CHAKA CHAKUKWERA KWA AMBUYE KUMWAMBA – CHAKA A.
“Inetu ndili nanu masiku onse.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 01: 01 – 11 (Yesu adatengedwa kupita kumwamba, iwo akupenya).
A Teofilo, m’buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi, kufikira tsiku limene adzatengedwa kupita kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adawasankha aja zoti iwowo adzachite. Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adawaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai. Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adawalamula kuti, “musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankaabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.” Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthawi yoti mukhazikitse ufumu mu Israele?” Iye adati, “si ntchito yanu kuti mudziwe nthawi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao. Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.” Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamlandira nkumubisa, iwo osamuonanso. M’mene atumwi aja ankayang’anitsitsabe kumwamba, Iye akupita, mwadzidzidzi anthu awiri ovala zoyera adaimirira pambali pao. Anthuwo adawafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang’ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita kumwamba, adzabwerenso monga momwe mwamuwoneramu akupita kumwambako.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 47: 02 – 03, 06 – 09.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
Ombani m’manja inu anthu a mitundu yonse,
Fulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe,
Paja Chauta Wopambanazonse ndi woopsa,
Ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira,
Chauta wakwera, akumuimbira lipenga,
Imbani nyimbo zotamanda Mulungu,
Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi,
Imbani mwaluso nyimbo zotamanda,
Mulungu amalamulira mitundu ya anthu,
Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 01: 17 – 23 (Iye wakhala kudzanja lamanja la Atate).
Abale, ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziwe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m’mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziwe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja la manja m’dziko la kumwamba. Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angawatchule nthawi ino kapenanso nthawi ilikudza. Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa mpingo. Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 28: 19a, 20b.
Alleluia, Alleluia – Pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukawasandutse ophunzira anga. Ndipo ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 28: 16 – 20 (Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano).
Ophunzira khumi ndi mmodzi aja adapita ku Galileya kuphiri kumene Yesu adaapangana nawo kuti akakumane. Pamene adamuwona, adampembedza, koma ena ankakayika. Yesu adadza pafupi nawauza kuti, “mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukawasandutse ophunzira anga. Muzikawabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera. Mudzikawaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza Yesu Khristu ali nafe masiku onse, tiyeni, pamodzi naye tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti Ufumu wao udze:
1. Akhristu onse alimbikire kufalitsa Mthenga Wabwino pakati pa anzao, pokhala mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Atate, Ufumu wanu udze!
2. Achinyamata apezeke ambiri odzipereka ku ntchito yokalalikira mau a Mulungu ku maiko akunja.
Atate, Ufumu wanu udze!
3. Anthu odwala ndi onse amene ali m’mavuto, alimbe mtima ndi kusangalala, pozindikira kuti Yesu ali nawo pafupi nthawi zonse.
Atate, Ufumu wanu udze!
4. Ife tonse tili muno, mau athu ndi ntchito zathu zisonyeze kuti Yesu Khristu alikukhazikadi ufumu wake leroli ndi masiku onse.
Atate, Ufumu wanu udze!
Mulungu Atate athu, muunikire anthu onse ndi Mzimu wanu Woyera kuti azindikire ntchito zodabwitsa zimene mulikuchita ponseponse, kudzera mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment