Saturday, July 15, 2023

LAMULUNGU LA 15 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 15 PA CHAKA – CHAKA A.

“Mbeu zogwera pa nthaka yabwino zimabereka.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MNENERI YESAYA; YESAYA 55: 10 – 11 (Mvula imapatsa alimi mbeu ndi chakudya).

 

Chauta akunena kuti: “Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m’kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidawatumira zidzayenda bwino.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 65: 10 – 14.

 

(Luka 8:8) Mbewu ina idagwera pa nthaka yabwino ndipo idabereka zokolola zambiri.

 

Tsono Inu mumadalitsa dziko lapansi ndi kulithirira,

Ndipo mumalilemekeza kwambiri,

Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi,

Inu mumawapatsa anthu dzinthu.

 

Mbewu ina idagwera pa nthaka yabwino ndipo idabereka zokolola zambiri.

 

Pakuti ndimo m’mene mwalikonzera dzikolo,

Inu mumathirira kwambiri makwawa am’mizere,

Mumasalaza nthumbira zake, mumafewetsa nthaka ndi mvula,

Ndipo mumadalitsa mbeu.

 

Mbewu ina idagwera pa nthaka yabwino ndipo idabereka zokolola zambiri.

 

Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu,

Kulikonse kumene Inu mupita,

Kumapezeka dzinthu dzambiri,

Ngakhale ku mabusa akuchipululu kumamera msipu wambiri.

 

Mbewu ina idagwera pa nthaka yabwino ndipo idabereka zokolola zambiri.

 

Ndipo mapiri amadzazidwa ndi chimwemwe,

Madambo adzaza ndi zoweta,

Zidikha zadzaza ndi dzinthu,

Zonsezo zikufuula ndi kuimbira limodzi mwachimwemwe.

 

Mbewu ina idagwera pa nthaka yabwino ndipo idabereka zokolola zambiri.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 08: 18 – 23 (Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera).

 

Abale, Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuwamva tsopano salingana mpang’ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m’tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti zolengedwazo zidaasanduka zogonjera zopanda pake, osati chifukwa zidaafuna kutero ai, koma chifukwa Mulungu adaagamula choncho. Komabe zili ndi chiyembekezo ichi, chakuti izonso zidzamasulidwa ku ukapolo wa kuwola, ndi kulandirako ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu. Tikudziwa kuti mpaka tsopano zolengedwa zonse zakhala zikubuula ndi kumva zowawa, zonga za mkazi pa nthawi yake yochira. Tsonotu si zolengedwa zokhazi zikubuula ai. Koma ngakhale ifenso amene tili ndi mphatso zoyamba za Mzimu Woyera, tikubuula mu mtima, podikira kuti Mulungu atilandire ngati ana ake, ndi kupulumutsa matupi athu omwe.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO –

 

Alleluia, Alleluia – Mbeu ija ndiye mau a Mulungu, Yesu Khristu ndiye wofesa uja; aliyense wopeza mbeu ija adzakhala mwa lye mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 13: 01 – 09, 18 – 23 (Munthu wina adaapita kukafesa mbeu).

 

Tsiku lomwelo Yesu adatuluka m’nyumba nakakhala pansi m’mbali mwa nyanja. Anthu ambirimbiri adasonkhana kumene kunali Iye. Tsono Yesu adalowa m’chombo nakhala pansi, anthu onse aja ataima pa munda. Yesu adalankhula nawo zambiri m’mafanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m’njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola. Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama. Koma pamene dzuwa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu. Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi khumi, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi atatu.” Tsono Yesu adati, “Amene ali ndi makutu, amve! Tsono inu mumvetse bwino tanthauzo lake la fanizo la munthu wofetsa mbeu lija. Munthu aliyense akamva mau onena za Ufumu wakumwamba, koma osawamvetsa, Woipa uja amabwera nkudzalanda zimene zidafesedwa mumtima mwake. Zimenezi ndiye mbeu zogwera m’njira zija. Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu, nthawi yomweyo nkuwalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangolimbika kanthawi pang’ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthawi yomweyo munthuyo amabwerera m’mbuyo. Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi za pansi pano ndi kukondetsa chuma kumafooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso. Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu nawamvetsa. Munthu wotere amaberekadi zipatso, mwina makumi khumi, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi atatu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti tidalandira Mzimu Woyera, tingathe kupempherera anthu onse mosakayika, podziwa kuti Mulungu salephera kukwaniritsa malonjezo ake.

 

1.     Atsogoleri olalika Mau a Mulungu, alimbikire kufalitsa Mthenga Wabwino ponseponse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akatekumeni ndi ena onse amene adakali padera, atsekulire Mulungu mitima yao polandira bwino mau ake.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Makolo a ana atsogolere ana ao m’njira yachikhristu, pakuwaphunzitsa Mau a Mulungu kunyumba.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe amene tasonkhana pano, Mau a Mulungu akhazikike m’mitima mwathu ndi kubereka zipatso zokondweretsa Ambuye.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani kuti mau anu ndi opatsa moyo wosatha. Mutithandize kuwasunga ndi kuwagwiritsa ntchito pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...