LAMULUNGU
LA 24 PA CHAKA (CYCLE C)
“Ndinyamuka ndi kubwerera kwa bambo wanga”
MAU WOYAMBA A
M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKISODO; EKISODO 32: 07 – 11, 13 – 14. (Choncho
Chauta adaleka chilango choposa chimene adaati agwetsere anthu akewo.)
Chauta adauza Mose kuti, “fulumira, tsika phiri, chifukwa anthu ako amene udawatsogolera powatulutsa ku Ejipito aja, adziipitsa kwambiri. Asiya mwansanga zonse zija zimene ndidawalamula kuti azichita. Adzipangira fano la mwanawang’ombe wa golide wosungunula, ndipo alipembedza ndikuliphera nsembe, namanena kuti, ‘inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku aejipito.”’ Ndipo Chauta adaonjeza kuti, “anthu amenewa ndikuwadziwa, ngokanika kwambiri. Nchifukwa chake tsono, undileke kuti ndiwaononge chifukwa ndili wokwiya kwambiri, koma iweyo ndidzakusandutsa mtundu waukulu wa anthu.” Koma Mose adapepesa Chauta wake, nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukukwiyira anthu anu chotero, anthu amene mudawatulutsa mu ukapolo ku Ejipito kuja ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu? Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudawalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudawauza kuti, ‘ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.”’ Choncho Chauta adaleka chilango choopsa chimene adaati agwetsere anthu akewo.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51: 03 – 04, 12 – 19.
Ndinyamuka, ndipita kwa bambo
wanga.
Mundichitire chifundo, Inu
Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika.
Mufafanize machimo anga, malinga
ndi chifundo chanu chachikulu,
Mundisambitse kwathunthu pochotsa
kulakwa kwanga,
Mundiyeretse mtima pochotsa
machimo anga.
Ndinyamuka, ndipita kwa bambo
wanga.
Mundilengere mtima woyera, Inu
Mulungu,
Muike mwa ine mtima watsopano ndi
wokhazikika.
Musandipirikitse pamaso panu,
Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.
Ndinyamuka, ndipita kwa bambo
wanga.
Ambuye, tsekulani milomo yanga,
ndipo pakamwa panga padzalankhula
zotamanda Inu.
Nsembe imene Inu Mulungu
mumailandira ndi mtima wotswanyika,
Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu
Mulungu simudzanyoza.
Ndinyamuka, ndipita kwa bambo
wanga.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEO: 01 TIMOTEO 01: 12 – 17. (Yesu Khristu adabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa.)
Abale, ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene adandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Ndikumthokoza pondiwona wokhulupirika nandipatsa ntchito yomtumikira, ngakhale kuti kale ndinkamuchita chipongwe, kumzunza ndi kumnyoza. Koma Mulungu adandichitira chifundo chifukwa ndinkadzichita mosadziwa, poti ndinali wopanda chikhulupiliro. Ambuye athu adandikomera mtima koposa, nkundipatsa chikhulupiliro ndi chikondi zimene tili nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu. Awa ndi mau otsimikizika, oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa. Koma Mulungu adandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwa koposane, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse. Adafuna kuti ndikhale chitsanzo cha kuwalezera mtima onse amene adzamkhulupilire kuti alandire moyo wosatha. Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Mawu a Ambuye……………Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – 2 Akorinto 05: 19.
Alleluia, Alleluia – Mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiwalalike. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 15: 01 – 10. (Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.)
Pa nthawi yomweyo, anthu onse okhometsa msonkho ndi Ayuda enanso onyozera Malamulo ankabwera kwa Yesu kudzamva mau ake. Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuwinya nkumanena kuti, “munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.” Tsono Yesu adawaphera fanizo ili, adati, “ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, nawauza kuti, mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.” Yesu adapitiriza mau kuti, “ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima. Mwinanso mai amakhala ndi tindalama khumi, kamodzi nkutayika. Kodi suja amayatsa nyale nasesasesa m’nyumba nkufunafuna mosamala mpaka atakapeza? Atakapeza amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, nawauza kuti, ‘mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndakapeza kandalama kanga kaja kadaatayikaka.”’ Yesu popitiriza mau adati, “ndikunenetsa kuti ndi m’menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment