Saturday, June 10, 2023

CHAKA CHA UKARISTIA [CORPUS CHRISTI] – CHAKA A

 

CHAKA CHA UKARISTIA [CORPUS CHRISTI] – CHAKA A

“Ine ndine chakudya chopatsa moyo.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA DEUTERONOMO; DEUTERONOMO 08: 02 – 03, 14b – 16a (Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene

makolo anu anali asanadyepo).

 

Mose adauza anthu ake kuti, “Kumbukirani m’mene Chauta, Mulungu wanu, adakutsogolerani m’chipululu, pa ulendo wa pa zaka zonse makumi anai zapitazi. Adakuvutani nakuyesani ndi zowawa, kuti adziwe zimene zinali m’mitima mwanu, ndipo kuti aone ngati mudzamvera malamulo kapena ai. Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simunadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m’kamwa mwa Mulungu. Pamenepo musadzadyade ndi kuiwala Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito kumene mudali akapolo. Iye adakutsogolerani, mpaka mudabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija, m’mene munali njoka za ululu woopsa ndi zinkhanira. Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene makolo anu anali asanadyepo.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 147: 12 – 15, 19 – 20.

 

Tamanda Mulungu, iwe Yerusalemu

 

Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu,

Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,

Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako,

Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe.

 

Tamanda Mulungu, iwe Yerusalemu

 

Amadzetsa mtendere m’malire a dziko lako,

Amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala,

Akapereka lamulo pa dziko lapansi,

Mau ake amayenda mwaliwiro.

 

Tamanda Mulungu, iwe Yerusalemu

 

Amadziwitsa Yakobe mau ake,

Amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake,

Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu,

Iwo sadziwa malangizo ake.

 

Tamanda Mulungu, iwe Yerusalemu

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORITO: 01 AKORIRTO  10: 16 – 17 (Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi).

 

Abale, nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya? Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagawana mkate umodzi womwewo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 06: 51.

 

Alleluia, Alleluia – Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

Nyimbo ya Ukaristia (Sequence)

 

O SIYONI UYAMIKE

Mbusa wabwino, Buledi weniweni,

Mbuye Yesu, mutichitire chisoni.

Muteteze, nkulowetsa Nkhosa zanufe kumwamba.

 

1.     Siyoni, uyamike,
Mpulumutsi wako, Mbuye,
Mfumu ndinso Mbusa wako.

2.     Sudzafika kuimbira,
Mlungu wako mokwanira,
Ukwezetu mawu ako.

3.     Nkofunika ndithu lero,
Kutama Buledi wamoyo,
Ngwopatsa moyo womwewo.

4.     Tidziwa mosapeneka,
Kuti Yesu anapatsa,
Bulediyu kwa apositoli.

5.     Tsono tisankhule nyimbo,
Zokoma kwambiri lero,
Ndi kuimba mwachimwemwe.

6.     Misa itibweretsera,
Tsiku lomwe la kupanga,
Phwando loyerayerali.

7.     Ndi Pasaka yatsopano,
Ya Mfumu yatsopanonso,
Miyambo yakale yatha.

8.     Zalero zibadiritsa,
Zakale, monga kuyera,
M’mawa kuchotsatu mdima.

9.     Yesu anatilamula,
Kubwereza zomwe zija,
Anazichita tsikuli.

10.  Pomvera Yesu ifenso,
Tisandutsa buledi m’vinyo,
Pa nsembe yopulumutsa.

11.  Buledi asanduka Thupi,
Ndiponso vinyo Magazi,
A Khristu, Ambuye athu.

12.  Sitimvetsa, sitiona,
Koma ndithu tizimvera,
Zozizwitsa zimenezi.

13.  Buledi ndinso vinyo ali,
Chizindikiro chophimba,
Zazikulu zobisika.

14.  Tidya Thupi la Ambuye,
Ndi kumwa Magazi ake:
Akhala muziwirizi.

15.  Aliyense amlandira,
Wathunthudi, wosasweka,
Ndi wosagawika konse.

16.  Nayo Buledi wa anjelo,
Ngwa alendofe tsopano,
Manna wotipatsa nyonga.

17.  Mulungu wamphamvuzonse,
Ndiponso wodziwa zonse,
Inu mutidyetsa pano.

18.  Mutidyetsenso Kumwamba,
M’phwando la anthu oyera.
Amen. Amen. Aleluya.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 06: 51 – 58 (Thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni).

 

Yesu adati kwa makamu a Ayuda, “Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikupereka kuti anthu a pa dziko lapansi akhale ndi moyo.” Pamenepo Ayuda adayamba kukangana okhaokha, ankati, “Munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa thupi lake kuti tidye?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti thupi ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine. Chakudya chimene chidatsika kuchokera kumwamba nchimenechi. Nchosiyana ndi mana aja amene makolo anu ankadya koma nkufabe. Wodya chakudya chimenechi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Ukaristia ukusonyeza umodzi wathu ndi Yesu Khristu. Tiyeni pamodzi ndi Iyeyo tiyamike Mulungu popempherera anthu onse:

 

 

1.     Akhristu onse apeze m’sakramenti la Ukaristia gwero la moyo wa ungwiro, ndinso chifundo chokondana mwaubale, polumikizana ndi Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Makolo achikhristu adziwe kuphunzitsa bwino ana ao za Ambuye Yesu, ndipo autse m’mitima mwao chifundo chofunitsa kulandira Ukaristia.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Ansembe onse asenze udindo wao mokhulupirika ndi mwachangu, aziwonetsa chitsanzo chabwino kwa anthu ao powatsogolera m’njira ya ungwiro.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno tikhale amodzi ndi okondana mwaubale pakulandira Ukaristia kawirikawiri.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate a chifundo, tikukuthokozani chifukwa chotiitana tonse ku phwando lanu, Inu amene mufuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...