Thursday, June 15, 2023

CHAKA CHA MTIMA WOYERA WA YESU – CHAKA A

CHAKA CHA MTIMA WOYERA WA YESU – CHAKA A

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA DEUTERONOMO: DEUTERONOMO 07: 06 – 11 (Mulungu adakukondani ndi kukusankhani inu).

 

Mose adauza anthu ake kuti, “Inu ndinu mtundu wopatulika wa Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adasankha inu kuti mukhale anthu ake pakati pa anthu onse a pa dziko lapansi. Mulungu pokukondani ndi kukusankhani inu, sadachitire kuti munkaposa anthu ena onse pakuchuluka. Paja mudaali ochepa ndinuyo pakati pa mitundu yonse. Koma Chauta adakukondani, ndipo adafunadi kusunga malumbiro amene adaachita ndi makolo anu. Nchifukwa chake adakupulumutsani ndi mphamvu zake, nakusandutsani mfulu, kukuchotsani m’dziko laukapolo kwa mfumu ya ku Ejipito ija. Nchifukwa chake mudziwe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake. Koma onse amene amadana ndi Mulungu, adzawabwezera pakuwaononga. Sadzamlekerera munthu wodana naye, koma adzamubwezera pakumlanga ndithu. Motero, muzimvera mosamala malangizo ndi malamulo amene ndikukulamulani lerowa.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 01 – 04, 06 – 08, 10.

 

Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuwopa.

 

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera,

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.

 

Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuwopa.

 

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse,

Ndi kuchiritsa matenda ako onse,

Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda,

Amakuveka chikondi chake chosasinthika,

Ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.

 

Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuwopa.

 

Chauta amaweruza mwachilungamo onse opsinjidwa,

Amawachitira zolungama,

Adadziwitsa Mose njira zake,

Adaonetsa Aisraele ntchito zake.

 

Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuwopa.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga,

Ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu,

Satilanga moyenerera machimo athu,

Satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.

 

Chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omuwopa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE 04: 07 – 16 (Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife).

 

Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziwa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene. Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo. Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana. Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. Tikudziwa kuti limakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera. Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi. Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu. Motero ife timadziwa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 11: 29ab.

 

Alleluia, Alleluia – Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 19: 31 – 37 (Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m’nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthawi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi).

 

Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Pasaka. Akulu a Ayuda sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo ya anthu opachikidwa aja, nkuwachotsa. Tsono asilikali adabwera, nathyola miyendo ya mmodzi mwa awiri aja amene adaapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Adateronso ndi mnzake uja. Koma pamene adafika pa Yesu, poona kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake. Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m'nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthawi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi. Amene adaona zimenezi ndiye akuzichitira umboni, kuti inunso mukhulupirire. Umboni wakewo ngwoona, ndipo mwiniwakeyo akudziwa kuti zimene akunena nzoona. Izi zidaatero kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.” Ndipo penanso Malembo akuti, “Anthu azidzamuyang’ana amene iwo adamubaya.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Pokhala a mtima umodzi ndi Yesu Khristu, tiyeni tipempherere anthu onse, poyamika Atate athu a Kumwamba:

 

1.     Ansembe ndi akulu onse a Mpingo, atsogolere anthu ao m’njira ya chikondi, powaphunzitsa za kukoma mtima kwa Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Asistere, Abrazala ndi ena onse okhala m’zipani za Mulungu, ayende molimbika m’njira ya ungwiro polondola mapazi a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akhristu ofooka ndi otayika adzidzimuke m’mitima mwao ndi kubwerera kwa Mulungu, pozindikira chifundo chake chofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno tikhale ophunzira enieni a Yesu Khristu pomayesetsa kutengera maganizo ake ndi makhalidwe ake.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, tikupereka kwa Inu mapemphero athuwa pamodzi ndi zosowa za anthu onse, poyamika chifundo chanu chosasinthika. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...