Saturday, August 12, 2023

LAMULUNGU LA 19 PA CHAKA – CHAKA A.

LAMULUNGU LA 19 PA CHAKA – CHAKA A.

“Adakapemphera ali yekhayekha.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LOYAMBA LA MAFUMU; 01 MAFUMU 19: 09, 11 – 13 (Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga).

 

Eliya adayenda mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu. Kumeneko adafikira m’phanga, nagona momwemo. Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning’amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m’mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m’chivomezimo. Chitapita chivomezi chija, padafika moto, koma Chauta sanali m’motomo. Utapita motowo, padamveka kamphepo kongoti wii. Eliya atakamva, adafunda kumutu, ndipo adatuluka, nakaima pa khomo la phanga.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 85: 09 – 14.

 

Tiwone chifundo chanu, Ambuye, ndipo mutipulumutse ife ku zoipa.

 

Ndimve zimene Chauta adzalankhula,

Chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake,

Kuti apulumutse amene amamuwopa,

Kuti ulemerero wake ukhale m’dziko lathu.

 

Tiwone chifundo chanu, Ambuye, ndipo mutipulumutse ife ku zoipa.

 

Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana,

Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana,

Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano,

Ndipo Mulungu wakumwamba adzawalungamitsa.

 

Tiwone chifundo chanu, Ambuye, ndipo mutipulumutse ife ku zoipa.

 

Inde, Chauta adzapereka zabwino,

Ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri,

Mulungu ndi wolungama chikhalire,

Chilungamo chake chimaongolera zochita zake zonse.

 

Tiwone chifundo chanu, Ambuye, ndipo mutipulumutse ife ku zoipa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 09: 01 – 05 (Chifukwa cha abale anga, ndikadakonda kuti m’malo mwao, ineyo ndikhale wotembereredwa).

Abale, ndithudi ndikunena zoona ine amene ndili wake wa Khristu, ndipo sindikunama ai. Mtima wanga, umene Mzimu Woyera amautsogolera, ukundichitira umboni kuti ndili ndi chisoni chachikulu. Ndipo ukundipweteka kosalekeza chifukwa cha abale anga, anthu a mtundu wangawa. Ndikadakonda kuti m’malo mwao, ineyo ndikhale wotembereredwa, osakhalanso wake wa Khristu. Iwowa ndi Aisraele, amene Mulungu adawasankha kuti akhale ana ake, ndipo adawapatsa ulemerero. Mulungu adachita nawo mapangano, ndipo adawapatsa

Malamulo ake. Adawaphunzitsa mwambo wachipembedzo, ndipo adawapatsa malonjezo ake. Iwowa ndi zidzukulu za makolo athu akale aja, ndipo Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi wa mtundu wao, kunena za umunthu wake. Mulungu amene amalamulira zonse, alemekezeke mpaka muyaya. Amen.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 130: 05.

 

Alleluia, Alleluia – Ndimayembekeza ndi mtima wonse chithandizo cha Ambuye,

ndipo ndimakhulupirira mau ake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 14: 22 – 33 (“Tandiwuzani kuti ndibwere kwa Inu pamadzipo.”)

 

Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti alowe m’chombo, atsogole kupita ku tsidya, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao. Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri yekha kukapemphera. M’mene kunkayamba kuda, nkuti ali komweko yekhayekha. Pamenepo nkuti chombo chija chili kutalitali ndi mtunda, chikuvutika ndi mafunde, chifukwa chinali chitayang’anana ndi mphepo. M’mamawa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo Iye akuyenda pa madzi. Pamene ophunzira aja adamuwona akuyenda pa madzi, adaopsedwa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo adayamba kukuwa chifukwa cha mantha. Koma nthawi yomweyo Yesu adawauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine; musaope.” Apo Petro adati, “Ambuye, ngati ndinudi, tandiwuzani kuti ndibwere kwa Inu pamadzipo.” Yesu adati, “Chabwino, bwera.” Tsono Petro adatuluka m’chombo nayamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu. Koma ataona m’mene ikuwombera mphepo, adachita mantha, nkuyamba kumira. Tsono adafuula kuti, “Ambuye, pulumutseni!” Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?” Pambuyo pake awiriwo adalowa m’chombo muja, mphepo nkuleka. Apo amene anali m’chombo aja adamgwadira Yesu nati, “Ndithudi, ndinu Mwana wa Mulungu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

 

Abale, lero Mulungu watiwonetsanso chifundo chake chofuna kupulumutsa anthu onse. Tiyeni titule m’manja mwake mapemphero athu:

 

1.     Ansembe ndi atsogoleri onse apitirize ntchito yao molimbika, pokhala okonda kupemphera.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Ayuda, Mulungu awalitse nkhope yake pa iwo, kuti nawonso avomere Mpulumutsi wa anthu onse, Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu onse amene ali paulendo, Mulungu awatsogolere ndi kuwateteza, mpaka akafike bwino kumene alikulinga.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife amene timakhala otanganidwa ndi ntchito zosiyanasiyana, tidziwe kucheza ndi Ambuye masiku onse, timange moyo wathu pa chikondi chao.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani kuti simulephera kumvera madandaulo athu. Mulimbitse chikhulupiriro chathu, mutipatse mtima wokonda kucheza nanu masiku onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A [Gaudete Sunday] “Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.”   MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’N...