LAMULUNGU LA 04 LA PASAKA – CHAKA A.
LAMULUNGU LAMAITANIDWE (VOCATION SUNDAY)
“Ine ndadza kuti nkhosa zikhale ndi moyo.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 02: 14a, 36 – 41 (Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi).
Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Tsono Aisraele onse adziwe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidawalatsa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adawauza kuti, “tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawatama.” Petro adalankhulanso mau ena ambiri, nawachenjeza kuti, “muthawe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 23: 01 – 06.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu,
Amandigoneka pa busa lamsipu,
Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako,
Amatsitsimutsa moyo wanga.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Amanditsogolera m’njira za chilungamo,
Malinga ndi ulemerero wa dzina lake,
Ngakhale ndiyende m’chigwa chamdima wabi,
Sindidzaopa choipa chilichonse pakuti Inu Ambuye mumakhala nane.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona,
Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta,
Mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu,
Zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga.
Ndidzakhala m’Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 02: 20b – 25 (Koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang’anirani).
Koma ngati mukapirira zowawa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu. Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zowawa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake. Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lilonse. Pamene anthu ankamuchita chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama. Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m’thupi lake pa mtanda, kuti m’machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake. Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang’anirani.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 10: 14.
Alleluia, Alleluia – Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo izozo Ineyo zimandidziwa. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 10: 01 – 10 (Ine ndine khomo la nkhosa).
Yesu adanena kuti, “Kunena zoona, munthu wolowa m’khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda. Koma munthu wolowera pa khomo ndi mbusa wa nkhosazo. Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziwa mau ake. Mlendo sizidzamtsatira ai, zidzamthawa, chifukwa sizidziwa mau a alendo.” Yesu adawaphera fanizoli, koma iwo sadamvetse zimene ankawauzazo. Tsono Yesu adatinso, “ndithu ndikunenetsa kuti Ine ndi khomo la nkhosa. Ena onse amene adabwera Ine ndisanafike, ngakuba ndi olanda, koma nkhosa sizidawamvere. Khomo ndine. Munthu akalowera pa Ine, adzapulumuka. Azidzalowa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya. Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo wake wochuluka.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Ambuye adati: Dzinthu ndzochuluka, koma antchito achepa. Tiyeni, tipemphe Mulungu, mwini dzinthu, kuti atumize antchito ambiri kukatuta dzinthu dzake:
1. Ansembe onse adziwe kutsogolera anthu ao m’njira ya ungwiro ndi yachikondi, pokhala nawo mtima womwe unali mwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Amuna ndi akazi a m’zipani zachikhristu, akhale okhulupirika pa malonjezo ao, aonetse kudza kwake kwa Ufumu wa Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anyamata ndi atsikana amene Mulungu awaitana ku ntchito yake, alimbike m’maphunziro ao, mpaka akalowedi unsembe kapena moyo wa chipani.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tili muno tisenze udindo wathu wachikhristu mosafookera ndipo chitsanzo chathu chikokere ana athu ku ntchito ya Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukupemphani zimenezi kudzera mwa Mwana wanu amene mudamuika kukhala mbusa wotitsogolera ndi wansembe wotiimirira pamaso panu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment