LAMULUNGU LA 20 PA CHAKA – CHAKA A.
“Chikhulupiriro chako nchachikulu ndithu.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 56: 01, 06 – 07 (Ndidzabweretsa akunja onse ku phiri langa lopatulika).
Chauta akuuza anthu ake kuti, “Muzichita zabwino ndi zolungama, chifukwa ndikuwombolani posachedwa, chipulumutso changa chiwoneka.” Chauta akutinso, “Akunja amene amaphatikana ndi Chauta mpaka kumgwirira ntchito, kumkonda, ndi kumtumikira, amenenso amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, nasunga bwino chipangano changa, Ine ndidzawafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzawapatsa chimwemwe m’nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 02 – 03, 05 – 06, 08.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,
Mutiwunikire ndi chikondi chanu,
Njira yanu idziwike pa dziko lonse lapansi,
chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,
Chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo,
Ndi kuwatsogolera pa dziko lapansi.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,
Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni,
Inde, Mulungu watidalitsa,
Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 11: 13 – 15, 29 – 32 (Mulungu sasinthanso ataitana munthu ndi kumpatsa mphatso).
Abale, tsopano ndifuna kukuuzani kanthu, inu amene simuli Ayuda. Malinga nkuti ndine wotumidwa kwa anthu a mitundu ina, ndimaunyadira utumiki wanga umenewu. Koma ndimakhumba kuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena mwa iwo. Ngati anthu a pa dziko lonse lapansi adayanjanitsidwa ndi Mulungu chifukwa Iye adawaika pambali Ayuda, nanga kudzatani Iye akadzawalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka! Pakuti Mulungu sasinthanso ataitana munthu ndi kumpatsa mphatso. Kale inu a mitundu ina simunkamvera Mulungu, koma tsopano Mulungu akukuchitirani chifundo chifukwa cha kusamvera kwa Ayuda. Momwemonso Ayuda tsopano samvera Mulungu, koma cholinga chake nchakuti iwonso adzalandire chifundo pa nthawi yake, chifukwa cha chifundo mwalandira inuchi. Mulungu adasandutsa anthu onse akaidi a kusamvera, kuti Iye athe kuchitira onse chifundo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO
Alleluia, Alleluia – Yesu adalalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 15: 21 – 28 (Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu).
Yesu adachoka kumeneko, napita ku madera a ku Tiro ndi Sidoni. Mai wina wachikanani, wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.” Koma Yesu sadamuyankhe mau ndi amodzi omwe. Ophunzira ake adadza nampempha kuti, “Muuzeni azipita, onani akubwera natisokosera.” Yesu adati, “Inetu Mulungu adandituma kwa amene ali ngati nkhosa zotayika pa mtundu wa Aisraele.” Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.” Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.” Maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amadyako nyenyeswa zimene zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la mbuye ao?” Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti Yesu Khristu adadzaitana anthu a mitundu yonse, tiyeni tiwapempherere kuti Mulungu awaunikire ndi kuwafikitsa ku chikhulupiriro choona:
1. Eklezia, Mpingo wa Yesu Khristu, alimbikire pa ntchito yake yofalitsa Mthenga Wabwino mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu a mipingo yosiyanasiyana aleke kutsutsana kopanda phindu ndipo aphunzire kudziwana, kukondana ndi kulemekezana.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu amene adakali padera adziwe kukhulupirira Mulungu ndi kupemphera, maka adzazindikire kuwala kwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe osonkhana pano tizitekeseka ndi chipulumutso cha anthu onse, pakuwapempherera ndi kuwathandiza m’mavuto ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikuyamika chifundo chanu chofuna kusonkhanitsa anthu onse mu Ufumu wanu waulemerero. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:
Post a Comment