Saturday, April 15, 2023

LAMULUNGU LA 02 LA PASAKA – CHAKA A. [LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA AMBUYE – DIVINE MERCY SUNDAY]

LAMULUNGU LA 02 LA PASAKA – CHAKA A.

[LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA AMBUYE – DIVINE MERCY SUNDAY]    

“Mtendere wa Ambuye ukhale nanu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI; NTCHITO 02: 42 – 47 (Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagawana zinthu zao).

 

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagawana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagawira onse, malinga ndi kusowa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m’Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankawakonda mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawawonjezera ena olandira chipulumutso.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 02 – 04, 13 – 15, 22 – 24.

                                                

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Aisraele anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya,

Banja la Aroni linene kuti, Chikondi chake nchamuyaya,

Anthu oopa Chauta anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.

 

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa,

Koma Chauta adandithandiza,

Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga,

Ndiye Mpulumutsi wanga.

 

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

Womwewo wasanduka mwala wapangodya,

Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu,

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga,

Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

 

Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 01 PETRO 01: 03 – 09 (lye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso

pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa).

 

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati cholowa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthawi yotsiriza. Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zowawa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthawi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 20: 29.

 

Alleluia, Alleluia – Yesu adati, wakhulupirira chifukwa wandiona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 20: 19 – 31 (Patapita masiku asanu ndi atatu, Yesu adabwera).

 

Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira mpweya nati, “landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.” Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi awiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “ife tawaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “ndikapanda kuwona mabala a misomali m’manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m’nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.” Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m’nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m’nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m’buku muno. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m’dzina lake.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Ife tonse amene tikhulupirira Yesu ngakhale sitimuwona, tiyeni tiyamike Atate athu a Kumwamba ndi kupempha madalitso ao:

 

1.     Akhristu onse akonde ndi kumagwirizana monga akhristu oyamba aja, pozindikira kuti Yesu Khristu ali nawo nthawi zonse.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Anthu onse alandire mtendere wa Yesu Khristu m’mitima mwao, ndiponso m’banja mwao ndi pakati pa maiko onse.

Tikupemphani, mutivomereze.­

3.     Anthu odwala ndi onse amene avutika m’mitima mwao, akondwere pokhulupirira Yesu Khristu pa nthawi ino ya Pasaka.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse a m’Parishi yathu ino, tilimbikire kuchita zabwino ndi kumathandizana mwaubale, kusonyeza kuti Yesu Khristu ali moyodi akutitsogolera.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, poyamika Kuuka kwa Mwana wanu kwa akufa, tikutula mapemphero athuwa m’manja mwanu, pamodzi ndi mafuno a anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

 

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...