“Adzakupatsani Nkhoswe ina.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 08: 05 – 08, 14 – 17 (Adawasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera).
Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya, namalalikira anthu akumeneko za Khristu, mpulumutsi wolonjezedwa uja. Makamu a anthu ndi mtima umodzi ankatchera makutu ku zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera mau ake nkumaona zozizwitsa zimene iye ankachita. Pakuti mizimu yonyansa inkatuluka mwa anthu ambiri amene anali atagwidwa nayo, nimafuula kwambiri. Ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo kapena opunduka, ankachira. Choncho munali chimwemwe chachikulu mumzinda muja. Pamene atumwi okhala ku Yerusalemu adamva kuti anthu aku Samariya alandira mau a Mulungu, adatumako Petro ndi Yohane. Iwowo atafika, adayamba kupempherera okhulupirira aja kuti alandire Mzimu Woyera. Nthawiyo nkuti Mzimu Woyera asanafike pa wina aliyense mwa iwo. Onsewo anali atangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu. Tsono Petro ndi Yohane adawasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 66: 01 – 07, 16, 20.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau,
Inu anthu onse a pa dziko lapansi,
Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero,
Muuzeni Mulungu kuti, ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani,
Amaimba nyimbo zotamanda Inu,
Amaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
Ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Adasandutsa nyanja kuti ikhale nthaka youma,
Anthu adaoloka mtsinje uja poyenda pansi,
Nchifukwa timukondwerere Iye,
Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
Koma zoona Mulungu wandimvera,
Wasamala mau a pemphero langa.
Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa,
Sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 03: 15 – 18 (Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo).
Abale, muzilemekeza Khristu m’mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthawi iliyonse kuwayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza. Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsata, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao. Nkwabwino kumva zowawa chifukwa chochita zabwino, ngati Mulungu wafuna choncho, koposa kumva zowawa chifukwa chochita zoipa. Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m’malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 14: 23.
Alleluia, Alleluia – Yesu anati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine, Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.” – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 14: 15 – 21 (Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina).
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ngati mundikonda, mudzitsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziwitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziwa. Koma inu mumamdziwa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthawi pang’ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. Tsiku limenelo mudzadziwa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga nawatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa Iye.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti Ambuye Yesu alikukhala mwa ife, tingathe kupemphera mogwirizana ndi mosakaika, kuti “Ambuye, tumani Mzimu wanu Woyera!”
1. Eklezia akhale chizindikiro chosonyeza anthu onse chifundo cha Mulungu chofuna kuwapulumutsa.
Ambuye, tumani Mzimu wanu Woyera.
2. Ansembe apezeke ambiri olalikira Mthenga Wabwino ku maiko akunja.
Ambuye, tumani Mzimu wanu Woyera.
3. Anyamata oyembekeza kulandira Sakramenti la Ulimbitso akhale okonzeka kuchitira Yesu Khristu umboni pa moyo wao Wonse.
Ambuye, tumani Mzimu wanu Woyera
4. Ife tonse tili muno, tiyende molimbika m’njira ya ungwiro ndi ya chikondi.
Ambuye, tumani Mzimu wanu Woyera
Mulungu Atate athu, mwa chifundo chanu mverani mapemphero athuwa pamodzi ndi madandaulo a anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment