Saturday, April 29, 2023

LAMULUNGU LA 04 LA PASAKA – CHAKA A.

LAMULUNGU LAMAITANIDWE (VOCATION SUNDAY)

“Ine ndadza kuti nkhosa zikhale ndi moyo.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 02: 14a, 36 – 41 (Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi).

 

Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Tsono Aisraele onse adziwe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidawalatsa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adawauza kuti, “tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawatama.” Petro adalankhulanso mau ena ambiri, nawachenjeza kuti, “muthawe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 23: 01 – 06.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu,

Amandigoneka pa busa lamsipu,

Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako,

Amatsitsimutsa moyo wanga.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Amanditsogolera m’njira za chilungamo,

Malinga ndi ulemerero wa dzina lake,

Ngakhale ndiyende m’chigwa chamdima wabi,

Sindidzaopa choipa chilichonse pakuti Inu Ambuye mumakhala nane.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona,

Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta,

Mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu,

Zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga.

Ndidzakhala m’Nyumba mwanu moyo wanga wonse.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 02: 20b – 25 (Koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang’anirani).

 

Koma ngati mukapirira zowawa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu. Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zowawa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake. Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lilonse. Pamene anthu ankamuchita chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama. Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m’thupi lake pa mtanda, kuti m’machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake. Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang’anirani.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 10: 14.

 

Alleluia, Alleluia – Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo izozo Ineyo zimandidziwa. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 10: 01 – 10 (Ine ndine khomo la nkhosa).

 

Yesu adanena kuti, “Kunena zoona, munthu wolowa m’khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda. Koma munthu wolowera pa khomo ndi mbusa wa nkhosazo. Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziwa mau ake. Mlendo sizidzamtsatira ai, zidzamthawa, chifukwa sizidziwa mau a alendo.” Yesu adawaphera fanizoli, koma iwo sadamvetse zimene ankawauzazo. Tsono Yesu adatinso, “ndithu ndikunenetsa kuti Ine ndi khomo la nkhosa. Ena onse amene adabwera Ine ndisanafike, ngakuba ndi olanda, koma nkhosa sizidawamvere. Khomo ndine. Munthu akalowera pa Ine, adzapulumuka. Azidzalowa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya. Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo wake wochuluka.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Ambuye adati: Dzinthu ndzochuluka, koma antchito achepa. Tiyeni, tipemphe Mulungu, mwini dzinthu, kuti atumize antchito ambiri kukatuta dzinthu dzake:

 

1.     Ansembe onse adziwe kutsogolera anthu ao m’njira ya ungwiro ndi yachikondi, pokhala nawo mtima womwe unali mwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Amuna ndi akazi a m’zipani zachikhristu, akhale okhulupirika pa malonjezo ao, aonetse kudza kwake kwa Ufumu wa Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anyamata ndi atsikana amene Mulungu awaitana ku ntchito yake, alimbike m’maphunziro ao, mpaka akalowedi unsembe kapena moyo wa chipani.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno tisenze udindo wathu wachikhristu mosafookera ndipo chitsanzo chathu chikokere ana athu ku ntchito ya Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukupemphani zimenezi kudzera mwa Mwana wanu amene mudamuika kukhala mbusa wotitsogolera ndi wansembe wotiimirira pamaso panu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, April 22, 2023

LAMULUNGU LA 03 LA PASAKA – CHAKA A

LAMULUNGU LA 03 LA PASAKA – CHAKA A.

“Yesu akutitsogolera m’njira yopita kwa Atate.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 02: 14, 22 – 33 (Kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa).

 

Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mawu kuti, “inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga. Inu Aisraele mverani mawu awa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziwa. Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m’mene Iye amadziwiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. Koma Mulungu adammasula ku zowawa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe pa mtanda. Paja Davide ponena za Iye adati, ‘ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthawi zonse, pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja kuti ndingagwedezeke. Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m’manda, ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku malo akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole. Mudandidziwitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’ Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m’manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano. Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziwa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzalowe ufumu wake. Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, ‘Iye sadasiyidwe ku malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’ Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 16: 01 – 02, 05, 07 – 11.

 

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

 

Mundisunge In Mulungu pakuti ndikuthawira kwa Inu,

Ndimamuuza Chauta kuti, Inu ndinu Ambuye anga,

Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.

 

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

 

Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa,

Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe,

Nthawi zonse ndimalingalira za Chauta,

Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja palibe amene angandiopse konse.

 

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

 

Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,

Ndipo m’katikati mwangamu ndikusangalala,

Thupi langanso lidzakhala pabwino,

Chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,

Simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.

 

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

 

Mumandiwonetsa njira ya ku moyo,

Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,

Ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.

 

Chauta, mundiwonetse njira ya ku moyo.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 01: 17 – 21 (Adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu).

 

Okondeka, Mulungu alibe tsankho. Amaweruza aliyense molingana ndi zochita zake. Ngati mumutcha Atate pamene mukupemphera, mchitireni ulemu nthawi yonse muli alendo pansi pano. Mukudziwa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema. Iyeyo Mulungu adaamsankhiratu dziko lapansi lisanalengedwe, koma wamuwonetsa nthawi yotsiriza ino chifukwa cha inu. Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adaamukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 24: 32.

 

Alleluia, Alleluia – Ambuye Yesu, mutitanthauzire Malembo. Mitima yathu iyake

mwa ife pamene mumalankhula nafe. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 24: 13 – 35 (Maso ao adatsekuka, namuzindikira pamene adanyema buledi).

 

Tsiku lomwelo ophunzira awiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika. Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwini wake adayandikira nkumatsagana nawo. Koma maso ao adachita chidima, mwakuti sadamzindikire. Tsono Yesu adawafunsa kuti, “kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?”  Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni, kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “kodi mlendo ndinu nokha m’Yerusalemu muno, wosadziwa zimene zochitika m’menemo masiku apitawa?” Yesu adawafunsa kuti, “zotani?” Iwo adati, “za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali za mphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe. Akulu a ansembe ndi akulu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachita pamtanda. Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi. Komanso azimayi ena a m’gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m’mamawa, ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti Yesu ali moyo. Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe Azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuone ai.” Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira mnsanga zonse zija zimene aneneri adanena. Kodi inu simukudziwa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zowawa zonsezi kuti alowe mu ulemerero wake?” Kenaka Yesu adayamba kuwatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m’Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse. Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira. Koma iwo adamuumiriza kuti, “mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; Onani dzuwa likulowa.” Apo Iye adakalowa m’Nyumba nakakhala nawo. Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema nawagawira. Nthawi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira. Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira malembo.” Nthawi yomweyo adanyamuka kubwerera ku Yerusalemu. Adakapeza ophunzira khumi ndi mmodzi aja atasonkhana pamodzi ndi anzao ena, akunena kuti, Ambuye adaukadi, ndipo Simoni wawaona. Tsono nawonso awiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira paja, ndiponso m’mene iwo adaamzindikira pamene iye ankanyema buledi.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tamva mau a Yesu Khristu alikutanthauzira Malembo Oyera. Tiyeni timupemphe kuti kuwala kwake kuunikire anthu onse:

 

1.     Mpingo wa Mulungu uunikire anthu onse ndi maphunzitso ake ndi makhalidwe ake, powaonetsa kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Anthu amene akuvutika mumtima ndi kuyenda mu mdima, maso ao atsekuke popezana ndi Yesu Khristu m’Malembo Oyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anzathu amene ali ku ulendo ndi ena onse okhala okha kutali ndi kumudzi kwao, adziwe kupirira mavuto aliwonse, pokhulupirira Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse osonkhana pano, tipemphererane kuti tithe kuzindikira nkhope ya Yesu Khristu mwa anthu amene timakumana nawo masiku onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, tikuyamikani chifukwa mudatipatsa Mwana wanu kuti atsagane masiku onse pa ulendo wathu wonka kwa Inu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, April 15, 2023

LAMULUNGU LA 02 LA PASAKA – CHAKA A. [LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA AMBUYE – DIVINE MERCY SUNDAY]

LAMULUNGU LA 02 LA PASAKA – CHAKA A.

[LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA AMBUYE – DIVINE MERCY SUNDAY]    

“Mtendere wa Ambuye ukhale nanu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 02: 42 – 47 (Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagawana zinthu zao).

 

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagawana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagawira onse, malinga ndi kusowa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m’Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankawakonda mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawawonjezera ena olandira chipulumutso.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 02 – 04, 13 – 15, 22 – 24.

                                                

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Aisraele anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya,

Banja la Aroni linene kuti, Chikondi chake nchamuyaya,

Anthu oopa Chauta anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.

 

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa,

Koma Chauta adandithandiza,

Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga,

Ndiye Mpulumutsi wanga.

 

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

Womwewo wasanduka mwala wapangodya,

Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu,

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga,

Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

 

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 01: 03 – 09 (lye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso

pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa).

 

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati cholowa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthawi yotsiriza. Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zowawa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthawi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 20: 29.

 

Alleluia, Alleluia – Yesu adati, wakhulupirira chifukwa wandiona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 20: 19 – 31 (Patapita masiku asanu ndi atatu, Yesu adabwera).

 

Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira mpweya nati, “landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.” Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi awiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “ife tawaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “ndikapanda kuwona mabala a misomali m’manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m’nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.” Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m’nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m’nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m’buku muno. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m’dzina lake.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Ife tonse amene tikhulupirira Yesu ngakhale sitimuwona, tiyeni tiyamike Atate athu a Kumwamba ndi kupempha madalitso ao:

 

1.     Akhristu onse akonde ndi kumagwirizana monga akhristu oyamba aja, pozindikira kuti Yesu Khristu ali nawo nthawi zonse.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Anthu onse alandire mtendere wa Yesu Khristu m’mitima mwao, ndiponso m’banja mwao ndi pakati pa maiko onse.

Tikupemphani, mutivomereze.­

3.     Anthu odwala ndi onse amene avutika m’mitima mwao, akondwere pokhulupirira Yesu Khristu pa nthawi ino ya Pasaka.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’Parishi yathu ino, tilimbikire kuchita zabwino ndi kumathandizana mwaubale, kusonyeza kuti Yesu Khristu ali moyodi akutitsogolera.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, poyamika Kuuka kwa Mwana wanu kwa akufa, tikutula mapemphero athuwa m’manja mwanu, pamodzi ndi mafuno a anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

 

 

Saturday, April 8, 2023

LAMULUNGU LA PASAKA – CHAKA A.

LAMULUNGU LA PASAKA – CHAKA A.         

“Yesu Khristu ndiye Moyo Wathu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 10: 34a, 37 – 43 (Adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa).

 

Petro adayamba kuyankhula, adati, “zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Mukudziwa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthawi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziwa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzodza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi satana. Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m’dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera. Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 01 – 02, 16 – 17, 22 – 23.

                                                

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Kapena Alleluia, Alleluia, Alleluia!

 

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

Ndipo chikondi chake nchamuyaya,

Aisraele anene kuti, ‘Chikondi chake nchamuyuaya.’

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

 

Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,

Dzanja lamanja la Chauta lapambana,

Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,

Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

Womwewo wasanduka mwala wapangodya,

Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

Zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

--------------------------------------

 

[CHITSANKHO CHOYAMBA]

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 03: 01 – 04 (Muzifunafuna za Kumwamba, kumene kuli Ambuye).

 

Abale, ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

[CHITSANKHO CHACHIWIRI]

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: AKORINTO 05: 06b – 08.

 

Kodi simuwadziwa mau aja akuti, “chofufumitsa buledi chapang’ono chimafufumitsa mkate wonse?” Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale ndi oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Pasaka, adaphedwa kale ngati nsembe. Tiyeni tsono, tichite chikondwererocho, osati ndi chofufumitsira chakale chija cha uchimo ndi cha kuipa mtima, koma ndi buledi wosafufumitsa, wakuyera mtima ndi wa choona.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 01 AKORINTO 05: 07.

 

Alleluia, Alleluia – Kankhosa kathu ka Pasaka ndiye Yesu Khristu amene waphedwa ngati nsembe. Tiyeni tsono, tichite chikondwerero choyamikira Ambuye. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 20: 01 – 09 ('Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.').

 

Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m’mamawa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adawauza kuti, “Awachotsa Ambuye m’manda muja, ndipo sitikudziwa kumene akawaika.” Pamenepo Petro ndi wophunzira uja adatuluka napita ku manda. Onse awiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. Adawerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadalowemo. Simoni Petro atafika akumutsatira, adalowa m’mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire, ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adalowa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mpaka nthawi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, kuuka kwa Yesu Khristu kwa akufa kwadzaza mitima yathu ndi chikhulupiriro ndi chimwemwe. Tiyeni, tiyamike Atate athu a Kumwamba, popempherera anthu onse a m'dziko lino lapansi:

 

1.     Apapa, Aepiskopi ansembe onse alimbitse chikhulupiriro cha akhristu ao, pakuwalalikira mosakayika za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Akhristu onse, kukondana kwawo kupite m'tsogolo, ndipo ntchito zao zisonyeze anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu odwala ndi onse amene ali m’mavuto, chikondwerero cha Pasaka chiwalimbitse mtima, podziwa kuti Yesu Khristu adagonjetsa imfa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno, tikhaledi anthu atsopano ndi mboni zake za Yesu Khristu, poika mtima pa zinthu za kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani chifukwa mudatiwukitsa pamodzi ndi Yesu Khristu potininkha moyo wake. Mumvere mapemphero athuwa ndi kutisunga m'chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

LOWERUKA LOYERA – CHAKA A [MISA YA MADZULO/ USIKU YA KUUKA KWA AMBUYE]

 LOWERUKA LOYERA – CHAKA A

[MISA YA MADZULO/ USIKU YA KUUKA KWA AMBUYE]

 

1. MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 01: 01 - 2:2 (Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri).

 

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. Tsono Mulungu adati, “kuyere,” ndipo kudayeradi. Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima. Kuyerako adakutcha Usana, mdima uja adautcha Usiku. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku loyamba.

Kenaka Mulungu adati, “pakhale cholekanitsa madzi, kuti madziwo akhale pa malo awiri olekana,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga cholekanitsa madzi chija, nawagawa madziwo, ena pansi pa cholekanitsacho ena pamwamba pake. Cholekanitsacho adachitcha dzina loti Thambo. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachiwiri.

Mulungu adatinso, “Madzi apansiwa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi. Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adawasonkhanitsa aja adawatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Tsono adati, “panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi. Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobereka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachitatu.

Pambuyo pake Mulungu adati, “kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga miyuni iwiri yaikulu: dzuwa lowala masana, ndi mwezi wowala usiku. Adalenganso nyenyezi. Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, kuti iziwala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachinai.

Zitatero Mulungu adati, “m’nyanja mukhale zamoyo zambirimbiri, ndipo pakhale mbalame zouluka mu mlengalenga.” Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam’nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m’madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse Zimene adalengazo zinali zabwino. Adazidalitsa ponena kuti, “swanani ndipo mudzaze nyanja, mbalamenso ziswane pa dziko. Tsono kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachisanu.

Ndipo Mulungu adati, “padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoweta, zokwawa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi. Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoweta potsata mitundu yake, ndiponso zokwawa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino. Zitatha izo Mulungu adati, “tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam’nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoweta, ndi zokwawa zonse za pa dziko lapansi.” Motero Mulungu adalenga munthu, m’chifanizo chake, adawalengadi m’chifanizo cha Mulungu. Adawalenga wina wamwamuna wina wamkazi. Adawadalitsa powauza kuti, “mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.” Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya. Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwawa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

Motero dziko lonse lapansi, thambo ndi zonse zokhala m’menemo, zidatha kulengedwa. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiwiri.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 03: 04 – 07, 12 – 13, 20, 22.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Mau a Chauta ndi olungama,

Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,

Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi

 

Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa,

Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake,

Adasonkhanitsa pamodzi madzi a m’nyanja zakuya,

Ndipo adaziikira malire kuti zisasefukire.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi

 

Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta,

Anthu amene Chauta wawasankha akeake,

Chauta ali kumwamba, amayang’ana pansi,

Ndi kuwona anthu onse.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi

 

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,

Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,

Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi

--------------------------------------


2. MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 22: 01 – 18 (Nsembe ya Abrahamu, bambo wathu wachikhulupiriro).

 

Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.” Mulungu adati, “tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza. M’mawa mwake Abrahamu adakonza chishalo pa bulu wake nadulanso nkhuni zokaotchera nsembe, ndipo adatenga Isaki pamodzi ndi antchito ake awiri, nanyamuka ulendo wopita ku malo amene Mulungu adaamuuza. Pa tsiku lachitatu lake Abrahamu adaona malowo chapatali. Ndipo adauza antchito ake aja kuti, “inu bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, pambuyo pake tidzakupezani.” Abrahamu adasenzetsa Isaki nkhuni zokaotchera nsembe yopsereza ija, iyeyo adaatenga moto m’manja mwake, pamodzi ndi mpeni, onse nkumayendera limodzi. Tsono Isaki adaitana bambo wake kuti, “Atate.” Abrahamu adavomera kuti, “Ee, mwana wanga.?” Isaki adafunsa kuti, “moto ndi nkhuni ndikuziwona, zilipo, koma nanga mwana wankhosa wokaotchera nsembe ali kuti?” Abrahamu adamuyankha kuti, “mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwana wankhosa yo.” Choncho onse awiri adapitiriza ulendo wao limodzi. Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo. Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo. Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, “usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziwa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo. Abrahamu atayang’ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m'ziyangoyango. Adapita kukaigwira, naipha ngati nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake uja. Abrahamu adawatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa. Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiwiri kuchokera kumwamba, adati, “Chauta akunena kuti, ‘ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezi, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m’mbali mwa nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 06: 05, 08 – 11.

                                                

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

 

Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa,

Tsogolo langa lili m’manja mwanu,

Nthawi zonse ndimalingalira za Chauta,

Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.

 

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

 

Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,

Ndipo m’katikati mwangamu ndikusangalala,

Thupi langanso lidzakhala pabwino,

Chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,

Simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.

 

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

 

Mumandiwonetsa njira ya ku moyo.

Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,

Ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja,

Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana.

 

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

--------------------------------------

 

3. MAU A M’BUKU LA EKSODO; EKSODO 14: 15 – 15: 01. (Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziwiri)

 

Chauta adafunsa Mose kuti, “chifukwa chiyani ukulira kwa ine? Auze Aisraele kuti aziyenda. Tenga dodo yakoyo, ndipo utambalitse dzanja pa nyanja, kuigawa nyanjayo kuti Aisraele aoloke pouma. Ndidzawaumitsa mtima Aejipitowo, kotero kuti adzalondola Aisraele ndithu. Ndipo kugonjetsa kumene ndidzagonjetsa Farao pamodzi ndi ankhondo ake, magaleta ake ndi oyendetsa ake omwe, ndidzapeza nako ulemerero. Aejipitowo adzadziwa kuti Ine ndine Chauta, akadzaona m’mene ndipambanire Farao ndi magaleta ake ndi owayendetsa ake. Apo mngelo wa Mulungu, yemwe ankatsogolera Aisraele aja, adakakhala cha kumbuyo kwao. Mtambo womwe unkakhala patsogolo pao uja, udakakhalanso chakumbuyo kwao. Unali pakati pa gulu lankhondo la Aejipito ndi gulu lankhondo la Aisraele.

Choncho panali mtambo ndi mdima, kotero kuti magulu ankhondo awiriwo sadayandikane usiku wonse. Tsono Mose adatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo pompo Chauta adaumitsa nyanja ija, pogwiritsa ntchito mphepo yamkuntho yakuvuma, imene idaomba usiku wonse ndi kuumitsa nyanjayo. Madziwo adagawikana, ndipo adakhala ngati chipupa pa mbali zonse ziwiri, motero Aisraele adaoloka pouma. Aejipito aja adalondola Aisraelewo mpaka kukalowa nawo m’nyanja muja. Akavalo onse a Farao adalowa m’nyanja, pamodzi ndi magaleta ake ndi owayendetsa ake omwe. Tsono kusanache m’mawa ndithu, Chauta, ali m’chipilala chamtambo ndi chamoto, adayang’ana ankhondo a Aejipito ndipo adawachititsa mantha. Adapinda mikombero ya magaleta ao, kotero kuti magaletawo ankayenda movutika. Pamenepo Aejipito aja adati, “tiyeni tiwathawe Aisraelewa, chifukwa Chauta akuwamenyera nkhondo, kulimbana nafe.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “tambalitsa dzanja lako kunyanjako kuti madziwo abwerere, ndi kumiza Aejipitowo pamodzi ndi magaleta ao ndi owayendetsa ake omwe.!” Motero Mose adatambalitsa dzanja lake ku nyanja, ndipo m’mene kunkacha, nkuti madziwo akubwerera m’malo mwake. Aejipitowo adayesa kuthawa, koma Chauta adawabweza momwe m’nyanjamo. Ndipo madziwo adabwerera, namiza magaleta aja ndi owayendetsawo, pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Farao lija linkawatsatali. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka. Koma Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziwiri. Pa tsiku limenelo, Chauta adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito. Aisraele adaona Aejipitowo ali ngundangunda m’mbali mwa nyanja. Choncho adaona mphamvu zazikulu zimene Chauta adaonetsa pogonjetsa Aejipito aja. Tsono adayamba kuwopa Chauta, ndipo ankakhulupirira Chautayo ndi Mose mtumiki wake. Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati,

 

A Choir ayimbe nyimbo ili pansipa.

 

Nyimbo ya Mose – Eksodo 15: 01 – 06, 17 – 18.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana,

Waponya m’nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe,

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira,

Ndiye chipulumutso changa.

Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda.

Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Chauta ndi wankhondo, Chauta ndilo dzina lake,

Chauta adaponya m’nyanja magaleta a Farao,

Pamodzi ndi gulu lake lankhondo,

Adammizira Atsogoleri ake amphamvu m’Nyanja Yofiira,

Nyanja yozamayo idawaphimba onse, a

Adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero,

Chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.

Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Mudzawalowetsa ndi kuwakhazika pa phiri lanu,

Pa malo amene Inu Chauta mudawapanga kuti akhale anu,

M’nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga

Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

--------------------------------------

 

4. MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 54: 05 – 14 (Ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya, akuterotu Chauta, Momboli wako).


Mlengi wako ali ngati mwamuna wako. Chauta Wamphamvuzonse ndiye dzina lake. Woyera Uja wa Israele ndiye Momboli wako, dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi. Iwe Israele, Chauta wakuitananso. Uli ngati msungwana wosiyidwa, amene ali wodzaza ndi chisoni mu mtima, ngati mkazi wapaunyamata amene wachotsedwa, akuterotu Mulungu wako. “Ndidaakusiya pa kamphindi kochepa, koma ndidzakutenganso ndi chikondi chachikulu. Ndidaakufulatira pa mphindi yaing’ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako. “Kwa ine zimenezi zili monga m’mene zinaliri nthawi ya Nowa: monga momwe ndidaalumbirira nthawi imeneyo kuti sindidzaononganso dziko lapansi ndi chigumula, chonchonso tsopano ndikulumbiranso kuti sindidzakupseranso mtima, ndipo sindidzakudzudzulanso. Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo. Chauta akunena kuti, “Iwe Yerusalemu ndiwe mzinda wozunzika, wosowa chithandizo, wopanda wokutonthoza. Ndidzakongoletsa miyala yako, ndidzamanganso maziko ako ndi miyala ya mtengo wapatali. Ndidzamanga nsanja zako ndi miyala yofira. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yochezimira ngati moto. Ndidzamanganso linga lokuzungulira ndi miyala ya mtengo wapatali. Anthu ako ndidzawaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzawadalitsa ndi kuwapatsa mtendere waukulu. Udzakhazikika m’chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 30: 01, 03 – 05, 10 – 12.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta,

Pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa,

Simudalole kuti adani anga akondwere,

Inu Chauta, mwanditulutsa m’dziko la akufa,

Mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

 

Imbani nyimbo zotamanda Chauta,

Inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera,

Mkwiyo wake ndi wa kanthawi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse,

Misozi kumabwera chimwemwe chokhachokha.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

 

Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima,

Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga,

Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina,

Chauta, Mulungu wanga ndidzakuthokozani mpaka muyaya.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

--------------------------------------

 

5. MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 55: 01 – 11 (Mubwere kwa Ine, mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha).

 

Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse. Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona. Tcherani makutu, ndipo mubwere kwa Ine. Mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha, ndipo ndidzakuwonetsani chikondi chosasinthika ndi chosapeneka, chimene ndidaalonjeza Davide. “Mudziwe kuti iye uja ndidamsankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira anthu ambiri. Tsopano mudzaitana mitundu imene simuidziwa. Mitundu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kuti ikhale nanu, chifukwa cha Ine Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, amene ndidakupatsani ulemerero. Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo awachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye awakhululukire machimo ao mofewa mtima. Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu. Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m’kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidawatumira zidzayenda bwino.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 12: 02 – 06.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Zoonadi Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye,

Ndipo sindidzaopa pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa,

Ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga,

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Thokozani Chauta, tamandani dzina lake,

Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,

Mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu,

Zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi,

Fuulani ndi kuimba mokondwa, inu anthu a ku Ziyoni,

Pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

--------------------------------------

 

6. MAU A M’BUKU LA MPROFETI BARUKI; BARUKI 03: 09 – 15, 32 – 04: 04 (Yenda molondola m’kuwala kwa kuyera kwa Ambuye).

 

Iwe Israele, imva malamulo opatsa moyo. Tchera khutu kuti udziwe nzeru. Zakhala bwanji, iwe Israele, zakhala bwanji kuti ukupezeka m’dziko la adani, ndipo kuti wayamba kukalamba m’dziko lachilendo? Zakhala bwanji kuti uli woipitsidwa pakati pa anthu akufa? Chifukwa chiyani wasanduka mnzao wa anthu akumanda? Iwetu udasiya kasupe wa nzeru. Ukadatsata njira ya Mulungu, bwenzi uli mu mtendere nthawi zonse. Phunzira kumene kuli luntha, kumene kuli mphamvu, kumene kuli nzeru zomvetsa zinthu. Pamenepo udzazindikira kumene kuli moyo weniweni wa zaka zambiri, kumene kuli kuyera kokuunikira, ndiponso kumene kuli mtendere. Ndani adapeza malo ake kumene kumakhala nzeru? Ndani adalowa m’nyumba yosungiramo chuma chake? Koma Iye amene amadziwa zonse, amadziwadi nzeru. Adazipeza chifukwa cha kumvetsa bwino zinthu. Ndiye amene adakonza dziko lapansi kuti likhalepo mpaka muyaya, nalidzaza ndi nyama zamitundumitundu. Amatuma kuwala, ndipo kumapitadi. Amakuitana kuwalako, ndipo kumamvera mau ake monjenjemera. Nyenyezi zimawala pamalo pamene adziikapo ndipo zimasangalala. Iye akaziitana, izo zimayankha kuti, “Tili pano” Ndipo zimawala mosangalala, kuwalira amene adazilenga. Ameneyu ndiye Mulungu wathu, palibe wina wofanafana naye. Iye adatulukira njira zonse zofikira ku nzeru, nzeruzo adazipatsa Yakobe mtumiki wake, adazipatsa Israele wokondedwa wake. Pambuyo pake nzeruzo zidadzaoneka pansi pano nkudzakhazikika pakati pa anthu. Nzeru ndiye Buku la Malamulo a Mulungu. Malamulo ake odzakhala mpaka muyaya. Onse ozigwiritsa nzeruzo, amakhala ndi moyo, koma olekana nazo amafa. Bwerera Yakobe, udzalandire nzeru, yenda molondola kuwala kwa kuyera kwake. Ulemerero wako usapatse munthu wina, madalitso ako usawapereke kwa anthu achilendo. Inu Aisraele, ifetu ndife odala, chifukwa timadziwa zokomera Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19: 08 – 11.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

 

Malangizo a Chauta ndi olungama,

Amasangalatsa mtima,

Malamulo a Chauta ndi olungama,

Amapatsa mtima womvetsa.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

 

Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,

Chimakhala mpaka muyaya.

Chiweruzo cha Chauta nchoona,

Ncholungama nthawi zonse.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

 

Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide,

Ngakhale golide wambiri wamtengowapatali,

Nzotsekemera kupambana uchi,

Ngakhale uchi wozuna kwambiri.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

--------------------------------------

 

7. MAU A M’BUKU LA MPROFETI EZEKIELE; EZEKIELE 36:16 – 28 (Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano).

 

Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti: “Munthu iwe, pamene Aisraele ankakhala m’dziko lao, adaliipitsa ndi makhalidwe oipa ndiponso ndi zochita zao. Ndidaona kuti makhalidwe ao anali onyansa pa za chipembedzo, ngati mkazi amene ali kunthawi yake. Ndidawalanga mokalipa chifukwa cha magazi a anthu amene iwo adakhetsa m’dzikomo, ndiponso chifukwa cha mafano amene iwo adaipitsa nawo dzikolo. Ndidawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo ndidawabalalitsira ku maiko osiyanasiyana. Ndidawalanga potsata makhalidwe ao ndi ntchito zao. Atafika pakati pa anthu a mitundu inayo, kulikonse kumene ankapita, adaipitsa dzina langa loyera. Zidatero chifukwa anthu ponena za iwowo ankati, ‘Awa ndi anthu a Chauta, koma onani adachotsedwa ku dziko lake.’ Komabe Ineyo ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraele adaliipitsa pamene ankakhala pakati pa anthu a mitundu ina kumene adapita. Nchifukwa chake Aisraelewo uwauze kuti Ine Ambuye Chauta mau anga ndi awa: ‘Zimene nditi ndichite, sindichita chifukwa cha inuyo Aisraelenu ai, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mudalipiitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene mudapita. Dzina langa lotchuka limene lakhala lonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaonetsa kuti nloyera. Tsono anthu a mitundu inayo atazindikira kuti ndaonetsa kuyera kwa dzina langa mwa inu, adzadziwa kuti Ine ndine Chauta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Ndidzakutulutsani pakati pa mitundu inayo, ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku dziko lililonse, ndipo ndidzakubwezani ku dziko lanu. Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo mudzayera, zonse zokuipitsani zidzachoka. Ndiponso ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri. Mudzakhala m’dziko limene ndidapatsa makolo anu. Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

A. Ngati palibe anthu oti abatizidwe

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 42: 02, 04; 43: 03, 04.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m’mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu,

Mulungu wamoyo,

Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Mtima wanga umawawa ndikamakumbukira m’mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu,

Powatsogolera ku Nyumba ya Mulungu.

Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala,

Akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Tumizani kuwala kwanu ndi choona chanu kuti zinditsogolere.

Zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kokhala Inu.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,

Kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana,

Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

--------------------------------------

 

B. Ngati pali anthu oti abatizidwe.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51:10 – 13, 16, 17.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,

Muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika,

Musandipirikitse pamaso panu,

Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

 

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,

Mulimbitse mwa ine mtima womvera,

Pamenepo ochimwa ndidzawaphunzitsa njira zanu,

Ndipo iwo adzabwerera kwa Inu.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

 

Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani,

Ndikapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo.

Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika.

Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

--------------------------------------

 

8. MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 06: 03 – 11 (Tikudziwa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso).

 

Abale, kodi inu simukudziwa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake? Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m’manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano. Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo. Tidziwa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo. Pakuti munthu akafa, ndiye kuti wamasuka ku mphamvu ya uchimo. Tsono ngati tidafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. Tikudziwa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu. Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 118: 01 – 02, 16 – 17, 22 – 23.

 

Alleluia – (Wansembe aimba katatu, ndipo anthu abwereza)

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya. Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.”

 

Alleluia – Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu. Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

 

Alleluia – Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu. – Alleluia, Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 28: 01 – 10 (Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya).

 

Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Maonekedwe ake anali ngati a mphezi, ndipo chovala chake chinali choyera chambee. Pamenepo alonda aja adachita mantha nayamba kunjenjemera, nkungoti gwa ngati anthu akufa. Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja nawauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu. Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona. Pitani msanga tsono, kauzeni ophunzira ake aja kuti, “Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya, mukamuwonera kumeneko.” Kumbukirani zimene ndakuuzanizi. Apo azimaiwo adachoka kumandako msanga, ali ndi mantha komanso ndi chimwemwe chachikulu, nathamanga kukauza ophunzira ake aja. Mwadzidzidzi Yesu adakumana nawo nati, “Monitu azimai!” Iwo adadza pafupi, nkugwira mapazi ake, nampembedza. Apo Yesu adawauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, podziwa kuti Yesu Khristu wouka kwa akufa alikukhaladi pakati pathu, tiyeni, pamodzi naye, tiwapempherere anthu onse:

 

1.     Eklezia alimbitse chikhulupiriro m' mitima ya anthu a mafuko onse, pakuwalalikira za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Akhristu amene akuzunzika chifukwa cha Mthenga Wabwino alimbike m’chikhulupiriro pozindikira kuti Yesu Khristu ali no pafupi.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Akatekumeni amene alandira Ubatizo leroli nawonso amuchitire Yesu Khristu umboni pamaso pa anthu anzao pakuwaonetsa makhalidwe a chikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno tizidzetsa chimwemwe cha Pasaka m’mitima ya anzathu pakuwatumikira mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athu amenewa, tilikuyamika kukoma mtima kwanu, chifukwa simulephera kukwaniritsa malonjezo anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...