LAMULUNGU LA 23 PA CHAKA – CHAKA A.
“M’bale wako akachimwa, mumdzudzule.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MPROFETI EZEKIELE; EZEKIELE 33: 07 – 09 (Ukapanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake).
Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda wa Aisraele. Ukamva mau anga, uwachenjeze. Ndikauza munthu woipa kuti, Munthu woipa iwe, udzafa, iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkupitiriza makhalidwe ake oipawo, adzafa ali wochimwa, koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95: 01 – 02, 06 – 09.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Bwerani, timuimbire Chauta,
Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa,
Tiyeni, tikafike pamaso pake,
Tikamthokoze, timuimbire nyimbo zotamanda.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira,
Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake,
Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Lero mukadamverako mau ake!
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,
Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,
Pamene makolo anu adandiputa mondiyesa ngakhale anali ataona ntchito zanga.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 13: 08 – 10 (Amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene
Malamulo a Mulungu akunena).
Abale, musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Pajatu malamulo amene amati, ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire,’ ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m’lamulo ili lakuti, ‘Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.’ Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 02 AKORINTO 05: 19.
Alleluia, Alleluia – Mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiwalalike. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 18: 15 – 20 (Mbale wako akakumvera, wamkonza mbale wakoyo).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli awiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena awiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziwiri kapena zitatu. Akapanda kuwamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho. Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.
Ndikunenetsanso kuti awiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Pajatu pamene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, podziwa kuti Yesu Khristu ali nafe pompano, tiyeni, pamodzi naye, tikweze mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba.
1. Ansembe ndi atsogoleri onse a Mpingo aonetse anthu ao mtima wachifundo pokonza milandu yao ndi powalangiza mofatsa ndi modzichepetsa.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu onse akhale otekeseka ndi chipulumutso cha anthu anzawo powaongolera m’njira ya ungwiro ndi yachikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akhristu otaika ndi ena onse amene ali pa milandu apeze njira yoyanjananso ndi Mulungu polandira malangizo abwino kuchokera kwa anthu anzawo.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno, mau athu ndi mayendedwe athu abweretse umodzi ndi chiyanjano pakati pa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mumvere mapemphero athuwa ndi kulunzitsa anthu onse M’chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment