LAMULUNGU LA 26 PA CHAKA – CHAKA A.
“Tisamangoti ‘Ambuye, Ambuye!’”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MPROFETI EZEKIELE; EZEKIELE 18: 25 – 28 (Munthu woipa akaleka zoipa zake, adzakhala ndi moyo, sadzafa).
Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti: “Inu mumati, ‘A! Zimene Ambuye amachitazi nzopanda chilungamo.’ Tamvani tsono Aisraele inu: Kani zochita zanga ndiye zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene zili zosalungama? Ngati munthu wabwino aleka kuchita zoyenera, namachita zoipa, adzafa chifukwa cha zoipa zakezo. Komanso munthu woipa akaleka zoipa zake, namachita zoyenera, adzapulumutsa moyo wake. Poti adazindikira kuipa kwa zolakwa zake, nazileka, ndiye kuti adzakhala ndi moyo, sadzafa.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 25: 04 – 09.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu.
Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta,
Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu,
Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza,
Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika,
Chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale,
Musakumbukire machimo a unyamata wanga,
Koma mundikomere mtima, Inu Chauta,
Chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu.
Chauta ndi wabwino ndi wolungama,
Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake,
Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,
Amawaphunzitsa njira zake.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI; AFILIPI 02: 01 – 11 (Nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu).
Abale, mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhawa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi. Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu. Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu: Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphawi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza. Zonse zidzavomereze poyera kuti, Yesu Khristu ndi Ambuye, ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 10: 27.
Alleluia, Alleluia – Nkhosa zanga zimamva mau anga, atero Ambuye. Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsatira. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 21: 28 – 32 (Okhometsa msonkho ndi akazi adama akulowa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m’mbuyo).
Yesu adawauza akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda kuti: “Kodi inu, mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Adapita kwa woyamba, nakamuuza kuti, ‘Mwana wanga, pita ukagwire ntchito m’munda wamphesa lero.’ Iyeyo adati, ‘Toto ine.’ Koma pambuyo pake adasintha maganizo, napitadi. Bambo uja adapita kwa mwana wina uja, nakamuuza mau omwe aja. Iyeyo adati, ‘Chabwino atate,’ koma sadapite. Kodi mwa awiriwo, yemwe adachita zimene bambo wake ankafuna ndi uti?” Iwo adati, “Woyamba uja.” Yesu adawauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti okhometsa msonkho ndi akazi adama akulowa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m’mbuyo. Paja Yohane Mbatizi adaabwera nadzakuwonetsani njira ya chilungamo, inu osamkhulupirira, m’menemo okhometsa msonkho ndi akazi adama adamkhulupirira. Inuyo ngakhale mudaziwona zimenezo, simudasinthe maganizo pambuyo pake kuti muzimkhulupirira.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti patokha timangofooka, tiyeni tikweze mitima yathu kumwamba kuti Mulungu atiwonjezere mphamvu ndi kuchirikiza anthu onse m’njira ya chipulumutso:
1. Apapa, Aepiskopi ndi ansembe onse, atsogolere akhristu ao m’njira yaungwiro, pakuwaphunzitsa za kulapa ndi za kutsanzira Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu amuna ndi akazi a m’zipani zamumpingo, alimbikire kusunga malonjezo ao ndi kuwonetsa anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu ofooka ndi okayikira alandire chithandizo kuchokera kwa akhristu anzao ndipo ayambe moyo watsopano wa kuyanjana ndi Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno tipitirize kuwongola makhalidwe athu ndi kukomera Mulungu ndi anthu omwe, potsanzira Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mverani mapemphero athuwa ndipo mutilimbitse, kuti tiyende mokhulupirika m’njira ya malamulo anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/