LAMULUNGU LA 13 PA CHAKA – CHAKA A.
“Tiwasonyeze Ambuye kuti tiwakondadi, pakutani?”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU: 02 MAFUMU 04: 08 – 11, 14 – 16 (Munthuyu ngwoyera wa Mulungu).
Tsiku lina Elisa adapita ku Sunemu kumene kunkakhala mai wina wachuma. Maiyo adaumiriza Elisayo kuti adye chakudya kunyumba kwake. Motero Elisa ankati akamadzera njira imeneyo, nthawi zonse ankapatuka kunyumbako nkukadya nao. Tsono maiyo adauza mwamuna wake kuti, “Tsopano ndikudziwa kuti munthu amene amadutsa pano kawirikawiriyu ngwoyera wa Mulungu. Tiyeni timmangire kachipinda kakang’ono kam’mwamba, ndipo timuikiremo bedi, tebulo, mpando ndi nyale, kuti nthawi zonse akatichezera, azitha kumakakhala m’menemo.” Tsiku lina Elisa uja adafika ku Sunemu, nakalowa m’kachipinda kam’mwamba kaja kuti akapumule m’menemo. Ndipo Elisa adafunsa Gehazi kuti, “Nanga tsono timchitire chiyani?” Gehazi adayankha kuti, “Pepani, mai ameneyu alibe mwana wamwamuna, ndipo mwamuna wake ngwokalamba.” Elisa adati, “Tamuitananso.” Ndipo atamuitana, maiyo adaima pa khomo. Tsono Elisa adauza mai uja kuti, “Pa nthawi yonga yomwe ino chaka chamawachi, mudzakhala mukululuza mwana wamwamuna.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 89: 02 – 03, 16 – 19.
Ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu, Inu Chauta.
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika,
Ndidzalalika ndi pakamwa panga kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse,
Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya,
Kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
Ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu, Inu Chauta.
Ngodala anthu amene mumawaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero,
Amene amayenda m’chikondi chanu, Inu Chauta,
Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu,
Ndipo amatamanda kulungama kwanu.
Ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu, Inu Chauta.
Amanyadira ulemerero wanu ndi mphamvu zanu,
Mphamvu zathu zalimba chifukwa mwatikomera mtima,
Chauta ndiye chishango chathu,
Woyera wa Israele ndiye mfumu yathu.
Ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu, Inu Chauta.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 06: 03 – 04, 08 – 11 (Tili amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, tili amodzi ndi Iye mu imfa yake).
Abale, kodi inu simukudziwa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake? Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m’manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano. Tsono ngati tidafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. Tikudziwa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu. Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 1 PETRO 02: 09.
Alleluia, Alleluia – Inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukalowe m’kuwala kwake kodabwitsa. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 10: 37 – 42 (Munthu amene sasenza mtanda wake, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga).
Ophunzira khumi ndi awiri amenewa Yesu adawauza mau akuti: “Munthu wokonda bambo wake kapena mai wake koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Ndipo wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Amene sasenza mtanda wake ndi kumanditsata, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga. Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma. Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu
chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama. Ndipo
aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angawa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, lero popempherera anthu onse, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti aike m’mitima mwao chikondi choti onse akondane moonadi:
1. Atsogoleri a Mpingo atumikire anthu ao modzipereka ndi mosadziwerengera, powaonetsa mtima wachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Mabanja achikhristu, eniake akhale a mtima umodzi pomasamalira ana awo ndi kuwatsogolera m’njira yachikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu amene ali pa mavuto alandire chithandizo chokwanira kuchokera kwa anthu anzao. Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse a m’parishi yathu ino, tidziwe kuwala mavuto athu, tizidzipereka ku ntchito zotumikira anzathu m’zosowa zao.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, ndi mphamvu ya Mzimu wanu Woyera, mutilunzitse tonse m’chikondi chanu, pomvera mapemphero athuwa. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment