Saturday, May 6, 2023

LAMULUNGU LA 05 LA PASAKA – CHAKA A.

“Ine ndine njira yopita kwa Atate."

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 06: 01 – 07 (Pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi awiri odzazidwa ndi Mzimu Woyera).

 

Masiku amenewo ophunzira aja ankachulukirachulukira. Koma Ayuda olankhula Chigriki anali ndi dandaulo pa Ayuda olankhula Chiyuda kuti akazi ao amasiye sankasamalidwa bwino pamene zachifundo za tsiku ndi tsiku zinkagawidwa. Tsono atumwi khumi ndi awiri aja adasonkhanitsa gulu lonse la ophunzira, nawauza akuti, “sibwino kuti ife tizisiya kulalika mau a Mulungu nkumayang’anira za chakudya. Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi awiri, a mbiri yabwino, odzadzidwa Mzimu Woyera ndiponso nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi. Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.”  Mau amenewa adakomera gulu lonse lija, motero adasankha Stefano, munthu wodzadzidwa ndi chikhulupiriro ndiponso ndi Mzimu Woyera. Adasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanore, Timoni, Parmenasi, ndi Nikolasi wa ku Antiokeya, yemwe kale anali atasiya chikunja kutsata chiyuda. Adawaimiritsa pamaso pa atumwi, ndipo atumwiwo adapemphera nawasanjika manja. Mau a Mulungu ankafalikira ponseponse, ndipo ophunzira ankachulukirachulukira ndithu ku Yerusalemu. Ansembe omwe ambirimbiri ankamvera chikhulupirirocho.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 01 – 05, 18 – 19.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake,

Zoonadi ochita zolungama azitamanda,

Tamandani Chauta ndi pangwe,

Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Mau a Chauta ndi olungama,

Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,

Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Chauta amayang’ana anthu omumvera,

Ndikudalira chikondi chake chosasinthika,

Iye amachita izi kuti awapulumutse ku imfa,

Ndi kuwasungira moyo anthuwo pa nthawi ya njala.

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 02: 04 – 09 (Inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu).

 

Bwerani kwa Iye amene ali mwala wa moyo womwe anthu adaukana, koma Mulungu adausankha kuti ngwamtengowapatali. Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M’menemo muzitumikira ngati nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu. Paja m’malembo mudalembedwa kuti, “ndasankha mwala wamtengowapatali. Ndikuuika tsopano m’Ziyoni, ngati mwala wapangodya. Wokhulupirira Iye sadzachita manyazi.” Tsono kwa inu okhulupirira, Iye ndi wamtengowapatali. Koma kwa osakhulupirira, ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “mwala womwe amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.” Mau a Mulungu akutinso, “umenewu ndi mwala wokhumudwitsa anthu, ndi nthathwe lowagwetsa.” Amakhumudwa popeza kuti amakana kumvera mau a Mulungu, ndipo anali oyeneradi kuti adzaone zotere. Komatu inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukalowe m’kuwala kwake kodabwitsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 14: 06.

 

Alleluia, Alleluia – Ineyo ndine njira, ndine Choona ndiponso Moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 14: 01 – 12 (Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo).

 

Yesu adawauza ophunzira akewo kuti, “mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, Khulupirirani inenso. M’nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine. Ndipo kumene ndikupita Ineko, njira yake mukuidziwa.” Tomasi adati, “Ambuye, sitikudziwa kumene mukupita, nanga njira yake tingaidziwe bwanji?” Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine. Mukadandidziwa Ine, Atate anganso mukadawadziwa. Kuyambira tsopano mukuwadziwa ndipo mwawaona.” Filipo adati, “Ambuye, tiwonetseni Atatewo, Mukatero tikhutira.” Yesu adamuyankha kuti, “Iwe Filipo, ndakhala nanu nthawi yonseyi, ndipo sunandidziwebe? Amene waona Ine, waonanso Atate. Nanga bwanji ukuti ‘tiwonetseni Atate?’ Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoopsa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pa Ubatizo tidasanduka anthu akeake a Mulungu. Tsono mogwirizana ndi Yesu Khristu, tipereke ulemu kwa Atate athu a Kumwamba popempha madalitso ao:

 

1.     Akhristu onse, akhale okondana ndi ogwirizana mwa Yesu Khristu, aoneke ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amange nayo nyumba.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Adikoni ndi atsogoleri ena a Mpingo, asenze udindo wao molimbana ndipo atumikire anthu a mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu amasiye ndi ena onse ali m’mavuto, alandire chisamaliro chokwanira kuchokera kwa anzao ndipo adziwe kuyamika chifundo cha Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tonse a m’Parishi yathu ino, mayendedwe athu ndi ntchito zathu zotumikira anzathu, zisonyeze kuti Yesu Khristu ndiyedi njira yopita kwa Atate.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, mutiyang’ane ndi maso achifundo ndipo mumvere mapemphero athuwa, popeza kuti mwatiwonetsa kukoma mtima kwanu, mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...