LAMULUNGU LA PASAKA – CHAKA A.
“Yesu Khristu ndiye Moyo Wathu.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 10: 34a, 37 – 43 (Adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa).
Petro adayamba kuyankhula, adati, “zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Mukudziwa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthawi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziwa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzodza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi satana. Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m’dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera. Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 01 – 02, 16 – 17, 22 – 23.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Kapena Alleluia, Alleluia, Alleluia!
Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,
Ndipo chikondi chake nchamuyaya,
Aisraele anene kuti, ‘Chikondi chake nchamuyuaya.’
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
Dzanja lamanja la Chauta lapambana,
Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,
Womwewo wasanduka mwala wapangodya,
Chauta ndiye amene wachita zimenezi,
Zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
--------------------------------------
[CHITSANKHO CHOYAMBA]
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 03: 01 – 04 (Muzifunafuna za Kumwamba, kumene kuli Ambuye).
Abale, ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
[CHITSANKHO CHACHIWIRI]
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: AKORINTO 05: 06b – 08.
Kodi simuwadziwa mau aja akuti, “chofufumitsa buledi chapang’ono chimafufumitsa mkate wonse?” Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale ndi oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Pasaka, adaphedwa kale ngati nsembe. Tiyeni tsono, tichite chikondwererocho, osati ndi chofufumitsira chakale chija cha uchimo ndi cha kuipa mtima, koma ndi buledi wosafufumitsa, wakuyera mtima ndi wa choona.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 01 AKORINTO 05: 07.
Alleluia, Alleluia – Kankhosa kathu ka Pasaka ndiye Yesu Khristu amene waphedwa ngati nsembe. Tiyeni tsono, tichite chikondwerero choyamikira Ambuye. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 20: 01 – 09 ('Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.').
Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m’mamawa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adawauza kuti, “Awachotsa Ambuye m’manda muja, ndipo sitikudziwa kumene akawaika.” Pamenepo Petro ndi wophunzira uja adatuluka napita ku manda. Onse awiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. Adawerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadalowemo. Simoni Petro atafika akumutsatira, adalowa m’mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire, ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adalowa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mpaka nthawi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, kuuka kwa Yesu Khristu kwa akufa kwadzaza mitima yathu ndi chikhulupiriro ndi chimwemwe. Tiyeni, tiyamike Atate athu a Kumwamba, popempherera anthu onse a m'dziko lino lapansi:
1. Apapa, Aepiskopi ansembe onse alimbitse chikhulupiriro cha akhristu ao, pakuwalalikira mosakayika za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu onse, kukondana kwawo kupite m'tsogolo, ndipo ntchito zao zisonyeze anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala ndi onse amene ali m’mavuto, chikondwerero cha Pasaka chiwalimbitse mtima, podziwa kuti Yesu Khristu adagonjetsa imfa.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tili muno, tikhaledi anthu atsopano ndi mboni zake za Yesu Khristu, poika mtima pa zinthu za kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukuyamikani chifukwa mudatiwukitsa pamodzi ndi Yesu Khristu potininkha moyo wake. Mumvere mapemphero athuwa ndi kutisunga m'chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment