Saturday, September 16, 2023

LAMULUNGU LA 24 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 24 PA CHAKA – CHAKA A.

“Uzikhululukira anzako monga Mulungu amakukhululukira.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPHUNZITSI; MPHUNZITSI 27: 30 – 28: 07 (Ukakhululukira mnzako amene wakuchimwira, nawenso Ambuye ukawapempha adzakukhululukira machimo ako).

 

Mkwiyo ndi ukali, nazonso nzoipa zazikulu, munthu wochimwa amakhala nazo ziwiri zonsezo. Munthu wokonda kulipsira anzake, nayenso adzamulipsira Ambuye amene amawerenga machimo ake. Ukakhululukira mnzako amene wakuchimwira, nawenso Ambuye ukawapempha adzakukhululukira machimo ako. Ngati munthu asungira chiwembu mnzake angayembekeze bwanji kuti Ambuye adzamumvera chisoni? Ngati sachitira chifundo munthu mnzake, angapemphe bwanji Ambuye kuti amkhululukire machimo ake? Ngati amene ali munthu chabe asunga mkwiyo, osafuna kukhululukira mnzake, iyeyo ndani adzamkhululukira zolakwa zake? Kumbukira kutha kwa moyo wako, ndipo lekeratu chidani. Kumbukira kuti udzafa ndi kuwola, ndipo sunga Malamulo mokhulupirika. Ganiza za Malamulo ndipo usakwiyire mnzako. Kumbukira chipangano cha Wopambanazonse, ndipo ukhululukire mnzako.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 01 – 04, 09 – 12.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga.

 

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera,

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga.

 

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse.

Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda,

Amakuveka chikondi chake chosasinthika,

Ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga.

 

Chauta ndi wosakwiya msanga,

Akatikalipira, mkwiyo wake sudzakhala woyaka mpakampaka,

Satilanga moyenerera machimo athu,

Satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga.

 

Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,

Ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta.

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe,

Ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 14: 07 – 09 (Ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye).

 

Abale, palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha. Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye. Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 13: 34.

 

Alleluia, Alleluia – Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana; monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana, atero Ambuye.  – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 18: 21 – 35 (Kodi ndikuti kasanunkawiri kokha ngati, iyai, koma maka kasanunkawiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi awiri).

 

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi m’bale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanu nkawiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanu nkawiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanu nkawiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi awiri. Tsono Ufumu wakumwamba tingaufanizire motere: Panali mfumu ina imene idaaitanitsa antchito ake kuti iwonenso bwino ngongole zao. Atangoyamba kumene, adabwera ndi wantchito wina amene anali ndi ngongole ya ndalama zochuluka kwabasi. Ndiye popeza kuti adaasowa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe. Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’ Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite. Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi m’modzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa.

Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘bweza ngongole yako ija.’ Apo wantchito mnzake uja adadzigwetsa pansi ku mapazi ake nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani.’ Koma iye adakana, nakamponyetsa m’ndende kuti mpaka abweze ndithu ngongoleyo. Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo. Tsono mbuye wakeyo adamuitana namuuza kuti, ‘Wantchito woipa iwe, ine ndinakukhululukira ngongole yonse ija pamene unandidandaulira.

Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’ Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija. Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, popereka mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba, tiyeni tipempherere anthu onse ndi mtima umodzi:

 

1.     Akhristu onse atsimikize kuti ndiwodi ake a Yesu Khristu pokhala nawo mtima wodziwa kukhululuka nthawi zonse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu amene akusowa mtendere m’mabanja mwao, ayesetse kuyanjana ndi kukhulupirirana, pokumbukira chifundo cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu amene akusunga udani kapena mkwiyo m’mitima mwao, azindikire kulakwa kwao ndipo akhululukire anzao mwaubale.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ifenso amene tili muno tipemphererane kuti tikhale oyanjana ndi anthu onse ngakhale iwo atinyoze ndi kutichimwira chotani.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, Inu mumatikhululukira kosalekeza, mutithandize kuwonetsa anzathu mtima womwewo, pakuwachitira chifundo, kuti tifanane ndi Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...