“Kani chifundo cha Mulungu nchotero?”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MPROFETI YESAYA; YESAYA 55: 06 – 09 (Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi).
Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo awachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye awakhululukire machimo ao mofewa mtima. Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 145: 02 – 03, 08 – 09, 17 – 18.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga,
Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse mpaka muyaya,
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri,
Ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
Wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika,
Chauta ndi wabwino kwa onse,
Amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba.
Chauta ndi wolungama m’zochita zake zonse,
Ndi wachifundo pa zonse zimene achita,
Chauta ali pafupi ndi onse,
Amene amamutama mopemba.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI; AFILIPI 01: 20 – 24, 27 (Kwa inetu moyo ndi Khristu amene).
Abale, motero ndikuyembekeza ndi kukhulupirira ndi mtima wonse kuti sipadzakhala konse manyazi. Koma ndikuyembekeza kuti ndidzalimba mtima kulankhula poyera, kuti tsopanonso, monga nthawi zonse, Khristu alemekezedwe mwa ine, ngakhale ndikhale moyo, kapena ndimwalire. Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu. Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziwa kaya ndingasankhe chiti. Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa. Koma kwinakunso nkofunika kwambiri kuti ndikhale moyo chifukwa cha inuyo. Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Cf. AKORINTO 16: 14b.
Alleluia, Alleluia – Ambuye tsekulani mitima yathu kuti mau a Mwana wanu akhale mwa ife. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 20:1-16 (Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalawirira m’mamawa kukalemba anthu okagwira ntchito m’munda wake wamphesa.
Adaapangana nawo kuti adzawalipira ndalama imodzi yasiliva pa tsiku, nawatuma kumunda kwake. Pa nthawi ya 9 koloko adapitanso, nakapeza ena atangokhala khale pa msika, osagwira ntchito. Adawauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa, ndidzakulipirani moyenerera.’ Iwowo adapitadi. Munthu uja adapitanso pa 12 koloko masana ndi pa 3 koloko, nakachita chimodzimodzi. Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adawafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ Iwowo adayankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba.’ Iye uja adawauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa.’ Dzuwa likulowa, mwinimunda uja adauza kapitao wake kuti, ‘Kawaitane antchito aja, uwalipire. Uyambire amene alembedwa potsirizawo, utsirizire oyamba aja.’ Pamene adabwera olembedwa pa 5 koloko yamadzulo aja, aliyense adalandira ndalama imodzi. Tsono pamene olembedwa poyamba aja adabwera, ankaganiza kuti alandira pakulu. Koma nawonso adangolandira aliyense ndalama imodzi. Ndiye iwowo polandira, adayamba kuwiringula, adati, ‘Aa! Anzathu otsirizirawa angogwira ntchito kanthawi pang’ono, bwanji mwawapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuwa chonse chija?’ Koma mwinimunda uja adayankha mmodzi mwa iwo kuti, ‘Iwe, inetu sindidakubere ai. Kodi suja tinapangana ndalama yasiliva imodzi? Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe. Kodi zinthu zanga ndisachite nazo monga ndifunira? Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?”’ Tsono Yesu adati, “Choncho amene ali oyambirira adzakhala otsirizira. Ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mulungu watitsimikizira chifundo chake chofuna kupulumutsa anthu onse. Tiyeni tipemphere mogwirizana ndi mosakayika:
1. Atsogoleri a Mpingo alondoloze anthu awo m’njira yachikondi, pakuwasamala osauka ndi ena osowa chithandizo.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamulira maiko akhale otekeseka ndi ubwino wa anthu ao poteteza ufulu wao ndi kutsata chilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala ndi ena onse amene akumva zowawa m’mitima mwao, alandire chisamaliro ndi chisangalalo kuchokera kwa anthu anzao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno tilimbikire kuchita zachifundo modziwala ndi mopanda tsankho, monga momwe Mulungu amakondera anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tili kuyamika ufulu wanu chifukwa mumasamala anthu onse ndipo mumatichitira zabwino koposa m’mene tingayembekezere. Mwa Yesu Khristu Ambuye anthu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment