“Wofuna kutsata Ine adzamva zowawa.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI YEREMIYA; YEREMIYA 20: 07 – 09 (Mau anu, Inu Chauta, andisandutsa wonyozeka ndi wonyodoledwa masiku onse).
Inu Chauta, mwandipusitsa ine, ndipo ndapusadi. Inu ndinu amphamvu kuposa ine, ndipo mwandipambana. Aliyense akundiseka tsiku lonse, aliyense akundinyodola kosalekeza.
Ndikamalankhula, ndimakweza mau, ndimafuula kuti, “Ndeu kuno, taonongeka!” Mau anu, Inu Chauta, andisandutsa wonyozeka ndi wonyodoledwa masiku onse. Ndikanena kuti, “Sindidzalalikanso za Chauta, sindidzalankhulanso m’dzina lake,” mau anu Inu Chauta, amayaka ngati moto mumtima mwanga. Ndimayesa kuwasunga m’kati, koma pambuyo pake ndimawatulutsa popeza kuti sindingathe kupirira.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 63: 02 – 06, 08 – 09.
Mtima wanga uli ndi ludzu la Inu, Ambuye.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani,
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu,
Thupi langa likulakalaka Inu,
Ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Mtima wanga uli ndi ludzu la Inu, Ambuye.
Ndikukhumbira kukuwonani m’malo anu oyera kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu,
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu chabwino kupambana moyo.
Mtima wanga uli ndi ludzu la Inu, Ambuye.
Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera,
Mudzandikhutitsa ndi zonona,
Ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala.
Mtima wanga uli ndi ludzu la Inu, Ambuye.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 12: 01 – 02 (Mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo).
Abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu.
Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziwa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AEFESO 01: 17 – 18.
Alleluia, Alleluia – Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu akuunikireni m’mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 16: 21 – 27 (Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo).
Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kudziwitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.” Apo Petro adamtengera pambali nayamba kumdzudzula. Adati, “Pepani Ambuye, zisatero ai. Mulungu asalole zimenezi.” Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akowa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.” Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, poganiza za zowawa zonse zimene anthu akuzimva m’dziko lino lapansi, tiyeni tipereke zonsezi, pamodzi ndi mapemphero athu, kwa Mulungu Mwini:
1. Atate, mulimbitse mtima atsogoleri a Mpingo, kuti asaope kumva zowawa ndi kutaya moyo wao womwe chifukwa cha akhristu ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, muthandize akhristu amene akuzunzidwa chifukwa chokhulupirira Mthenga Wabwino, kuti alimbe mtima podziwa kuti Ufumu wa Kumwamba ndi wao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, mudalitse anthu odwala ndi onse omva zowawa m’mitima mwao, kuti apeze mphamvu zopirira mavuto ao pokumbukira imfa ya Ambuye Yesu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mutidalitse ife tonse tili muno, kuti ntchito zathu zotumikira anzathu zitithandize kuiwala zowawa zathu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, okoma mtima, landirani mapemphero athuwa pamodzi ndi nkhawa ndi zowawa za anthu onse, zisanduke nsembe yangwiro ndi yokukondweretsani. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment