CHAKA CHA YESU KHRISTU MFUMU – A.
LAMULUNGU LOMALIZA LA PA CHAKA
“Ufumu wa Yesu Khristu ndi wachikondi.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI EZEKIELE; EZEKIELE 34: 11 – 12, 15 – 17. (Kunena za inu, nkhosa zanganu, Ine Ambuye Chauta ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa).
Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala. Monga m’busa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthawi yamdima ndi yankhungu. Ineyo mwiniwake ndidzakhala m’busa wa nkhosa zanga. Ndipo Ine ndemwe ndizidzazipumulitsa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosa zanga mwachilungamo. Tsono kunena za inu, nkhosa zanganu, Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zamphongo ndi atonde.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 23: 01 – 03, 05 – 06.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Chauta ndiye m’busa wanga,
Sindidzasowa kanthu,
Amandigoneka pa busa lamsipu.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako,
Amatsitsimutsa moyo wanga,
Amanditsogolera m’njira za chilungamo,
Malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Inu mumandikonzera chakudya,
Adani anga akuwona,
Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta,
Mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu,
Zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga,
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu,
Moyo wanga wonse.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 01 AKORINTO 15: 20 – 26, 28. (Mwana wa Mulungu nayenso adzagonjera Mulungu, kuti Mulungu akhale wolamulira aliyense kwathunthu).
Abale, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka. Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina. Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu. Koma aliyense adzauka pa nthawi yake: woyambirira ndi Khristu, ndipo pambuyo pake, pamene Khristuyo adzabwera, nawonso amene ali ake adzauka. Pamenepo chimalizo chidzafika. Khristu atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse, adzapereka ufumu uja kwa Mulungu Atate. Paja Khristu ayenera kulamulira mpaka atagonjetsa adani ake onse. Mdani wotsiriza kumthetsa mphamvu, ndiye imfa. Koma pamene zonse zidzakhala zitagonjera Khristu, pamenepo Mwana wa Mulungu nayenso adzagonjera Mulungu, amene adamgonjetsera zinthu zonse. Adzachita zimenezi kuti Mulungu akhale wolamulira aliyense kwathunthu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 11: 09, 10.
Alleluia, Alleluia – Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye. Udalitsidwe Ufumu wa atate athu Davide umene ulikudza tsopano. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 25: 31 – 46. (Adzakhala pa mpando wake wachifumu ndipo adzawalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa monga momwe m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Nkhosa adzazikhazika ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku dzanja lake lamanzere. Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti,
‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Lowani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi. Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m’ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti
tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m’ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Mfumuyo idzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthawi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa
abale anga ngakhale otsika kwambiriwa, munkachitira Ine amene.’ Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake. Ine ndidaali ndi njala, inu osandipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu osandipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu osandilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu osandiveka. Ndinkadwala, ndidaalinso m’ndende, inu osadzandichezetsa.’ Apo nawonso adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, kapena muli ndi ludzu, kapena wamaliseche, ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m’ndende, ife osachitapo kanthu?’ Mfumuyo idzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti, nthawi iliyonse pamene munkakana kuthandiza wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriwa, munkakana kuthandiza Ine amene.’ Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.”
Mthenga wa Ambuye…...…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti ndife ake a Khristu, tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti Ufumu wao ukhazikike m’dziko lonse lapansi.
1. Akhristu onse akondane ndi kuika mtima pa ntchito zachifundo, aonetse anthu onse kudza kwa Ufumu wa Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Mafumu ndi akulu olamulira maiko alimbikire kukhazikika pa chilungamo, chimvano ndi mtendere pakati pa anthu ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu amene akusauka ndi njala, odwala, olumala, omangidwa, ndi onse amene akuvutika m’mitima mwao, apeze anzao achifundo owachitira zabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno tiwafewere mtima anzathu amene ali osowa, tiziwathandiza monga momwe tingathere osaopa kupereka moyo wathu womwe.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikutamanda chifundo chanu chofuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/