Saturday, October 8, 2022

 


LAMULUNGU LA 28 PACHAKA (CYCLE C)

“Tithokoze Ambuye, Mulungu wathu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU; 02 MAFUMU 05: 14 – 17. (Naamani adabwerera kwa Elisa ndipo anamvera Mulungu wa ku Israele.)

 

Motero Naamaniyo adapita ku Yordani, nakakhuvula m’madzimo kasanunkawiri, malinga ndi m’mene adaamuuzira munthu wa Mulungu uja. Pompo adachira ndipo thupi lake lidangoti see ngati la kamwana, choncho adakhala woyeretsedwa. Pambuyo pake Naamani pamodzi ndi onse omperekeza, adabwerera kwa mneneri wa Mulungu uja. Adadzaima pamaso pa Elisa namuuza kuti, “ndithu, ine ndadziwa tsopano kuti padziko lonse lapansi kulibe Mulungu wina, koma wa ku Israele yekha. Tsono landirani mphatsoyi kwa ine mtumiki wanu.” Koma Elisa adati, “pali Chauta, Mulungu wamoyo, amene ndimamtumikira, ine sindilandira zimenezi.” Naamani adamkakamiza kuti atenge, koma iye adakana ndithu. Tsono Naamani adati, “ngati mukukana, ine ndikukupemphani kuti mundilole ine mtumiki wanu nditengeko dothi lokwanira kunyamula abulu awiri. Pakuti kuyambira tsopano ine sindidzaperekanso nsembe zopsereza, kapena nsembe ina iliyonse, kwa mulungu wina aliyense, koma kwa Chauta basi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 01 – 04.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

Popeza kuti wachita zodabwitsa,

Dzanja lake lamanja ndi mkono,

Wake woyera zampambanitsa.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

 

Chauta waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse,

Kuti Iye ndi wolungama,

Wakumbukira chikondi chake chosasinthika,

Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,

Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,

Fuulirani Chauta ndi Chimwemwe, inu dziko lonse lapansi,

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

 

Chauta waonetsa chipulumutso chake kwa mitundu yonse.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO; 02 TIMOTEO 02: 08 – 13. (Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye.)

 

Kumbukira Yesu Khristu amene adauka kwa akufa, ndiponso anali m’modzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika. Chifukwa cha uthenga wabwinowu ndimamva zowawa, mpakanso kumangidwa m’ndende, ngati chigawenga. Koma mau a Mulungu sangathe kumangidwa. Motero tsono ndimapirira zonsezi chifukwa cha anthu amene Mulungu adawasankha, kuti iwonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu, ndi kulandira ulemerero wamuyaya. Awa ndi mau otsimikiza ndithu: ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye. Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, iyenso adzatikana. Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupilika, pakuti sangathe kudzitsutsa.

 

Mau a Ambuye……………Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – 01 Atesalonika 05:18.

Alleluia, Alleluia – Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 17: 11 – 19. (Sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu.)

 

Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu adadzera m’malire a Samariya ndi Galileya. Pamene ankalowa m’mudzi wina, anthu khumi akhate adadzamchingamira. Adaima kutali, nanena mokweza mau kuti, “Yesu Ambuye, tichitireni chifundo.” Pamene Yesu adawaona, adawauza kuti, “pitani, kadziwonetseni kwa ansembe,” Pamene iwo ankapita, adachira. Tsono m’modzi mwa iwo, ataona kuti wachira, adabwerera nayamba kuyamika Mulungu mokweza mau. Adagwada nkuwerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo adali Msamariya. Apo Yesu adati, “kodi achira aja si khumi? Nanga asanu ndi anai ena aja ali kuti? Ndiye kuti sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu?” Kenaka Yesu adauza munthuyo kuti, “nyamuka, pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...