Saturday, August 5, 2023

CHAKA CHA KUSANDULIKA KWA AMBUYE YESU – CHAKA A. [TRANSFIGURATION OF THE LORD]

CHAKA CHA KUSANDULIKA KWA AMBUYE YESU – CHAKA A.

[TRANSFIGURATION OF THE LORD]

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI DANIELE; DANIELE 07: 09 – 10, 13 – 14 (Zovala zake zinali zambee ngati chipale).

 

Ine ndikuyang’ana, ndidaona mipando yaufumu ikuikidwa pa malowo, ndipo Mkulu amene analipo chikhalire adakhala pa mpando umodzi. Zovala zake zinali zambee ngati chipale, ndipo tsitsi lake linali loyera ngati ubweya wa nkhosa. Mpando wake unali wonga wa malawi a moto, mikombero yake ngati moto woyaka. Mtsinje wa moto udatuluka nkumayenda patsogolo pake. Panali chinamtindi cha anthu omtumikira, panalinso chinamtindi china chochuluka kupambana chinacho. Chimenechi chidaima pamaso pake. Tsono bwalo lidayamba kuweruza, ndipo mabuku adatsekulidwa. Pamene ndinkaonabe zinthu m’masomphenya usiku, ndidaona wina ngati mwana wa munthu akutsika ndi mitambo yakumwamba. Atayandikira Mkulu amene analipo chikhalire uja, ena adamperekeza kwa Mkuluyo. Pamenepo adampatsa ulamuliro, ulemerero ndi ufumu, kuti anthu a mitundu yonse, a mafuko onse ndi a zilankhulo zosiyanasiyana azimtumikira. Ulamuliro wake ndi wamuyaya, sudzatha. Ufumu wake ndi wosagawikana, ndipo sudzaonongedwa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 97: 01 – 02, 05 – 06, 09.

 

Chauta ndiye Mfumu, Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi.

 

Chauta ndiye Mfumu,

Anthu a pa dziko lapansi akondwere,

Anthu onse a m’mbali mwa nyanja asangalale.

 

Chauta ndiye Mfumu, Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi.

 

Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta,

Amalamulira molungama,

Mu ufumu wake mulibe tsankho.

 

Chauta ndiye Mfumu, Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi.

 

Mapiri amasungunuka ngati sera pamaso pa Chauta,

Ndiye wolamulira dziko lonse lapansi,

Zakumwamba zimalalika za kulungama kwake,

Ndipo anthu a mitundu yonse amaona ulemerero wake.

 

Chauta ndiye Mfumu, Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi.

 

Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse,

Wolamulira dziko lonse lapansi,

Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse.

 

Chauta ndiye Mfumu, Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PETRO WOYERA; 02 PETRO 01: 16 – 19 (Mau amenewa ifeyo tidawamva kuchokera kumwamba).

 

Abale, ife sitidatsate nthano zongopeka chabe, pamene tidakudziwitsani za mphamvu zao ndi za kubweranso kwao kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Koma tidachita kuwona ndi maso athu ukulu wake. Iye adalandira ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu Atate, ndipo adamufikira mau ochokera kwa Atate aulemererowo akuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” Ndipo mau amenewa ifeyo tidawamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija. Motero tikudziwa ndithu tsopano kuti mau aja a aneneriwa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muwayang’anitsitse ngati nyale yowala m’malo amdima, kufikira nthawi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam’mamawa idzayambe kuwala m’mitima mwanu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 17: 05c.

 

Alleluia, Alleluia – Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 17: 01 – 09 (Nkhope yake idawala ngati dzuwa).

 

Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, mbale wa Yakobo yo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Nkhope yake idawala ngati dzuwa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthawi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye. Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Akulankhula choncho, kudadza mtambo wowala nuwaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” Ophunzira aja atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri nadzigwetsa chafufumimba. Koma Yesu adabwera, nawakhudza nkunena kuti, “Dzukani, musachite mantha.” Iwo aja poweramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adawalamula kuti, “Zimene mwaona m’masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENT—A [Gaudete Sunday] “Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.”   MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’N...