LAMULUNGU LA 29 PACHAKA (CYCLE C)
“Mulungu adzatithandiza tikamapempha ndi mtima woona.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKISODO; EKISODO 17: 08 – 13. (Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo.)
Tsono kudabwera Aamaleke ku Redifidimu kudzamenyana ndi Aisraele. Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, mawa mupite kukamenya nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.” Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthawi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri. Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana. Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Awiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwira manja a Mose aja. Adawagwirira ndithu mpaka dzuwa kulowa. Ndipo Yoswa adagonjetseratu kwathunthu Aamalekewo.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 121: 01 – 08.
Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Ndimakweza maso anga ku mapiri,
Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta,
Amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Sadzalola phazi lako literereke,
Iye amene amakusunga sadzaodzera,
Zoonadi, amene amasunga Israele,
Ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chauta ndiye amene amakusunga,
Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja,
Dzuwa silidzakupweteka masana,
Mwezi sudzakuvuta usiku.
Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse,
Adzasamala moyo wako,
Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita,
Kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Chithandizo chathu nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO; 02 TIMOTEO 03: 14 – 04: 02. (Munthu amene ndi wa Mulungu amakhala wokonzeka kugwira ntchito ina iliyonse.)
Wokondeka Timoteo, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziwa kuti nzoona, paja ukuwadziwa amene adakuphunzitsa. Ukudziwanso kuti kuyambira ukali mwana wawazolowera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupilira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adawalembetsa mochita ngati kuwauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita Ntchito yabwino iliyonse. Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndiufumu wake wa Khristuyo. Ndikukulamula ndithu kuti uzilalikira mau a Mulungu. Uziwalalika molimbikira, pa nthawi imene anthu akuwafuna. Uziwalozera zolakwa zao, uziwadzudzula, uziwalimbitsa mtima, osalephera kuwaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – Aheberi 04: 12.
Alleluia, Alleluia – Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwao. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 18: 01 – 08. (Nanga Mulungu, angaleke kuwaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku?)
Yesu adawaphera Fanizo pofuna kuwaphunzitsa kuti azipemphera nthawi zonse, osataya mtima. Adati, “m’mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. M’mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzapempha kuti, ‘mundiweruzireko mlandu wanga umene uli pakati ine ndi mdani wanga.’ Kwa nthawi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘ngakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu, komabe chifukwa cha mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’” Tsono Ambuye adati, “mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja. Nanga Mulungu, angaleke kuwaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangowalekerera? Iyayi, kunena zoona adzawaweruzira mlandu wao mnsanga. Komabe mwana wa munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment