Saturday, October 7, 2023

LAMULUNGU LA 27 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 27 PA CHAKA – CHAKA A.

“Munda wa Ambuye ndife amene.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MPROFETI YESAYA; YESAYA 05: 01 – 07 (Tsonotu munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonse ndi dziko la Israele).

 

Ntamuimbirako bwenzi langa nyimbo yokamba za wokondedwa wanga ndi munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde. Adautipula nachotsa miyala yonse, ndipo adaokamo mipesa yabwino kwabasi. Adamanga nsanja pakati pa mundawo, nasema mopondera mphesa m’kati momwemo. Adaayembekeza kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ai, udabala mphesa zachabechabe. Ndiye wokondedwa wanga akuti, Inu amene mumakhala ku Yerusalemu, ndi inu anthu a ku Yuda, ndakupembani, taweruzani pakati pa ine ndi munda wanga wamphesawu. Kodi chilipo chinanso chimene ndidaayenera kuchitira munda wanga wamphesa, koma sindidachite? Pamene ndinkayembekeza kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji udabala mphesa zachabechabe? Tsopano taimani nkuuzeni zimene ndidzauchite munda wanga wamphesawo. Ndidzazula mpanda wake, ndipo mundawo udzaonongeka. Ndidzagwetsa chipupa chake, ndipo nyama zidzapondapondamo. Ndidzausandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira, ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pamundapo. Tsonotu munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonseyo ndi dziko la Israele, ndipo Ayuda ndiwo mipesa yake yokondweretsa. Iye ankayembekeza ntchito zabwino, koma adangoona kuphana. Ankayembekeza chilungamo, koma adangomva kulira kwa anthu

ozunzidwa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 80: 09. 12 – 16. 19 – 20.

 

Munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonse ndi dziko la Israele.

 

Mudatulutsa mpesa wanu Israele m’dziko la Ejipito,

Mudapirikitsa mitundu ina ya anthu kuti muubzale mpesawo,

Nthambizo zidafika mpaka ku nyanja yaikulu yakuzambwe,

Ndipo mphukira zake mpaka ku mtsinje waukulu wakuvuma.

 

Munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonse ndi dziko la Israele.

 

Nanga chifukwa chiyani mwagumula mpanda wake,

Kuti opita m’njira azithyola nawo zipatso zake?

Nguluwe zam’nkhalango zimauwononga,

Ndipo zonse zoyenda m’thengo zimaudya.

 

Munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonse ndi dziko la Israele.

 

Mutembenukirenso kwa ife, Inu Mulungu Wamphamvuzonse,

Muyang’ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone,

Samalani mpesawo, mtengo woyambirira,

Umene Inu mudaubzala ndi dzanja lanu lamanja.

 

Munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonse ndi dziko la Israele.

 

Tsono sitidzakusiyaninso, tipatseni moyo,

Ndipo tidzatama dzina lanu mopemba,

Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale,

Mutiwonetse nkhope yowala, kuti ife tipulumuke.

 

Munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonse ndi dziko la Israele.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI; AFILIPI 04: 06 – 09 (Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu).

 

Abale, musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma m’mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusowani, ndipo nthawi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu. Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu. Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 15: 16.

Alleluia, Alleluia – Ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa, atero Ambuye. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 21: 33 – 43 (Munda uja nkuubwereka alimi ena amene adzampatsa

zipatso zake pa nyengo yake).

 

Yesu adawauza akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda kuti: “Imvani fanizo lina. Munthu wina anali ndi munda wake. M’mundamo adaabzalamo mipesa, namanga mpanda kuzinga mundawo.

Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina. Nyengo yothyola zipatso itayandikira, munthu uja adatuma antchito ake kwa alimi aja, kuti akatengeko zipatso za m’munda muja. Koma alimiwo adawagwira antchito aja, wina kummenya, wina kumupha, wina kumponya miyala. Munthu uja adatumanso antchito ena, ochuluka koposa oyamba aja, ndipo alimi aja adawachita chimodzimodzi. Potsiriza pake adawatumira mwana wake, nanena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamchitira ulemu.’ Koma pamene alimiwo adaona mwana wakeyo, adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu? Tsono adamugwiradi, namuponya kunja kwa mundawo, nkumupha. Kodi mwini munda wamphesa uja akadzafika, adzawatani alimi aja?” Iwo adati, “Adzawapha mowazunza alimi oipawo, munda uja nkuubwereka alimi ena amene adzampatsa zipatso zake pa nyengo yake” Yesu adawafunsa kuti, “Kodi monga simudawerenge Malembo aja akuti, Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa. Ambuye ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri. Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakulandani Ufumu wake ndi kuupereka kwa anthu ena amene adzabala zipatso zoyenera.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, monga atilangizira Paulo Woyera, tisade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma tipemphe Mulungu zimene timazisowa, ndipo tipemphe ndi mtima woyamika:

 

1.     Tipempherere Eklezia amene ali ngati munda wa Ambuye, kuti anthu ake alimbikitse kuchita ntchito zabwino ndi kubala zipatso zokondweretsa Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere ansembe ndi atsogoleri a Mpingo kuti aonetse‚ changu pa ntchito zosamalira akhristu ao ndi zophunzitsira akatekumeni.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere mabanja achikhristu kuti eni ake akondane ndi kumagwirizana pa ntchito yolera bwino ana ao monga Mulungu afunira.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno tipemphererane kuti mau a Mulungu agwire ntchito mwa ife, ndipo moyo wathu ubale zipatso zokometsera Mpingo wa Ambuye.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikutula m’manja mwanu mapemphero athuwa pamodzi ndi zosowa za anthu onse, ndipo tikuyamika chifundo chanu chofuna kupulumutsa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...