LAMULUNGU LA 21 PA CHAKA – CHAKA A.
“Ndidzakupatsa makii a Ufumu wakumwamba.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 22: 19 – 23 (Ndidzampatsa makii a ulamuliro wa pa banja la mfumu Davide).
Chauta Wamphamvuzonse adamuuza Sebina, kapitao woyang’anira nyumba yaufumu, kuti: “Ndidzakuchotsa pa ukapitao wako, ndipo ndidzakutsitsa pakuthetsa udindo wako. Tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga Eliyakimu, mwana wa Hilikiya. Ndidzam’veka mkanjo wako ndi lamba wako ndi kumpatsa ulamuliro wako. Tsono adzalamulira anthu onse okhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. Ndidzampatsa makii a ulamuliro wa pa banja la mfumu Davide. Akadzatsekula, palibe amene adzatseke. Ndipo adzatseka, popanda wina wotsekula. Ndidzamulimbitsa ngati chikhomo pa udindo wakewo, ndipo adzakhala wopatsa ulemu kwa banja la atate ake.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 138: 01 – 03, 06, 08.
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse,
Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu,
Ndikugwada mowerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera.
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,
Chifukwanso cha kukhulupirika kwanu,
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha,
Mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Ngakhale Chauta ndi wamphamvu, amasamalira anthu otsika,
Koma anthu odzikuza amawadziwira chapatali,
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya,
Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 11: 33 – 36 (Zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye
ndipo zimalinga kwa Iye).
Abale, chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndikudziwa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire? Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, Ndani amadziwa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo? Ndani adaayamba waperekapo kanthu kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezereko kanthu? Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo
zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 16: 18.
Alleluia, Alleluia – Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 16: 13 – 20 (Ndiwe Petro, ndipo ndidzakupatsa makii a Ufumu wakumwamba).
Pamene Yesu adafika ku madera a ku Kesareya Filipi, adafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthune ndine yani?” Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu Yeremiya kapena mmodzi mwa aneneri.” Apo Yesu adawafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.” Yesu adamuuza kuti, “Ndiwe wodala, Simoni mwana wa Yona, pakuti si munthu wakuululira zimenezi ai, koma ndi Atate anga amene ali Kumwamba. Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli
ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa. Ndidzakupatsa makii a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.” Yesu atanena zimenezi, adalamula ophunzira aja kuti asauze munthu aliyense kuti Iye ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tigwirizane nawo akhristu onse popereka mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba, podziwa kuti Yesu Khristu akutitsogolera:
1. Apapa ndi Aepiskopi onse asenze udindo wao molimbika ndi mogwirizana, ndipo ayendetse Mpingo m’njira yaungwiro ndi yachikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Ansembe onse asamalire akhristu ao ndi kuwalimbikitsa, pakuwadyetsa Mau a Mulungu ndi kuwagawira Chakudya cha Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Abale athu a mipingo ina, Mulungu awaunikire ndi Kuwakhazikitsa m’chikondi chake, mpaka tidzalumikizane tonse m’chikhulupiriro chimodzi.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse a m’Parishi yathu ino, tithandizane kuti ntchito zathu zotumikira Mpingo ziwawonetse anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu Ambuye athu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukuyamikani chifukwa mwatisonkhanitsa tonse m’mbumba yanu kuti tikhale amodzi m’chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/