Saturday, June 3, 2023

CHAKA CHA UTATU WOYERA – CHAKA A

CHAKA CHA UTATU WOYERA – CHAKA A.

“Mulungu ndiye yani?”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKISODO; EKISODO 34: 04 – 06, 08 – 09 ("Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima.”)

 

Kutacha m’mawa, Mose adakwera phiri la Sinai monga momwe Chauta adamlamulira. Anali atanyamula miyala iwiri ija. Tsono Chauta adatsika mu mtambo, naimirira pomwe panali iyepo, ndipo adatchula dzina lake loti Chauta. Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzadza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake. Pamenepo Mose adagwada pansi napembedza. Kenaka adati, “ngati mwandikomera mtima, inu Chauta, ndikukupemphani kuti mupite nafe. Anthuwa ngokanika, koma Inu mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo mutilandire ife, kuti tikhale anthu anu.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: DANIELE 03: 52 – 55.

 

Mulandire Ulemu ndi chiyamiko mpaka muyaya.

 

Tikutamandani, Inu Ambuye, Mulungu wa makolo athu.

Tikutamanda dzina lanu la ulemerero.

 

Mulandire Ulemu ndi chiyamiko mpaka muyaya.

 

Tikutamandani m’Nyumba yanu ya ulemerero.

Tikutamandani Inu amene mwakhala pa chimpando chaufumu.

 

Mulandire Ulemu ndi chiyamiko mpaka muyaya.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORITO; 02 AKORITO 13: 11 – 14 (Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera).

 

Abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu Mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu. Mupatsane moni mwa chikondi choona. Anthu onse a Mulungu akukupatsani moni. Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi Chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – CHIBVUMBULUTSO 01: 08.

 

Alleluia, Alleluia – Ulemu ukhale kwa Atate, ndi kwa Mwana ndi kwa Mzimu Woyera, kwa Mulungu amene alipo, ndipo analipo, ndipo alikudza. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 03: 16 – 18 (Mulungu adatuma Mwana wakeyo kuti adzapulumutse dziko lapansi).

 

Yesu adati kwa Nikodemo, “Mulungutu adawakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzawapulumutse. Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Mulungu watiwonetsa kukoma mtima kodabwitsa potisonkhanitsa tonse m’mbumba yake. Tiyeni timuyamike popempherera anthu onse:

 

1.     Akhristu onse akhale a mtima umodzi ndi a chikhulupiriro chimodzi, monga Mulungu ali m’modzi, Atate ndi Mwana ndi Mzimu Woyera.
Ambuye mutimvere, Ambuye, mutivomereze.

2.     Atsogoleri a maiko onse alamulire anthu ao mwachilungamo ndi mwachikondi, ndipo alekeretu makhalidwe ankhanza ndi a tsankho.
Ambuye mutimvere, Ambuye, mutivomereze.

3.     Mabanja onse, eni ake akhale a maganizo amodzi ndipo kukondana kwao kukhale chizindikiro chosonyeza kukoma mtima kwa Mulungu.

Ambuye mutimvere, Ambuye, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno, timange moyo wathu pa maziko a chikondi ndi amtendere, pokumbukira kuti tonse ndife ana a Mulungu, ndi abale ake a Yesu, kudzera mwa Mzimu wake Woyera.
Ambuye mutimvere, Ambuye, mutivomereze.

 

 

Mulungu Atate athu, popereka mapemphero athuwa, tikuti: Ulemu ukhale kwa Inu, ndi kwa Mwana wanu ndi kwa Mzimu Woyera, leroli ndi masiku onse mpaka muyaya.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...