milandu.” Kodi tonsefe suja tili ndi bambo mmodzi? Kodi suja adatilenga ndi Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tsono tikuphwanya chipangano cha Mulungu ndi makolo athu posamakhulupirirana?

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 131.

 

Ambuye, sungani mtima wanga mwa mtendere.

 

Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza,

Maso anga ndi osanyada,

Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.

 

Ambuye, sungani mtima wanga mwa mtendere.

 

Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga,

Monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere.

Momwemo mtima wanga uli phe m’kati mwanga.

 

Ambuye, sungani mtima wanga mwa mtendere.

 

Iwe Israele, khulupirira Chauta,

Kuyambira tsopano mpaka muyaya.

 

Ambuye, sungani mtima wanga mwa mtendere.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 01 ATESALONIKA 02: 07 – 09, 13 (Tidatsimikiza zogawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe).

 

Abale, tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe. Abale, simukumbukira nanga kuti tinkagwira ntchito kwambiri mpaka kutopa? Monse muja tinkakulalikirani Uthenga Wabwino wa Mulungu, tinkagwira ntchito zamanja usana ndi usiku, kuwopa kuti tingavutitse wina aliyense mwa inu. Pa mbali yathu, timathokoza Mulungu kosalekeza. Timatero chifukwa chakuti pamene mudamva mau a Mulungu amene tidakulalikirani, mudawalandira osati ngati mau a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mau a Mulungu. Mauwo ndi omwe akugwira ntchito mwa inu okhulupirira.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 23: 9b, 10b.

Alleluia, Alleluia – Muli ndi Atate amodzi okha, ndiwo Atate anu akumwamba. Mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 23: 01 – 12 (Sachita zimene amaphunzitsa).

 

Pa nthawi yomweyo, Yesu adalankhula ndi gulu la anthu ochuluka pamodzi ndi ophunzira ake. Adawauza kuti, “Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ali ndi udindo wotanthauzira malamulo a Mose. Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa. Iwo amamanga katundu wosautsa kunyamula nkusenzetsa anthu, koma iwowo samukhudzako mpang’ono pomwe. Zonse zimene amachita amangozichita kuti anthu awaone. Amadzimangirira timapukusi tikulutikulu ta mau a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono. Amatalikitsanso mphonje za zovala zao. Amakonda malo olemekezeka pa maphwando ndiponso mipando yaulemu kwambiri ku nyumba zamapemphero. Amakondanso kuti anthu aziwalonjera mwaulemu pa misika, ndipo kuti aziwatchula aphunzitsi. Koma inuyo anthu asati azikutchulani aphunzitsi, pakuti muli ndi

Mphunzitsi mmodzi yekha, ndipo nonsenu muli pa chibale. Musamatchulanso munthu pansi pano kuti atate, popeza kuti muli ndi atate amodzi okha, ndiwo Atate anu akumwamba. Anthu asatinso azikutchulani atsogoleri, popeza kuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu. Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pozindikira kuti tonse tili pachibale ndipo Yesu Mtsogoleri wathu waimirira pakati pathu, tiyeni tipempherere anthu onse:

 

1.     Ansembe ndi akulu onse a Mpingo asenze udindo wao mokhulupirika ndi modzichepetsa, pakutumikira anthu ao mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu onse nawonso ayesetse kutsogolera anthu anzao pa njira ya chipulumutso, pakuwaphunzitsa ndi kuwaonetsa mtima wachikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akhristu amene akhumudwa ndi zitsanzo zoipa za atsogoleri ao, asati ataye mtima, koma ayesetse kulangiza atsogoleriwo mwaubale.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse osonkhana pano, tileke mtima wamantha, kuti tiziweruzana ndi kumalangizana mwachifundo, pofuna kukometsa makhalidwe a Mpingo.
Tikupemphani, mutivomereze.


Atate, mutiwongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti tikutumikireni modzichepetsa polondola mapazi a Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...