Saturday, October 21, 2023

LAMULUNGU LA 29 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 29 PA CHAKA – CHAKA A.

“Perekani kwa Mulungu zake za Mulungu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MPROFETI YESAYA; YESAYA 45: 01, 04 – 06 (Chauta adamgwira Kirusi padzanja lamanja, kuti agonjetse mitundu ina ya anthu).

 

Chauta akulankhula ndi wodzozedwa wake Kirusi amene adamgwira dzanja lamanja, kuti agonjetse mitundu ina ya anthu, awathe mphamvu mafumu, ndi kutsekula zitseko kuti zipata zisatsekeke. Akunena kuti, “Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israele, ndikukuitana potchula dzina lako, ndikukupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziwa. Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziwa. Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziwe kuti palibe wina koma Ine ndekha.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 01, 03 – 05, 07 – 10.

 

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!

Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.

 

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

 

Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri,

Ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse,

Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe,

Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.

 

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

 

Tamandani, inu anthu a mitundu yonse,

Vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nzake.

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta,

Bwerani ndi zopereka, ndipo mulowe m’mabwalo a Nyumba yake.

 

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

 

Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera,

Njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi,

Uzani mitundu ya anthu kuti, ‘Chauta ndiye Mfumu,

Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.’

 

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 01 ATESALONIKA 01: 01 – 05 (Timakumbukira kosalekeza za chikhulupiriro chanu, chikondi chanu ndi chiyembekezo chanu).

 

Abale, ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Timathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m’mapemphero athu. Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m’mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m’mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m’mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu. Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziwa kuti Iye adakusankhani kuti mukhale ake. Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziwa m’mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 02: 15d, 16a.

Alleluia, Alleluia – Pakati pa anthu mumawala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi pakuwauza mau opatsa moyo. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 22: 15 – 21 (Perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu).

 

Nthawi ina Afarisi adakapangana zodzatapa Yesu m’kamwa. Adatuma ophunzira ao ena pamodzi ndi ena a m’chipani cha Herode kwa Yesu. Iwowa adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziwa kuti Inu mumanena zoona, mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Paja Inu simuyang’anira kuti uyu ndani. Ndiye timati mutiwuze zimene mukuganiza. Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?” Koma Yesu podziwa maganizo ao oipa, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala, anthu achiphamasonu? Tandiwonetsani ndalama yamsonkho.” Iwo adampatsadi ndalamayo. Pamenepo Iye adawafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adawauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pokumbukira kuti Ufumu wa Mulungu uyambirira pansi pano pomwe, m’mitima ya anthu, tiyeni tiwapempherere anthu onse:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo asaope kulankhula mau ndi kuteteza anthu ao pamene paoneka zina ndi zina zotsutsana ndi chilungamo, ufulu ndinso mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu a boma ndi akulu ena osenza maudindo osiyanasiyana, asenze udindo wao mokhulupirika ndi mosakondera potsata ubwino wa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akhristu onse adzipereke kwathunthu ku ntchito zotukula moyo wa anthu anzao, podziwa kuti pakutero alikudzetsa Ufumu wa Mulungu m’mitima mwao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse osonkhana pano, chikhristu chathu chiziwonekera poyera, osati lamulungu lokha, komanso m’zochita zathu za masiku onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mwa chifundo chanu mumvere mapemphero athuwa, ndipo mutiwongolere kuti ntchito zathu zonse zikhale zogwirizana ndi zimene mufuna Inu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...