Saturday, October 22, 2022


 

 LAMULUNGU LA 30 PACHAKA (CYCLE C)

“Mundichitire chifundo wochimwane!”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA SIRAKI (MPHUNZITSI); SIRAKI 35: 12 – 14, 16 – 19. (Pemphero la munthu wodzichepetsa limabzola mitambo.)

 

Usayese kupereka chiphuphu kwa Ambuye, chifukwa sadzachilandira. Ndipo usadalire nsembe yopanda chilungamo, chifukwa Ambuye ndiwo muweruzi, muweruzi wake wopanda tsankho. Saonetsa kukondera poweruza wosauka, amamvera pemphero la amene anzake adamulakwira. Sanyozera pempho la mwana wamasiye kapena madandaulo a mkazi wamasiye. Uzitumikira Ambuye mokhulupirika, ndipo iwowo adzakulandira. Pamenepo mapemphero ako akafika kumwamba. Pemphero la munthu wodzichepetsa limabzola mitambo, ndipo mtima wake sudzakhazikika mpaka Ambuye atamva pempherolo. Sadzaleka kupempha mpaka wopambanazonse atamuyendera, ndi kuchitira chilungamo anthu abwino pakuweruza moona. Ambuye sadzachedwa ndipo sadzapirira anthu ochimwa, mpaka atadzaphwanya misana ya anthu opanda chisoni, ndi kulipsira mitundu ya akunja; mpaka ataonongeratu anthu achipongwe ndi kuthyola mphamvu za anthu osalungama; mpaka aliyense atampatsa molingana ndi zochita zake, ndi kulipira ntchito zakezo potsata zolinga za mumtima mwake; mpaka atagamula mlandu wa anthu ake, ndi kuwasangalatsa ndi chifundo chao. Panthawi ya mavuto chifundo cha Ambuye nchokondweretsa, ngati mitambo yamvula panthawi ya chilala.

 

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34: 02 – 03, 17 – 19, 23.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

 

Ndidzayamika Chauta nthawi zonse,

Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza,

Moyo wanga umanyadira Chauta,

Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

 

Koma Chauta amawakwiyira anthu ochita zoipa,

Anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano,

Pamene anthu ake akulira kuti awathandize,

Chauta amamva nawapulumutsa m’mavuto ao onse.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

 

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka,

Amapulumutsa otaya mtima,

Chauta amaombola moyo wa atumiki ake,

Palibe wothawira kwa Iye amene adzalangidwe.

 

Munthu wosauka adalira, ndipo Chauta adamumva.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO; 02 TIMOTEO 04: 06 – 08, 16 – 18. (Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira.)

 

Paja ine ndiye moyo wanga Wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m’moyo uno. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro, ndasunga chikhulupiliro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungura. Ambuye amene ali woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphotoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso. Pamene ndinkadziteteza pa mlandu wanga poyamba paja, panalibe ndi mmodzi yemwe amene adabwera kudzandithandizira, onse adangondisiya ndekha. Mulungu awakhululukire. Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a uthenga wabwino, kuti anthu amitundu yonse awamve. Motero ndidapulumuka m’kamwa mwa mkango. Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundilowetsa mu ufumu wake kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.

 

Mawu a Ambuye……...Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – 2 Akorinto 05: 19.

 

Alleluia, Alleluia – Mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiwalalike. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 18: 09 – 14. (Wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai.)

 

Yesu adawapheranso fanizo anthu ena amene ankadziyesa olungama nkumanyoza anzawo. Adati, “Anthu awiri adapita ku nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho. Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai. Ine ndimasala zakudya kawiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’ Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang’ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’” Yesu popitiriza mau adati, “kunena zoona, wokhometsa mnsokhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...