Saturday, July 29, 2023

LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – CHAKA A.

“Chuma changa ndiye Mulungu Mwini.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LOYAMBA LA MAFUMU; 01 MAFUMU 03: 05, 07 – 12 (Wapempha nzeru zolamulira anthu bwino).

 

Ku Gibiyoniko Chauta adamuwonekera Solomoni m’maloto usiku, namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse. Solomoni adati, “Inu Chauta Mulungu wanga, mwaika mtumiki wanune pa malo a Davide bambo wanga, ngakhale ndine mwana wamng’ono chabe, ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yanga. Tsono ine mtumiki wanu ndikukhala pakati pa anthu amene mudawasankha, mtundu waukulu, anthu ake ochuluka, oti nkosatheka kuwawerenga. Nchifukwa chake mundipatse mtumiki wanune nzeru zolamulira anthu anu, kuti ndizidziwa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu chotere wa anthu anu?” Zidawakomera Ambuye kuti Solomoni adapempha zimenezi. Tsono Mulungu adauza Solomoni kuti, “Chifukwa chakuti wapempha zimenezi, osapempha moyo wautali kapena chuma kapena imfa ya adani ako, koma nzeru zolamulira anthu bwino, ndiye Ine ndikuchitira zimene wapempha. Zoona, ndikupatsa mtima wanzeru ndi waluntha, kotero kuti sadaonekepo kale lonse wina wofanafana nawe, ndipo sadzaonekanso wina wolingana nawe, iweyo utafa.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 119: 57, 72, 76 – 77.

 

Ambuye, ndimakonda malamulo anu.

 

Inu Chauta, ndikulonjeza kumvera mau anu,

Malamulo a pakamwa panu amandikomera,

Kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.

 

Ambuye, ndimakonda malamulo anu.

 

Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu,

Monga momwe mudalonjezera,

Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo,

Pakuti malamulo anu amandikondwetsa.

 

Ambuye, ndimakonda malamulo anu.

 

Koma ine ndimasamala malamulo anu,

Kupambana golide, golide wosungunula bwino,

Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga,

Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.

 

Ambuye, ndimakonda malamulo anu.

 

Malamulo anu ndi abwino,

Nchifukwa chake ndimawatsata ndi mtima wanga wonse,

Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuwala,

Kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

 

Ambuye, ndimakonda malamulo anu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 08: 28 – 30 (Mulungu adawapatulanso kale kuti akhale monga Mwana wake).

 

Abale, tikudziwa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziwakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amawaitana monga momwe Iye adazikonzera. Pakuti anthu amene Mulungu adawasankhiratu, Iye adawapatulanso kale kuti akhale monga Mwana wake, kuti choncho Mwanayo akhale woyamba mwa abale ambiri. Mulungu sadangowapatula, komanso adawaitana. Sadangowaitana, komanso adawaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adawagawirako ulemerero wake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 11: 25.

 

Alleluia, Alleluia – Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 13: 44 – 52 (Amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda).

 

Yesu adauza khamu la anthu kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja. Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati munthu wamalonda wonka nafunafuna ngale zokongola zamtengowapatali. Atapeza ngale imodzi yamtengowapatali kwambiri, amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula ngale ija. Ufumu wakumwamba ulinso ngati khoka limene anthu amaliponya m’nyanja, ndipo limagwira nsomba za mitundu yonse. Likadzaza, anthu amalikokera ku mtunda. Tsono amakhala pansi, nsomba zabwino nkumaziika m’madengu, zachabe nkumangozitaya. Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama, nkumawaponya m’ng’anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.” Yesu adawafunsa anthu aja kuti, “Mwazimvetsa zonsezi kodi?” Iwo adati, “Inde.” Apo Iye adawauza kuti, “Nchifukwa chaketu mphunzitsi aliyense wa Malamulo, amene adaphunzira za Ufumu wakumwamba, ali ngati mwinibanja amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zinthu zakale m’nkhokwe ya chuma chake.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale monga mfumu Solomoni uja, ifenso popempherera anthu onse tipemphe nzeru yozindikira zokoma zimene Mulungu adatikonzera mu Ufumu wake:

 

1.     Ansembe ndi akulu a Mpingo, aonetse anthu onse chifundo cha Mulungu chofuna kuwagawirako moyo wake ndi chikondi chake.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu amene maganizo ao angoima pa zinthu za pansi pano, maso ao atsekuke ndipo mitima yao ikopedwe ndi zinthu zakumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Achinyamata amene Mulungu awaitana ku ntchito yake, avomere kuitanako ndi mtima wonse, pozindikira kukoma kwa Ufumu wa Kumwamba.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse tili muno, titsate molimbika malamulo onse a Ambuye‚ podziwa kuti chikondi cha Mulungu ndi chuma cha mtengowapatali chotipatsa moyo wosatha.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, mverani mapemphero athuwa ndipo mutikhazikitse m’chikondi chanu, popeza kuti Inu nomwe mudzakhala mphotho yathu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...