Saturday, July 8, 2023

LAMULUNGU LA 14 PA CHAKA – CHAKA A

 

LAMULUNGU LA 14 PA CHAKA – CHAKA A.

“Phunzirani kwa Ine: ndine wodzichepetsa mtima.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MNENERI ZEKARIYA: ZEKARIYA 09: 09 – 10 (Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu).

 

Chauta akunena kuti: “Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono. Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu. Uta wankhondo adzauthyola. Mfumu yanu idzachititsa mtendere pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku mathero a dziko lapansi.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 145: 01 – 02, 08 – 11, 13 – 14.

 

Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse, Inu Mulungu Mfumu.

 

Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga,

Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse mpaka muyaya,

Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku,

Ndidzatamanda dzina lanu maka muyaya.

 

Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse, Inu Mulungu Mfumu.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo,

Wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika,

Chauta ndi wabwino kwa onse,

Amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.

 

Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse, Inu Mulungu Mfumu.

 

Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta,

Anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani,

Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu,

Adzasimba za mphamvu zanu.

 

Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse, Inu Mulungu Mfumu.

 

Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse,

Ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse,

Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto,

Amakweza onse otsitsidwa.

 

Ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse, Inu Mulungu Mfumu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA  08: 09, 11 – 13 (Ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo).

 

Abale, inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufawa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m’moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 11: 25.

 

Alleluia, Alleluia – Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaaululira anthu osaphunzira. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 11: 25 – 30 (Ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa).

 

Pa nthawi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu. Atate adaika zonse m’manja mwanga. Palibe wina wodziwa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira. Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m’mitima mwanu. Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Pamodzi ndi Yesu Khristu, tiyamike Atate a Kumwamba amene adatiwululira chifundo chake chofuna kupulumutsa anthu onse:

 

1.     Eklezia wa Mulungu, aunikire anthu a mafuko onse powalalikira Mthenga Wabwino, ndipo adzetse mtendere m’mitima ya anthu.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Akatekumeni ndi anthu onse amene ali padera, mitima yao ikopedwe ndi maphunziro a Yesu ndi kumvera malamulo ake.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu onse amene ali otopa ndi olemedwa atembenukire kwa Yesu Khristu, pozindikira kuti Iye angapatse anthu mtendere weniweni.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tonse tili muno tikhale anthu odzetsa mtendere pakati pa anthu powatumikira mofatsa ndi modzichepetsa mtima.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, okoma mtima, mverani mapemphero athuwa, ndipo mutiwongolere ndi Mzimu wanu Woyera kuti tipeze mpumulo weniweni polondola mapazi a Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...