Saturday, June 17, 2023

LAMULUNGU LA 11 PA CHAKA – CHAKA A

 

 
LAMULUNGU LA 11 PA CHAKA – CHAKA A.

“Ambuye atituma kwa anzathu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKSODO: EKSODO 19: 02 – 06 (Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera).

 

Aisraele atachoka ku Refidimu adakafika ku chipululu cha Sinai, kumene adamangako mahema pafupi ndi phirilo. Mose adakwera phiri kukakumana ndi Mulungu, ndipo Mulungu adamuitana

M’phirimo namuuza kuti, “Uuze zidzukulu za Yakobo, ndiye kuti mtundu wonse wa Aisraele kuti, ‘Mudaona zimene ndidawachita Aejipito, ndiponso muja ndidakunyamulani monga m’mene mphungu imanyamulira ana ake pa mapiko ake, ndipo ndidakufikitsani kwa Ine. Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa. Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine

ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera.’ Tsono ukawauze mau amenewa Aisraele.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 100: 02 – 03, 05.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse,

Tumikirani Chauta mosangalala,

Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Dziwani kuti Chauta ndiye Mulungu,

Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake,

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Paja Iye ndi wabwino,

Chikondi chake nchamuyaya,

Kukhulupirika kwake nkosatha.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 05: 06 – 11 (Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni).

 

Abale, pa nthawi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusowabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe. Nchapatali kuti munthu afere munthu wina, ngakhale winayo akhale wolungama. Kaya kapena mwina munthu nkulimba mtima mpaka kufera munthu wabwino. Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera. Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 01: 15.

 

Alleluia, Alleluia – Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 09: 36 – 10: 08 (Adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi awiri aja, nawatuma).

 

Pamene Yesu adaona makamu a anthu, adawamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono adauza ophunzira ale kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo. Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi awiri aja, nawapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti azitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam’thupi. Atumwi khumi ndi awiriwo maina ao ndi awa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane; Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobo, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Simoni, wa m’chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake. Anthu khumi ndi awiri amenewa Yesu adawatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukalowa m’mudzi uliwonse wa Asamariya ai. Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika. Pitani, muzikalalika kuti, Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano. Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, poona kuti dzinthu ndzochuluka, koma antchito ngochepa, tiyeni tipemphe mwini dzinthu kuti atumize antchito okatuta dzinthu dzakezo:

 

1.     Ansembe ndi atsogoleri onse a Mpingo asenze udindo mwachangu ndi mogwirizana, pomamvera chifundo anthu onse amene ali olema ndi ovutika.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Akhristu onse popemphera adziwe kusinkhasikha za kukoma mtima kwa Mulungu Mpulumutsi wao, kuti iwonso aziwonetsa anzawo mtima womwewo pakuwatumikira mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Achinyamata apezeke ambiri odzipereka ku ntchito zotumikira Mpingo, pozindikira kuti anthu ambirimbiri ali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tonse tili pano tiyesetse kusenza udindo wathu wachikhristu mosatopa, kuti ana athu ndi abale athu nawonso aphunzire kumanga moyo wao pa chikondi cha Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikutamanda chifundo chanu chofuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...