“Adawauzira Mpweya wopatsa moyo.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 02: 01 – 11 (Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula).
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Ndipo adaona ngati timalawi ta moto tooneka ngati malilime tikugawikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankawalankhulitsira. Tsono, m’Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku mayiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankawamva akulankhula chilankhulo chake. Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “Kodi onse akulankhulawa, si Agalileya? Nanga bwanji aliyense mwa ife akuwamva akulankhula chilankhulo chakwao? Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuwamva anthuwa akulankhula m’zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 104: 01, 24, 29 – 34.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,
Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri,
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri,
Ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Mukazichotsera mpweya, zimafa nkubwerera ku fumbi,
Mukatumiza mpweya wanu zimalengedwa,
Ndipo mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya,
Chauta akondwe nazo ntchito zakezo,
Mapemphero anga amkomere Chauta,
Popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORITO; 01 AKORITO 12: 03b – 07, 12 – 13 (Tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi).
Abale, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, ‘Yesu ndi Ambuye.’
Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera m’modzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timawatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi m’modzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakuti yakuti yoti ayigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
Nyimbo ya Pentekoste (Sequence)
(Nyimboyi itha kunenedwa kapena kuyimbidwa)
Bwerani Mzimu Woyera
Tumizani kuwala kwanu
Kufumira kumwambako.
Bwerani, Tate wa amphawi
Bwerani, wopatsa mphatso
Inu muuni wa mitima.
Ndinu Msangalatsi ndithu
Woyendera mitima yathu
Kuti mudzaithunzitsa.
Pa ntchito ndinu Mpumulo
Mumatichotsera kutentha
Ndi kutsangula misozi yathu.
Ndinu kuwala kokoma
Dzazani mitima yathu
Ya ife anthu okumverani.
Mutapanda kudzamthandiza
Munthu sangapeze kanthu
Zonse zidzamuipira.
Tsukani zoipa zathu
Dzatsirireni zouma
Chiritsani mabala athu.
Dzafewetseni zolimba
Funditsani zozizira
Lungamitsani zokhota.
Tipatseni anthu anufe
Okhulupirira Inu
Mphatso zisanu ndi ziwiri.
Kometsani makhalidwe athu
Katifikitseni kumwamba
Kukadala nthawi zonse.
Amen.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO
Alleluia, Alleluia – Bwerani Mzimu Woyera, mudzaze mitima ya anthu okhulupirira ndipo chikondi chanu chikhazikike mwa iwo. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 20: 19 – 23 (Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani. Landirani Mzimu Woyera).
Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’thiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira m’pweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, lero popempherera anthu onse, tikumbukire kuti Atate athu a Kumwamba salephera kupereka Mzimu Woyera kwa iwo amene amapempha:
1. Eklezia afalitse Mthenga Wabwino ponseponse ndi mphamvu za Mzimu Woyera, ndipo atsogolere anthu m’njira ya ungwiro ndi ya chikondi.
Tumizani, Ambuye, Mzimu wanu Woyera.
2. Akhristu onse ayesetse kukhala a mtima umodzi, Mzimu Woyera alunzitse mitima yao ndi kuwatsogolera m’choona chonse.
Tumizani, Ambuye, Mzimu wanu Woyera.
3. Anthu onse amene adakali padera, Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwalondoloza m’njira ya chipulumutso.
Tumizani, Ambuye, Mzimu wanu Woyera.
4. Ife tonse tili muno, titumikire Mpingo wa Mulungu modzipereka, pakugwiritsa ntchito mphatso zomwe tidalandira kwa Mzimu Woyera.
Tumizani, Ambuye, Mzimu wanu Woyera.
Mulungu Atate athu, tikuthokozani chifukwa mwa Ubatizo Mzimu Woyera wanu adatisandutsa thupi limodzi limene mutu wake ndi Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment