LAMULUNGU LA 30 PA CHAKA – CHAKA A.
“Uzikonda mnzako, kusonyeza Mulungu kuti umamukondadi.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKSODO; EKSODO 22: 20 – 26 (Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamawazunza, Ine ndidzakukwiyirani).
Chauta adamuuza Mose kuti, “Muwauze ana a Israele kuti, ‘Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m’phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito. Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamawazunza, Ine ndidzawamva iwowo akamalira kwa Ine. Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye. Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphawi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja. Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuwa lisanalowe, poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo.’”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 18: 02 – 04, 47, 51.
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.
Chauta ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga,
Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathawirako,
Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.
Chauta ndi wamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wondipulumutsa
Mulungu amathandiza mfumu yake,
kuti izipambana nthawi ndi nthawi,
Amaonetsa chikondi chake kwa wodzozedwa wake.
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 01 ATESALONIKA 01: 05 – 10 (Mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu, kuti muzimtumikira: tsopano mukudikira Mwana wake).
Abale, Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziwa m’mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni. Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa chimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. Motero nanunso mudakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse a ku Masedoniya ndi a ku Akaiya. Inde kuchokera kwa inu mau a Ambuye adakafika ku Masedoniya ndi ku Akaiya, ndipo kuwonjezera apo mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu. Iwo amakamba okha za m’mene mudatilandirira, ndi za m’mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira. Tsopano mukudikira
Mwana wake kuti abwerenso kuchokera Kumwamba. Mwana wakeyo ndi Yesu, amene Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ulikudza.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 14: 23.
Alleluia, Alleluia – Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate
anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 22: 34 – 40 (Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndipo uzikonda mnzako
monga momwe umadzikondera iwe wemwe).
Afarisi atamva kuti Yesu adatsutsa Asaduki, adasonkhana. Tsono mmodzi mwa iwo, katswiri wa Malamulo adafunsa Yesu funso kuti amutape m’kamwa. Adati, “Aphunzitsi, kodi mwa malamulo onse a Mulungu, lalikulu ndi liti?” Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiwiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo awiriwa.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti Mulungu amakonda anthu kwambiri timupemphe kuti aike chikondi chake chomwecho m’mitima mwathu ndi mwa anthu onse:
1. Akhristu onse alimbikire kuchita ntchito zachifundo ndi kusonyeza chikondi choona kwa anthu anzawo.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atsogoleri a mipingo yachikhristu aongolere akhristu ao m’njira yachikondi, pokumbukira kuti ili ndi lamulo la Ambuye.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala, ovulala ndi onse amene akuvutika, apeze anzao achifundo owasamala ndi owalimbitsa mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse a m’Parishi yathu ino, kukondana kwathu kupite m’tsogolo kusonyeza kuti ndifedi abale ake a Yesu ndipo kuti Iye akukhaladi pakati pathu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, ife tazindikira chikondi chanu poona kuti Mwana wanu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Mudzaze mitima yathu ndi chikondi chanu chomwecho, nafenso tidziwe kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295