Saturday, June 24, 2023

LAMULUNGU LA 12 PA CHAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 12 PA CHAKA – CHAKA A.

“Yesu amapulumutsa onse omukhulupirira.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU MNENERI YEREMIYA: YEREMIYAYA 20: 10 – 13 (Chauta, ndiye amapulumutsa osauka kwa adani ao).

 

Ndimamva ambiri akunong’ona. Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati, “kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!” Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti ndigwa pansi, amati, “mwina mwake adzatha kunyengedwa, tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.” Koma Chauta ali nane, ndiye wankhondo woopsa. Nchifukwa chake anthu ondizunza adzakhumudwa, ndithu sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri, chifukwa cha kundilepherako, ndipo manyazi aowo sadzaiwalika konse. Inu Chauta Wamphamvuzonse, amene mumaweruza anthu molungama, amene mumapenya zamumtima, ndikupereka mlandu wanga kwa Inu. Ndikukupemphani kuti mundilipsire adani anga. Imbirani Chauta, mtamandeni Chauta! Ndiye amapulumutsa osauka kwa adani ao.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 69: 08 – 10, 14, 17, 33 – 35.

 

Mundiyankhe Inu Ambuye, chifukwa chikondi chanu nchachikulu.

 

Pakuti ndanyozedwa, nkhope yanga yagwidwa ndi manyazi chifukwa cha Inu,

Kwa abale anga ndasanduka mlendo, kwa ana a mai wanga ndili ngati wakudza,

Changu chochitira Nyumba yanu chandiphetsa,

Chipongwe cha anthu okunyozani chandigwera.

 

Mundiyankhe Inu Ambuye, chifukwa chikondi chanu nchachikulu.

 

Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta,

Mundiyankhe pa nthawi yabwino, Inu Mulungu,

Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika,

Ndi chithandizo chanu chokhulupirika. mundiyankhe, Inu Chauta,

Pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino.

Munditchere khutu, chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.

 

Mundiyankhe Inu Ambuye, chifukwa chikondi chanu nchachikulu.

 

Ozunzika aone zimenezo ndipo asangalale,

Inu amene mumafunafuna Mulungu, mulimbenso mtima

Paja Chauta amamvera anthu osowa,

Sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo.

Kumwamba ndi pansi pano,

Nyanja ndi zonse zoyenda m’menemo zitamande Iye.

 

Mundiyankhe Inu Ambuye, chifukwa chikondi chanu nchachikulu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA  05: 12 – 15 (Sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai).

 

Abale, uchimo udalowa m’dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe malamulo, machimo a munthu sawerengedwa ai. Komabe kuyambira nthawi ya Adamu kufikira nthawi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye munthu mmodzi uja, Yesu Khristu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 15: 26b, 27a.

 

Alleluia, Alleluia – Mzimu wa choona akadzabwera, adzandichitira umboni. Inunso

mudzandichitira umboni. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 10:  26 – 33 (Musamawaopa amene amapha thupi).

 

Ophunzira khumi ndi awiri amenewa Yesu adawatuma ndi mau akuti: “inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululika, ndipo kalikonse kobisika kadzadziwika. Zimene ndikukuuzirani m’chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m’manong’onong’o, inu mukazilalikire pa madenga. Musamawaopa amene amapha thupi, koma Mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m’Gehena. Suja amagulitsa atimba awiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m’modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziwa. Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliwerenga lonse. Choncho musati muziopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri. Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomera pamaso pa Atate anga amene ali kumwamba. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziwa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali kumwamba kuti sindimdziwa.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, lero popempherera anthu onse, tipereke kwa Mulungu Atate athu madandaulo ao, mavuto ndi nkhawa zao zonse:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo agwire ntchito yao mosakayika ndi mopanda mantha, adziwe kuteteza akhristu ao ndi kuwalimbitsa mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu amene akuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chao asataye mtima, koma aonetse chamuna pomchitira Yesu Khristu umboni.

Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu odwala ndi ena onse amene akuyesedwa ndi zoipa, nawonso alimbe mtima pakuphatikizana ndi Yesu Khristu m’mavuto ao.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse osonkhana pano, tileke mtima wamantha: mau athu, mayendedwe athu ndi ntchito zathu zisonyeze kuti ndifedi anthu ake a Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikuyamika kukoma mtima kwanu, chifukwa mwatipatsa mphamvu zogonjetsera zoipa zili zonse mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...