LAMULUNGU LA 28 PA CHAKA – CHAKA A.
“Mulungu amaitana anthu onse ku chikondwerero chosatha.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MPROFETI YESAYA; YESAYA 25: 06 – 10 (Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse
phwando ndipo adzapukuta misozi m’maso mwa aliyense).
Pa phiri ili la Ziyoni Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zokoma ndi la vinyo wabwino, phwando la nyama yonona ndi la vinyo amene wafikapo. Pa phiri limeneli adzachotsa chisoni chimene chaphimba anthu a mitundu yonse, chimene chakuta mafuko onse. Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m’maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta. Tsiku limenelo aliyense adzati, Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi. Chauta adzateteza phirili ndi dzanja lake.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 23.
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye, moyo wanga wonse.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu,
Amandigoneka pa busa lamsipu,
Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako,
Amatsitsimutsa moyo wanga,
Amanditsogolera m’njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye, moyo wanga wonse.
Ngakhale ndiyende m’chigwa chamdima wabii,
Sindidzaopa choipa chilichonse,
Pakuti Inu Ambuye mumakhala nane,
Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye, moyo wanga wonse.
Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona,
Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta,
Mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye, moyo wanga wonse.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu,
Zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga,
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu, Ambuye, moyo wanga wonse.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI; AFILIPI 04: 12 – 14, 19 – 20 (Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu).
Abale, kukhala wosauka ndimakudziwa, kukhala wolemera ndimakudziwanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoweratu. Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu. Komabe mudaachita bwino kundithandiza pa zovuta zanga. Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani
zonse zimene mukusowa. Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AEFESO 01: 17 – 18.
Alleluia, Alleluia – Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu akuunikireni m’mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 22: 01 – 14 (Mukaitane aliyense amene mukampeze, kuti abwere kuno ku phwando laukwati).
Yesu adalankhulanso ndi anthu aja m’mafanizo. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Mfumu ina idaakonzera mwana wake phwando laukwati. Idatuma antchito ake kuti akawauze anthu amene adaaitanidwa kuphwandoko kuti azibwera, anthuwo nkukana. Idatumanso antchito ena nkunena kuti, Kawauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng’ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati. Koma oitanidwawo sadalabadireko, adangopita ku zao: wina kumunda kwake, wina ku ntchito yake yamalonda. Enawo adagwira antchito a mfumu aja nawazunza, nkuwapha. Pamenepo mfumu idapsa mtima kwambiri, mwakuti idatuma ankhondo ake kuti akaononge opha anzao aja, ndi kutentha mudzi wao. Pambuyo pake idauza antchito ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzekatu, koma oitanidwa aja anali osayenera. Pitani tsono ku mphambano za miseu, mukaitane aliyense amene mukampeze, kuti abwere kuno ku phwando laukwati.’ Apo antchitowo adapitadi ku miseu nakasonkhanitsa onse amene adawapeza, abwino ndi oipa omwe, mwakuti nyumba yaphwando idadzaza ndi anthu. Pamene mfumu ija idalowa m’nyumbamo kukaona anthu odzadya phwando aja, idapezamo wina amene sadavale chovala chaukwati. Tsono idamufunsa kuti, ‘Kodi iwe, walowa bwanji muno opanda chovala chaukwati?’ Iye uja adangoti chete. Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, ‘Mmangeni manja ndi miyendo, mukamponye kunja ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.’” Tsono Yesu adati, “Inde oitanidwa ngambiri, komatu osankhidwa ngowerengeka.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti Mulungu ngwa chuma chochuluka ndipo mwa Yesu Khristu amatipatsa zonse zimene timasowa, tiyeni tipempherere anthu onse:
1. Akhristu onse avomere kuitanidwa kwao ndi kumavala makhalidwe oyenera pa moyo wao wa tsiku ndi tsiku poyembekezera tsiku lolowera m’nyumba yachaka.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Ayuda atsekule mitima yao ndi kuvomera Mthenga wa Yesu Khristu, ndipo choncho afikire ku chipulumutso cha Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu amafuko onse nawonso azindikire ndi kuvomera kuitanidwa kwao, mpaka alowe ndithu m’chikondwerero cha Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tili muno, tikhale oyera mtima posunga malonjezo a ubatizo wathu, kufikira tsiku limene Ambuye adzatitsekulira nyumba yachaka.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mwa chifundo chanu mverani mapemphero athuwa pamodzi ndi madandaulo a anthu onse; ndipo mutifikitse tonse ku chikondwerero chosatha. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:
Post a Comment