LAMULUNGU LA 16 PA CHAKA – CHAKA A.
“Inu, Ambuye, ndinu wachifundo ndi woleza mtima.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA LUNTHA; LUNTHA 12: 13, 16 – 19 (Mumakhululukira anthu ochimwa).
Pajatu Mulungu ndinu nokha, palibenso wina. Ndinu nokha amene mumasamala anthu onse. Palibenso wina amene muyenera kumufotokozera ngati chigamulo chanu ndi cholungama.
Mphamvu zanu ndiye gwero la chilungamo chanu, choncho popeza kuti ndinu mwini anthu onse, mumawachitira chifundo onse. Anthu amene amakayika kuti ndinu Mulungu Wamphamvuzonse,
mumawaonetsa mphamvu zanu. Anthu amene amadziwa zimenezi nkukuchitanibe chipongwe, mumawachititsa manyazi. Koma ngakhale ndinu mwini mphamvu, mumawaweruza mofatsa. Mumatilamula ndi mtima wachifundo, poti mukangofuna, mumaonetsa mphamvu zanu. Pochita ntchito zanu zoterezi, mudaphunzitsa anthu anu kuti wolungama ayenera kukhala wachifundo, mudadzaza ana anu ndi chikhulupiriro, chifukwa mumakhululukira anthu ochimwa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 86: 05 – 06, 09 – 10, 15 – 16.
Inu, Ambuye, ndinu abwino ndipo mumakhululukira anthu anu.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu,
Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu, kwa onse amene amakupembedzani,
Tcherani khutu, Inu Chauta, kuti mumve pemphero langa,
Mverani kulira kwanga kopemba.
Inu, Ambuye, ndinu abwino ndipo mumakhululukira anthu anu.
Mitundu yonse ya anthu imene mwailenga idzabwera, idzakuweramirani, Inu Ambuye,
Ndipo idzalemekeza ukulu wanu,
Pakuti Inu ndinu wamkulu, mumachita zinthu zodabwitsa,
Inu nokha ndinu Mulungu.
Inu, Ambuye, ndinu abwino ndipo mumakhululukira anthu anu.
Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo,
Ndinu Mulungu wokoma mtima,
Wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika,
Mundiyang’ane ndipo mundichitire chifundo.
Inu, Ambuye, ndinu abwino ndipo mumakhululukira anthu anu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 08: 26 – 27 (Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka).
Abale, momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziwa m’mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo
osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang’ana za m’kati mwa mitima ya anthu, amadziwa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 11: 25.
Alleluia, Alleluia – Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaaululira anthu osaphunzira. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 13: 24 – 43 (Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula).
Yesu adawaphera fanizo linanso. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaafesa mbeu zabwino m’munda mwake. Koma anthu onse ali m’tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka. Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m’munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’ Iye adawayankha kuti, ‘Ndi mdani amene wachita zimenezi.’ Antchito aja adamufunsa kuti, ‘Bwanji tikamzule?’ Koma iye adati, ‘Iyai, mungakazulire kumodzi ndi tirigu pozula namsongoleyo. Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthawi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m’mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m’nkhokwe yanga.’” Yesu adawaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m’munda mwake. Ndi yaing’ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina zonse. Komabe mbeu yake ikakula, imapambana zitsamba zina zonse. Imasanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.” Yesu adawaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.” Zonsezi Yesu adalankhula ndi anthu aja m’mafanizo. Sadalankhule nawo kanthu popanda fanizo. Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, “Ndidzalankhula nawo m’mafanizo. Ndidzaulula zimene zinali zobisika chilengedwere dziko lapansi.” Pambuyo pake Yesu adawasiya anthu ambirimbiri aja, nakalowa m’nyumba. Tsono ophunzira ake adadzampempha kuti, “Tatimasulirani fanizo la namsongole wam’munda lija.” Yesu adati, “Wofesa mbeu zabwino uja ndi Mwana wa Munthu. Munda uja ndi dziko lino lapansi. Mbeu zabwino zija ndi anthu ake a Ufumu wakumwamba. Namsongole uja ndi anthu ake a Woipa uja. Mdani wodzafesa namsongole uja ndi Satana. Kudula kuja nkutha kwake kwa dziko lino lapansi, ndipo odula aja ndi angelo. Monga momwe adaazulira namsongole uja nkumutentha pa moto, zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa, nadzawaponya m’ng’anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. Tsono anthu olungama adzawala ngati dzuwa mu Ufumu wa Atate ao. Amene ali ndi makutu, amve!”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mzimu Woyera amatitsogolera potidziwitsa m’mene tiyenera kupempherera, tiyeni titembenukire kwa Atate athu a Kumwamba poyang’ana zosowa zathu ndi za Mpingo wonse:
1. Atsogoleri a Mpingo aongolere anthu ao mofatsa, moleza mtima ndi mopanda tsankho.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atsogoleri olamulira milandu asenze udindo wao mokhulupirika ndi mosakondera, ndipo adzetse chiyanjano ndi mtendere pakati pa anthu ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akulu oweruza milandu asenze udindo wao mokhulupirika ndi mosakondera, ndipo adzetse chiyanjano ndi mtendere pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse a m’Parishi yathu ino tileke makhalidwe a kukwiyirana ndi a kuganizirana zoipa, podziwa kuti tonse ndife ana ake a Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate oleza mtima, titumizireni Mzimu wanu Woyera kuti tilondole mapazi a Mwana wanu pokhala anthu ofatsa ndi achifundo. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment