“Ambuye, mutiwonjezere chikhulupiliro.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI HABAKUKU; HABAKUKU 01: 02 – 03; 02: 02 – 04. (Ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.)
Kodi inu Chauta, ndidzakhala ndikukupemphani chithandizo nthawi yaitali bwanji, inuyo osandiyankha? Kapena kukudandaulirani kuti “Nkhondo kuno,” Inuyo osatipulumutsa? Chifukwa chiyani mukufuna kuti ndiziwona mavuto oterewa. Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa? Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo. Pali ndeu ndi kukangana kwambiri. Chauta adandiyankha kuti, “lemba uthengawu, ulembe mooneka bwino pa mapale, kuti wowerenga awerenge mosavuta. Uthengawu ukudikira nthawi yake. Nthawi yakeyo idzabwera mofulumira, sizidzalephera kuchitika. Ngati ziwoneka kuti zikuchedwa, mudikire. Zidzafika ndithu, si kuchedwa ai. Ochita zoipa adzalephera, koma ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95: 01 – 02, 06 – 09.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Bwerani, timuimbire Chauta,
Tiyeni tifuule ndi Chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa,
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,
Timuimbire nyimbo zotamanda.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira,
Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake,
Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Lero mukadamverako mau ake!
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,
Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,
Pamene makolo anu anandiputa mondiyesa,
Ngakhale anali ataona ntchito zanga.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO; 02 TIMOTEO 01: 06 – 08, 13 – 14. (Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu.)
Wokondeka, nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto. Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira. Usachite manyazi tsono kuchita umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m’ndende chifukwa cha Iye, koma umve nao zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu ya Mulungu. Uwagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti udzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu. Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.
Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – 01 Petro 01: 25.
Alleluia, Alleluia – Mau a Mulungu ngokhala mpaka muyaya. Mau amenewa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 17: 05 – 10. (Mutiwonjezere chikhulupiriro.)
Atumwi adapempha Ambuye kuti, “mutiwonjezere chikhulupiriro.” Koma Yesu adati, “mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambewu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘zuka, kadzibzale m’nyanja.’ Ndipo ukadakumveranidi ndithu.” Yesu adatinso, “utha kukhala ndi wantchito wolima ku munda kapena woweta nkhosa. Pamene iye wafika kuchokera ku munda, kodi ungamuuze kuti, ‘bwera mnsanga, udzadye?’ Sungatero ayi, koma udzamuuza kuti, ‘konzere chakudya. Ukonzeke kunditumikira mpaka ineyo ndidye ndi kumwa. Iweyo udya ndikumwa ndi kudya pambuyo pake. Kodi ungamuthokoze wantchitoyo chifukwa chakuti wachita zimene unamlamula? Choncho inunso, mutachita zonse zimene adakulamulani, muziti, ‘Ndife antchito osayenera kulandira kanthu. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment